NJIRA YOKHAYO YOCHOKERA

Yolembedwa ndi Tony Alamo

Mbewu imene MULUNGU anauza Abrahamu kuti idzadalitsa mafuko onse inali mbewu imene inali ndi moyo wosatha mwa iyo (Genesis 12:3). Mbewu zonse zili ndi moyo wochepa mwa izo, koma mbewu imodzi yokha ili ndi moyo wosatha mwa iyo, ndipo “mbewu imeneyi ndi MAWU a MULUNGU,” amene ali YESU (Luka 8:11).1 YESU ndi mbewu yokhayo komanso ndi odzala wa mbewuyo, MAWU a MULUNGU (Luka 8:5-15). Ife amene tili kachisi wa MULUNGU ndi thupi la KHRISTU, mkwatibwi WAKE, tili ndi YESU ndi ATATE mwa MZIMU amene akhala mwa ife, kotero ife mwa MZIMU takhala ofesa mbewu za moyo wosatha, zimene zilinso KHRISTU, MAWU (Yohane 4:36).2

Komanso, ndife oitanidwa-a-dziko-lapansi, tchalitchi.3 Komanso, mbewu, YESU, ndi MAWU a MULUNGU. Ife, olungama, oitanidwa-a-dziko-lapansi, tchalitchi—zonsezi ndi moyo, moyo wosatha, umene uli mbewu yosafa ndi, komanso, ndiyo MAWU a MULUNGU, amene ali MULUNGU amene anakhala munthu ndikukhala nafe pansi pano, EMANUELI, kutanthauza kuti MULUNGU nafe (Mateyu 1:23).

Ena opusa amati, “Chabwino, ndikudziwa sindimawerenga Baibulo monga ndikuyenera kuchitira,” poganiza kuti mawu opusa amanenawa ndi njira yodzichepetsera ndi kudzitsitsa, kuulula mwachilungamo, ndipo kuti adzapulumuka pakunena zinthu zogwetsa ulesizi. Komabe, akungodzipweteka okha kosalekeza. Chomwecho “chikhulupiliro chidza ndi mbiri, ndipo mbiri idza mwa MAWU a MULUNGU,” amenenso ali mbewu, chinthu chokhacho chimene chili ndi moyo wosatha mwa icho (Aroma 10:17). MAWU ndiye MULUNGU (Yohane 1:1). MULUNGU ndi wamuyaya, kotero ngati MULUNGU ali mwa inu mwa ubwino wa MAWU, simudzafa, ngati mungakhanzikike mpaka ku chimaliziro.4

China chili chonse tikuchiona padziko lapansi chinaukitsidwa ndi MAWU a MULUNGU kuchoka ku dziko lapansi, kuti tithe kuona bwinobwino, makamaka kwa ife amene timamudziwa MULUNGU kapena takhala tikumudziwa IYE.

“Pakuti mkwiyo wa MULUNGU waonekera kuchokera Kumwamba kutsutsana ndi zonse zopanda umulungu ndi chilungamo za anthu, amene akakamiza pansi choonadi m’chosalungama chawo; Chifukwa chodziwika cha MULUNGU chaonekera mkati mwawo; pakuti MULUNGU anachionetsera kwa iwo. Pakuti zinthu zosaoneka za IYE kuyambira nthawi imene analenga dziko lapansi zikuoneka bwinobwino, kuzindikiridwa ndi zinthu zimene zinalengedwa, ngakhale mphamvu YAKE yosatha ndi UMULUNGU wake; kuti iwo akhale opanda mawu akuwilingura: Chifukwa kuti, akamudziwa MULUNGU [osiya chi Khristu], anamulambira IYE osati ngati MULUNGU, ndipo sanamuyamike; koma anakhala opanda pake m’maganizo awo, ndipo mtima wao wopulukira unada. Pakunena kuti ali a nzeru, anapusa, nasandutsa ulemelero wa MULUNGU wopanda chinyengo kukhala fanizo la munthu wachinyengo, ndi kwa mbalame, komanso nyama za miyendo inayi, ndi zinthu zokwawa.

“Chifukwa chake MULUNGU anawapereka iwo ku zonyansa kudzera m’zilakolako zamitima yawo ya chiwerewere, kunyazitsa matupi awo pakati pawo: Amenewo anasandutsa choonadi cha MULUNGU kukhala chabodza, napembedza ndikutumukira cholengedwa kuposa Mlengi, amene ali wolemekezeka ku nthawi yosatha. Amen. Chifukwa cha ichi MULUNGU anawapereka iwo ku zilakolako za manyazi: pakuti angakhale akazi awo anasandutsa machitidwe awo a chibadwidwe kukhala machitidwe osalingana ndi chibadwidwe: Chimodzimodzinso amuna, anasiya machitidwe a chibadwidwe cha akazi, natenthetsana ndi chilakolako chawo wina ndi mzake; amuna okhaokha anachitirana chamanyazi, ndipo analandira mwa iwo okha mphoto yakuyenera kulakwa kwawo [chiyenerezo].

“Ndipo monga iwo anakana MULUNGU mwakudziwa kwawo, MULUNGU anawapereka ku mtima wokanika, kukachita zinthu zosayenelera; Anadzadza ndi zosalungama zonse, chisembwere, kuipa, kusilira, dumbo; odzala ndi kaduka, mbanda, mtsutso, chinyengo, udani; akazitape, osinjilira, adani a MULUNGU, achipongwe, odzitama, amatukutuku, oyamba zoipa, osamvera makolo, opanda nzeru, osasunga mapangano, opanda chikondi cha chibadwidwe, osakhutitsidwa, opanda chifundo: amene ngakhale adziwa kuweruza kwake kwa MULUNGU [chifukwa anapulumutsidwapo nthawi ina], kuti iwo amene achita zotere ayenera imfa, azichita iwo okha, ndiponso abvomerezana ndi iwo akuzichita” (Aroma 1:18-32).5

Dziko lapansi tsopano labweleranso kukhala ngati dziko lomwe lija la masiku a Noah (Genesis 6:5-7, Matthew 24:37-44). Maganizo a anthu lero asintha choonadi cha MULUNGU kukhala chabodza (Aroma 1:21-25).6 Choonadi  cha MULUNGU ndikuti IYE ndi mbewu yokhayo imene ili ndi moyo wosatha mwa IYE. Tsopano akunena kuti, monga anachitira m’nthawi ya Nowa, kuti choonadi ichi cha MULUNGU kukhala mbewu yokhayo ya moyo wosatha ndi bodza, ndipo akuphunzitsa ana athu zoipazi, zachinyengo, mphulupulu zopweteketsa moyo kwambiri m’masukulu onse aboma. Zisokwanira kwa iwo kukwatirana wina ndi mzake. Akufuna kuphunzitsa ana athu kuti choonadi cha MULUNGU ndichabodza. Anavomereza ziwanda (ziwanda za chiwerewere cha pakati pa amuna okhaokha kapeza akazi okhaokha, umathanyula) mwa iwo, ziwanda zamphamvu zimene zikuwapangitsa kulambira zinthu zimene zili zopatsa chilakolako cha chiwerewere, kotero amatumikira fano kuposa Mlengi (Aroma 1:25). Chifukwa cha ichi, MULUNGU waasiya.  IYE waalekelera kuchita zoipitsitsa, kuchita zoipitsitsa zawo, zimene amakonda kwambiri. MULUNGU amaona momwe am’kanira IYE ndi moyo WAKE wosatha, ndipo mwa mwano amalimbana NAYE pa chifukwachi, ndipo MULUNGU anangowasiya. MULUNGU anawasiya iwo kukhala ndi zinthu zimene akufuna, zimene zili zoipitsitsa! IYE anawalora iwo kuchita zimene asankha kuchita—akazi ndi akazi, amuna ndi amuna, kugonana kwa pakati pa akazi okhaokha ndi kugonana kwa pakati pa amuna okhaokha.

Komabe, mbewu ya MULUNGU, mbewu ya moyo wosatha ya MULUNGU, siingakhale m’moyo wa munthu oipitsitsa, chifukwa ichi chimasintha choonadi cha MULUNGU kukhala bodza! Chiwanda ichi chogonana akazi okhaokha kapena amuna okhaokha ndi champhamvu, koma YESU, mbewu ya moyo wosatha mwa IYE, ndi yamphamvu koposa.7  MULUNGU amatiuza kuti tim’kane mdierekezi ndipo adzathawa ife (Yakobo 4:7).8 Koma boma la dziko lapansi likuta ngati tikana kugonana akazi okhaokha kapena amuna okhaokha, tikupalamula mlandu wachidani.

YESU asanakwerenso Kumwamba, IYE anali atagonjetsa imfa, Gehena, manga, Satana, ndi ziwanda zonse zoipitsitsa, koma aliyense wokana moyo wosatha adzalandira mphotho chifukwa cha maganizo awo oipa.9 Adzalandira mwa iwo okha mphotho yakuyenera kulakwa kwao imene ili Gehena ndi Nyanja ya Moto, kuzunzika kosatha. Akuchita izi kwa iwo okha monga kunakhala masiku a Nowa (Luka 17:26-30).
Chakhala chizolowezi kutsatira Satana, amene wanamiza dziko lonse lapansi (Chivumbulutso 12:9).10

Zomwe ofalitsa uthenga ndi boma akuchita zikupangitsa MAWU a MULUNGU kukhala mlandu wa chidani, koma ndi moyo okhawo komanso njira yokhayo yothawira ku mazunzo ndi nkhanza zosatha ku Gehena ndi Nyanja ya Moto. YESU ndi anthu AKE ndiokhawo amene asamala za moyo wako. Osalora mzimu wa Satana kukupusitsani. Simunabadwe choncho. Chiwanda chikhonza kukulowani momwe munali mwana wamng’ono kwambiri, koma YESU amachotsa ziwanda mwa anthu.11 IYE ndi MOYO ndipo moyo wochuluka.12 “Ndadza ine kuti akhale ndi moyo, ndikukhala nao wochuluka” (Yohane 10:10).

Nditati ndikuonetsani inu momwe mungathawire chilango chosatha, mukhonza kukhulupilira kuti uwu ndi mlandu wa chidani. Moyo kuno ndiwaufupi, koma muyaya ndi wautali.13 Siumatha. Mizimu ya anthu idzakhala ndi moyo wosatha Kumwamba kapena ku Gehena.14 Tonse ndife anthu. Tonse tinapatsidwa ufulu osankha moyo kapena imfa, chabwino kapena choipa, MULUNGU kapena Satana.15 Pamene MZIMU wa MULUNGU wakulowani ndipo inu ndikusunga IYE pakumulandira IYE, MAWU AKE, tsiku lili lonse, inu mudzakwanitsa kukhala ndi mphamvu-ya-moyo WAKE mwa inu ndi mphamvu YAKE kufikira inu mudzafe. Komabe, khama lonse liperekedwe pa ichi. Satana sakusewera nanu! Akufuna inu mukakhale ku Gehena ndi Nyanja ya Moto ndi iyeyo.

MULUNGU sakusewera, nayenso. IYE anatifera pamtanda wa Kavari, kenako anauka kwa akufa ndikukwera Kumwamba kutitsimikizira ife kuti IYE ndi MULUNGU ndipo kuti ali ndi mphamvu zotipulumutsira ndikutiukitsanso ife pa tsiku lomaliza.16

Chikondi si chiwerewere. Chikondi ndikusunga malamulo a MULUNGU (1 Yohane 5:3).17 Mukatero, mudzakhala ndi moyo. YESU anati munthu wakunena kuti andidziwa INE (andikonda INE) koma osasunga malamulo ANGA ali wabodza, ndipo mwa iye mulibe choonadi (1 Yohane 2:4). “Ndipo monga iwo anakana kukhala naye MULUNGU m’chidziwitso chawo, MULUNGU anawapereka ku mitima yokanika” (ndi ku m’chitidwe wawo wokanika), kukachita zinthu zimene Satana akufuna iwo azichita, ndipo mzimu wake woipa mwa iwo umawapangitsa iwo kuvomereza kuzichita (Aroma 1:28-32).

Asiyeni opusa akhale mafumu ndikulamulira dziko ndi golide, mphulupulu, ndale, ndi zinthu zina, koma usiyeni mtima wanga ubweretse chikondi chimene sichidzakalamba. Landirani mbewu ya moyo wosatha. Yambani pakunena pemphero ili:

Prayer

AMBUYE wanga komanso MULUNGU wanga, ndichitireni chifundo ndine munthu wochimwa.1 Ndikukhulupirira kuti YESU KHRISTU ndi MWANA wa MULUNGU wamoyo.2 Ndimakhulupiriranso kuti IYE anafera pamtanda ndipo anakhetsa mwazi WAKE wamtengo wapatali ndi cholinga choti machimo anga onse akhululukidwe.3 Ndikukhulupiriranso kuti MULUNGU anaukitsa YESU kwa akufa pogwiritsa ntchito mphamvu ya MZIMU WOYERA,4 ndiponso kuti IYE anakhala kudzanja lamanja la MULUNGU ndipo panopa akumva pemphero langa lolapali.5 Ndikutsegula zitseko za mtima wanga, ndipo ndikukuyitanani kuti mulowe mumtima mwanga, inu AMBUYE YESU.6 Tsukani machimo anga ambirimbiri achoke onse mu mwazi wamtengo wapatali umene INU munakhetsa m’malo mwanga pamtanda wa ku Kavari.7 Ndikudziwa kuti mundimvera pemphero langali AMBUYE YESU; INU mukhululukira machimo anga ndi kupulumutsa moyo wanga. Ndikudziwa izi chifukwa MAWU ANU, Baibulo, limanena zimenezi.8 MAWU ANU amati INUYO simudzakana kumvetsera pemphero la munthu aliyense, ndipo ine ndili m’gulu la anthu amenewo.9 Choncho, ndikudziwa kuti INUYO mukundimvetsera pamene ndikupemphera ndipo ndikudziwanso kuti INUYO mundiyankha komanso mundipulumutsa.10 Ndipo ndikukuthokozani AMBUYE YESU, chifukwa chopulumutsa moyo wanga, ndipo ndisonyeza kuyamikira mwa kuchita zinthu zimene INUYO munalamula komanso kupewa kuchita uchimo.111

Pambuyo pa chipulumutso, YESU ananena kuti munthu ayenera kubatizidwa pomizidwa thupi lonse m’madzi, m’dzina la ATATE, ndi la MWANA, ndi la MZIMU WOYERA.12 Muziphunzira mwakhama Baibulo la Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu, [King James Version] ndipo muzichitazimene Baibulolo limanena.13

AMBUYE akufuna inu muwauze ena za chipulumutso chanu (Marko 16:15). Mukhoza kukhala ogawa Uthenga Wabwino olembedwa ndi M’busa Tony Alamo. Tikutumizirani zolembedwa zaulere. Tiyimbireni kapena titumizireni imelo kuti mumve zambiri. Gawanani uthengawu ndi wina.

Ngati mukufuna kuti dziko lipulumutsidwe monga m’mene YESU akulamulira, mukufunika kupereka chakhumi kwa MULUNGU. MULUNGU anati, “Kodi munthu angabere MULUNGU? Inde, mwandibera kale. Koma akuti, Ife tikumubera bwanji MULUNGU? Mu chakhumi ndi mu zopereka. Anthuwo ndi otembereredwa chifukwa akundibera, ngakhale mtundu wonsewu [dziko lonse lapansi]. Bweretsani nonse chakhumi [‘chakhumi’ ndi gawo limodzi la magawo khumi (10%) ya malipiro anu] m’nkhokwe zanga n’cholinga choti pakhale nyama [chakudya cha Uzimu] mu nyumba
YANGA [anthu opulumutsidwa] kuti mundiyese, akutero AMBUYE wa MAKAMU, kuti muone ngati sindidzakutsegulirani mazenera a Kumwamba ndi kukukhuthulirani madalitso amene mudzasowa malo owalandirira.” Ndipo ndidzadzudzula anthu okudyerani masuku pamutu ndipo sadzawononga zipatso za nthaka yanu; ngakhalenso mphesa wanu sudzalephera kubala zipatso pa nyengo yake m’minda yanu, watero AMBUYE wa MAKAMU. Ndipo mitundu yonse idzakutchani odala: chifukwa
dziko lanu lidzakhala labwino, watero AMBUYE wa MAKAMU”(Malaki 3:8-12).


Chichewa/Nyanja Alamo Literature

Ngati mukufuna kudziwa zambiri kapena ngati mukufuna mabuku kapenanso nkhani zina zimene zimakusangalatsani, tiimbireni foni kapena tilembereni.

Tony Alamo, World Pastor
Tony Alamo Christian Ministries Worldwide
P. O. Box 2948
Hollywood, CA 90078

Lamya ya pemphero ndi uthenga maola 24: (661) 252-5686

Tony Alamo Christian Ministries Worldwide imalandira anthu onse ndipo imapereka zinthu zofunika Kwa onse amene ali ku U.S. amene akufunitsitsadi kuti ayambe kutumikira AMBUYE ndi mtima wawo wonse moyo wawo wonse ndi mphamvu zawo zonse.

Mapemphero amachitika mu Mzinda wa New York Lachiwiri lili lonse nthawi ya 8 Koloko usiku ndi madera ena usiku okhaokha. Chonde imbani foni kuti mumve zambiri: +1 (908) 937-5723. ZAKUDYA ZIMAGAWIDWA PA MAPETO PA MAPEMPHERO ALI WONSE

Funsani buku la M’busa Alamo, lakuti Mesiya, losonyeza KHRISTU kuyambira ku Chipangano Chakale mu maulosi oposa 333.

Khalani wogwira ntchito yokolola miyoyo ya anthu pakukhala ogawira mabuku a M’busa Alamo. Mabuku ndi zinthu zonse zomvetsera n’zaulere, ndipo simulipira ndalama yotumizira

M’BUKU ILI MULI CHIKONZERO CHENICHENI CHA CHIPULUMUTSO (Machitidwe 4:12).
MUSALITAYE, PATSANI ENA KUTI AWERENGE.

Anthu amene muli m’mayiko ena, tikukulimbikitsani kuti mumasulire n’chinenero chanu mabukuwa. Ngati mukusindikizanso bukuli, musaiwale kuika mawu ali m’munsiwa omwe ndi okhudzana ndi zamalamulo:

© Copyright November 2014, February 2015 All rights reserved World Pastor Tony Alamo ® Registered November 2014, February 2015


Makalata opita kwa M'busa Alamo
Nigeria
Okondeka M’busa Tony,
Moni kwa inu mu dzina la Yesu. Ndine okondwa kukudziwitsani kuti ndakhala kale mtumiki wa Mulungu kudzera m’mabuku a uthenga wabwino amene ndinawerenga komanso porogaramu yanu ya pa Radio Africa. Ndikukuthokozani ndi m’mene mukuulutsira Mau a Mulungu kwa ife kuno. Ndine wongosinthika kumene ndipo ndikufuna munditumizire Baibulo Lopatulika lathunthu ndi makalata a nkhani pamodzi ndi mabuku a Messiah. Ndinali wosochera ndipo ndapezekanso.
Ambuye adalitse utumiki wanu koposa. Ndikhulupilira kuti ndimva kuchoka kwa inu posachedwa.
Wanu Mokhulupirika,
Mone Akinwa and family
Sunshine State, Nigeria

Congo
(Zomasuliridwa kuchoka kuchi Faransa)
M’busa wa dziko lonse Tony Alamo,
Mtendere mwa Khristu! Ndine M’busa Andre Hilarion, m’modzi  mwa okonda kwambiri kuwerenga nkhani zanu za m’makalata. Makamaka munali mu 2006 m’mene ndinazindikira za zolemba zanu zosindikizidwa ndipo zinasinthiratu utumiki wanga. Chifukwa Mzimu Woyera unanditsegula maso pamene ndinaziwerenga. Pachifukwa ichi, pa tchalichi pomwe ine ndili m’busa, tsopano tikugwiritsa ntchito zolembedwazi  “Chinsinsi cha Papa’’ ngati chida chopelekera umboni m’malo opezekera anthu, ndipo Ambuye tsopano akuchita zinthu zazikulu. Sabata iliyonse tikumalandira anthu atsopano omwe akumagwidwa ndi Mzimu Woyera akatha kuwerenga ndikuchilandila, popereka mitima yawo kwa Yesu ndikuyamba moyo watsopano.
Tsopano, chomwe tikupempha ndi chakuti muzititumizila makalata ambiri mosalekeza ndi nkhani zamu chiFaransa zomwe zidzatithandize kukhanzikitsa malo ogawilira zolembedwa za M’busa Tony Alamo.
Kotero, M’busa Tony Alamo, Mulungu wanu ndi Mulungu wathu. Cholinga chanu chakhala cholinga chathunso. Ndipo nkhondo yanu ndi nkhondo yathunso. Tikuthokozelatu , ndipo tikupemphera kwa Mulungu wa Mphamvu zonse kuti mupitilirebe kukhala njira ngati m’dalitso wathu komanso wa anthu a mitundu ina yonse.
Andre Hilarion
Kimpese, Democratic Republic of the Congo

Missouri

Okondeka M’busa Tony Alamo
Ndili oyamika chifukwa cha utumiki wanu ndi chibvumbulutso cha choonadi chomwe Mulungu anakupatsani. Mwanditsekula m’maso m’choonadi ndikulimbikitsa chikhulupiliro changa mwa Mulungu, mwandiululira  zinyengo za Satana, boma la maiko onse, ntchito zake zosutsana nafe, Mkwatibwi, ndi zonse zomwe amagwiritsa nthito mu dziko losocherali.
Chonde nditumizireni zipangizo zonse zimene mungakwanitse kundipatsa. Ndikuzifuna ZONSE. Zikomo kwambiri ndipo Mulungu Wamoyo akudalitseni ndi utumiki wanu kopambana mu chisomo ndi mphamvu Zake!
Chonde muyike dzina langa pa m’ndandanda wa mapemphero anu.
Mwa Khristu,
Terry Birmingham                                                                     Cameron, MO

India

Okondeka M’busa Tony,
Ndinapita kumudzi kwa bambo anga kotchedwa Sandipudi masiku khumi apitawo kukaona nyumba yathu yakale. Ndipo kunali okhulupilira odwalika kwambiri atagona pa bedi lake anthu nkumaganiza kuti mwina wamwalira, koma ndinapita kukamuona ndi kukamupemphelera. Mulungu anamva mapempherowo ndipo anamuchiritsiratu. Kudzera munjira imeneyi mseu onse unandipatsa ulemu kwambiri, koma ndinakhulupilira ndipo ndinanena kwa iwo, “Si ine, koma Yesu ndi amene wachita izi. Tiyeni timutamande ndi kumupatsa ulemu Iye.”
Ndikhulupilira kuti mapemphero anu aphindu anandithandiza mu utumiki Wake. Tiyeni timulemekeze Iye kudzera m’machitidwe komanso m’mawu.
Ndikukuthokozani nonse. Chonde ndipempherereni ndi zolinga zathu koposa.
M’chikondi chake,
M’bale wanu,
Rajesh Tatapudi
Andhra Pradesh, India

Kenya

Moni M’busa Tony Alamo,
Ndadzichepetsa chifukwa chakukhudzidwa kwanu. Ndinadalitsika kwambiri ndi kalata yanu ya nkhani “Ndinam’peza Yesu pa webusaiti ya Tony.” Ndinayiwerenga nkhani ndipo ndinanena pemphero lopempha chikhululuko pa kalata ya nkhani. Ndinalapiratu machimo anga, ndipo ndinasunthidwa mpaka misonzi pamene ndimanong’oneza bondo panthawi yomwe ndinataya m’dziko kunyoza Mulungu! Ndinamva kupepukidwa katundu olemetsa wa machimo atachoka mwa ine. Zoonadi ndikumva kupepukidwa ndi kumasulidwa. Oh, ndithudi ndinkasowa chisangalalo choterochi, chisangalalo chokhululukidwa machimo, chisangalalo chokhala mwa Khristu. Ndikuthokoza AMBUYE populumutsa moyo wanga ndipo ndikupemphera kuti MZIMU WOYERA undiyang’anire munjira iyi ya uzimu. Tsopano, ndine ongoyamba kumene mu ulendo wa uzimuwu. Chonde ndiyang’anireni mmene ndizichitira ndikuchititsa manyazi mdierekezi ndi bodza lake. Ndikubwerenzanso kuti ndikuyamika mautumiki anu pamene akupereka chili chonse chokhudzana ndi uzimu. Mulungu akudalitseni kopambana inu pamodzi ndi mautumiki anu.
Sarah Terry                                                      Bungoma, Kenya

Arkansas

Okondeka M’busa Tony,
Lero ndinali ndi mzanga amene ali m’Khristu wobadwanso mwatsopano. Anali kumaliro. Mzibambo amene anamwalira anali m’busa, ndipo panali anthu ambiri pa maliro ake. Umboni wake asanamwalire unali wakuti kulikonse kumene adzapite, adzakhala akuuza anthu nthawi zonse, kaya ndiku Walmart kapena m’sitolo ya mankhwala kapenanso pamsewu, “Kodi mumamudziwa Yesu Khristu ngati Mpulumutsi wa moyo wanu? Muli m’chiyero ndi Mulungu?” Anachita izi pali ponse pamene amapita, mpaka anthu ena ankadabwa chifukwa chake ankachitira izi.
Ndithu, ku maliro, mwana wake wamkazi anayima ndikunena kuti, “Ndikufuna kukuuzani nonse nkhani ya bambo anga. Ndili wamng’ono, ndili ndi zaka pafupifupi 13, ndimakonda kupita nawo nthawi zambiri, ndipo kuli konse komwe timapita amaima ndikufunsa wina wake ngati anali bwino ndi Yesu, kapena ankanena kuti, ‘Kodi ukumudziwa Yesu Khristu ngati Mpulumutsi wa moyo wako?’ Panali nthawi zina zimene ndimaona ngati ankaonjeza. Amatha kuuza aliyense, ndipo ankangopitilizabe.
“Tsiku lina tinalowa mu galimoto ndipo ndinati, ‘Bambo, ndi chifukwa chiyani mumauza aliyense za Yesu?’ Bambo anga anati, ‘Mwana wanga, ndikuuza nkhani. Ndinali ndi masomphenya a maloto pamene ndinali ndi zaka 17, ndipo m’masophenyawo ndinamwaliramo ndi kupita Kumwamba. Anali malo okongola kwambiri kuposa onse. Kenako ananditengera ku mphepete kwa Kumwamba, ndipo ndinayang’ana pansi mu Gehena. Ndinaona manja atakwenzedwera kwa ine ndipo amakuwira pa ine, “N’chifukwa chiyani sunatiuze! N’chifukwa chiyani sunatiuze! N’chifukwa chiyani sunatiuze!” Ndipo anali anthu amene ine ndimawadziwa. Maloto anatha ndipo ndinabwelera pano pa dziko lapansi ndipo ndi chifukwa chake ndimauza aliyense.’”
Mzanga ananena kuti zinamukumbutsa zambiri za ife, ndi zolemba za M’busa Alamo, chifukwa kuli konse komwe tingapite, timakhala tikugawa zolembedwa nthawi zonse. Ananena kuti M’busa Tony wakhala akuchenjeza anthu kwa zaka ndi zaka.
Alemekezeke Ambuye,
M’bale Tommy

Nigeria

Okondeka Mpingo wa  Alamo,
Landirani moni mu dzina lodalitsika la Ambuye ndi Mpulumutsi wathu Yesu Khristu. Kalata ya nkhani ya dziko lonse ya Tony Alamo Christian Ministries ikusintha miyoyo ya mzinda wa Igodan Lisa ku Nigeria. Kudzodza kwa kalata imeneyi ndi kwakukulu kwambiri. Yathandiza moyo wanga wauzimu pondisunthira malo ena otha kumvetsa zinthu za Mulungu. Anali ogawa makalata wanu amene anandipatsa kalata yanu ya nkhani yotchedwa “Chivomelezi.” Ndinapezeraponso mwayi opatsa anthu ena ndipo kwa onse amene ndinawapatsa pepala, analandira Yesu kukhala Mbuye wa moyo wao. Ulemelero, matamando akhale kwa Mulungu.
Chonde ndikupempha kuti mutitumizire zambiri, kuti atithandize kukopa miyoyo yambiri. Mulungu adalitse ntchito zanu. Zikomo.
Wanu mwa Khristu,
Jasaau Imamu                                                           Ondo State, Nigeria

New York

Okondeka M’busa Tony Alamo,
Ndinalandira kalata yanu ya nkhani m’njira ya sitima ya panjanji ypyenda kunsi kwa nthaka (subway) ku New York, ndipo inandipeza nthawi yomwe ndinkafuna thandizo kwambiri. Uthenga womwe uli m’zolembedwa zanu ndiofunikira kwambiri.
Ndikupemphanso bukhu lanu lotchedwa Mesiya, nkhani za m’makalata 100, komanso mauthenga a pa CD.
Zikomo,
Eric F.                                                                         Rhinebeck, NY

Kuchokera ku Nthambi yathu Yomasulira Mawu

Tikugwira ntchito yomasulira Ilacono (chiyankhulo choyankhulidwa ku Mpoto kwa Phillipines), ndipo m’modzi mwa omasulira ndi wachinyamata amene analeledwa Pentekosto, anatsiliza maphunziro ake a zauzimu ku seminale (theological seminary), ndi kuphunzitsa pa sukulu ya Baibulo ya ana. Tchalitchi chawo chili ndi matchalitchi ena 50 amene anamwazikana ku Mpoto kwa Phillipines konse, chili chonse ndi M’busa wakewake. Panopa akugwira ntchito ndi American Bible Society kumasulira ndemanga za m’Baibulo ndi kuthandizira bukhu lili lonse la Baibulo.
Anatiuza kuti pamene anaona za umwinimwini (copyrights) pa “Chinsisi cha Papa,” “Papa Wothawa Mlandu” “Yesu Anati Satana akadakhala ndi Tchalitchi komanso Boma,” ndi “Mfumukazi ya Mahule,” anaona kuti zinali zoti zinalembedwa m’zaka za ma 80 ndi 90. Anati ndizozizwitsa kuti M’busa Alamo analemba mfundozi kalekale, ndipo pa nthawi imeneyo palibe yemwe ankaona kuti ndi zoona, koma pano mutha kuona mosavuta. M’busa Alamo anadziwa zinthuzi wina aliyense asanadziwe ndipo anazisindikiza kuti achenjeze aliyense.
Iye anati Phillipines ndi ya Katolika kwambiri sungamuuze munthu za Ambuye, koma atawerenga makalata a anthu opempha zolembedwa kuti azigawa ndi kuchitira umboni kwa anthu, anapempha zolembedwa100 pa gawo lili lonse la zomwe zinalembedwa  zomwe anathandiza kumasulira kuti akagawe. Anayitanitsanso bandulo ya mabuku a Mesiya. Iye anati, “Ndimamasulira zaku Bible Society, koma izi ndi zokopa miyoyo.” Iye anati ndiosangalala kukhala gawo la izi, ndipo akugwiritsa ntchito zolembedwazi m’makalasi ake. Iye anati, “Ndakhala ku seminare ndipo zili mwa ine, koma zolembedwazi ndi zoona komanso ndi zofunikira kwambiri. Ndikutha kuona kufunikira kwa zimene zikuchitika pano m’moyo mwanga. Ndikuona zolembedwazi ndi zimene zikuchitika pano.”

*********************************
Omasulira m’chi Swahili ndi mayi wa ana atatu yemwe mwamuna wake ndi m’busa. Iye anati amayenera kukhala wachilungamo, kuti mmene amagwira ntchito pa magawo a zolembedwa zosiyanasiyana okhudza Papa, ankaganiza kuti zina mwa zomwe ankamudzudzula Papa ndi Tchalitchi cha Katolika zinali zongopeka ndi zongoganizira. Anati amadziwa kuti chiKatolika chinali chiphunzitso chabodza, kotero choonadi cha mauthenga analibe nacho ntchito nabola anthu amachikana. Komabe, sankakhulupilira.
Iye anati mamuna wake ankawerenga zolembedwazi usiku wina ndipo anafunsa, “Ndi chifukwa chiyani unayitanitsa izi?” Anati kwa iye, “Kuti ndikagawe kwa anthu ndikapita ndi ana ku paki.” Nthawi yomweyo anati, “Ayi ndithu! Uzisunge izi! Sungakangozigawa zimenezi. Izi ndi zoona! Tiyenera kuziwerenga.” Anati, “Ndinapita ku koleji ya Baibulo ndipo zinthu izi zimaphunzitsidwa ndi kulembedwa ndipo zonse zalembedwazi ndi zoona.”
Iye anati anamuyang’ana mwamuna wake ndipo anayankhula chamumtima, “Unapita ku koleji ya Baibulo zaka zapitazo ndipo umadziwa zinthuzi kuti ndi zoona.  Ndi chiyani iwe kapena koleji munachita kuchenjeza dziko lapansi? Iwe ngakhale ali yense palibe amene anachitapo kanthu za izi. Bambo uyu (M’busa Alamo) anaitanidwa mwa padera ndi Mulungu kuti ayankhule chifukwa iwe ngakhale ali yense simunatero kapena simukutero.”

******************************
Omasulira waku Sweden analeredwa Purotestanti, koma kwa zaka zambiri wakhala alibe nazo ntchito za tchalitchi, mpingo, kapena Mulungu. Ndi oona za ndale, olimbana ndi zolakwika zosiyanasiyana m’boma la Sweden. Amalemba ma bulogu a zandale ndipo amakhala ndi misonkhano komanso amamasulira zolembedwa mwa padera. Amavomereza kwambiri zikhulupiliro zake, koma akuwerenga kanusu kotengedwa m’bukhu la Mesiya, anayamba kulira atawerenga, “Gulu linafuula, ‘Mpachikeni Iye, Mpachikeni Iye’.” 
Iye anatiuza kuti, “Ndaphunzira njira za ziwembu (conspiracy theories), koma sindinaonepo aliyense akugwirizanitsa zonse ku Vatican ngati chonchi. Izi ndi zodabwitsa. Ndikukonda ndithu kuchita ichi. Nonsenu mwayamba kundipatsa chikoka. Ndimalemba bulogu yanga ndipo ndinangoona ndikutchula za Chivumbulutso.”

************************************
Omasulira waku Serbia, yemwe ali ndi digri ya batchala mu history, anati ndi zosangalatsa kutengapo mbali pa izi. Anati Serbia ili ndi mbiri yovuta kumvetsa yokhudzana ndi nkhanza za chipembedzo ndi kuphana kwambiri, ndipo M’busa Alamo akuvutika ndi mazunzo okhudza chipembedzochi ndipo akulankhulabe. Iye anati zimenezi ndi zosangalatsa.

Cuba

(Zomasuliridwa kuchoka mu Spanish)
Moni kuchoka ku Cuba,
Mtendere wa Ambuye ukhale ndi aliyense. Tithokoze Ambuye, lero tinali ndi m’dalitso otenga maphukusi ena awiri.
Tithokozereni kwa atumiki onse a Mulungu omwe ali ndi mdalitso ofalitsa Mawu ku dziko lonse kudzera mu utumiki umenewu. Ndikuthokoza mwa padera kwa onse.

Mulungu akudalitseni,
Reverend Marrero      Havana, Cuba


footnotes:

1. Mat. 4:3-4, Yoh. 1:1, 14, 1 Yoh. 1:1-3, 5:11, Chiv. 19:13 return

2. Mark 16:15-16, 1 Ako. 1:21-24, 6:19, 2 Ako. 5:17-21 return

3. Yoh. 15:16, 19, 17:6, 14-16, 2 Ako. 6:14-18, 1 Pet. 2:9 return

4. Mat. 4:4, 10:22, 24:13, Yoh. 5:24, 6:63, 11:26, Mac. 14:22, Aro. 11:22, Ako. 1:22-23, 1 Tim. 4:16, 2 Tim. 2:1-3, 3:13-17, 4:5, Yak. 5:10-11, 1 Yoh. 2:24-25 return

5. Gen. 19:1-13, 24-25, Lev. 18:22, 20:13, Det. 22:5, 23:17-18, Owe. 19:22-28, 1 Maf. 14:24, 15:11-12, 2 Maf. 22:1-2, 23:7, Ezek. 16:49-50, Aro. 1:18-32, 1 Ako. 6:9-10, 1 Tim. 1:9-10, 2 Tim. 3:1-5, Yuda 7, Chiv. 22:14-15 return

6. 1 Tim. 4:1-3, 2 Tim. 4:3-4, 2 Pet. 2:1-3 return

7. Det. 4:39, 32:39, 1 Sam. 2:6-8, 1 Mbi. 29:11-12, 2 Mbi. 20:6, Mas. 46:1, Yes. 44:6, 45:23, Yer. 10:10, 18:6, Dan. 4:35-37, Yoh. 10:29, Mac. 17:24-26, Chiv. 1:12-18 return

8. Mat. 4:1-11, Aro. 12:9, Aef. 4:27, 5:3-17, 1 Ate. 5:21-22 return

9. 1 Mbi. 28:9, Yobu 4:7-9, 21:14-20, Miy. 1:22-32, 8:36, 10:25, Yes. 1:15-20, Dan. 12:2-3, Luka 12:4-9, Yoh. 3:16-21, 36, Aro. 1:18, 1 Ako. 6:9-10, Yuda 14-15, Chiv. 20:11-15, 21:8, 27 return

10. Mat. 24:11-12, 24, 1 Tim. 4:1-2, 2 Tim. 3:13, 2 Pet. 2:1-3, Chiv. 13:1-4, 11-15, 14:8, 17:8, 18:2-3, 23 return

11. Mat. 8:16-17, 28-34, 9:32-33, 10:1, Marko 1:34, 39, 7:25-30, 9:17-27, 16:9, Luka 11:14 return

12. Yoh. 11:25-26, 14:6 return

13. 2 Sam. 14:14, 1 Mbi. 29:15, Yobu 7:6-10, 8:9, 9:25-26, 14:1-2, Mas. 22:29, 39:4-6, 11, 78:39, 89:47-48, 90:5-6, 9-10, 102:11, 103:14-16, 144:3-4, 146:4, Mlal. 1:4, 3:19-21, 6:12, 12:7, Yes. 2:22, 40:6-8, 24, 51:12, Yak. 1:10-11, 4:14, 1 Pet. 1:24 return

14. Yes. 66:24, Dan. 12:1-3, Mat. 25:31-46, Marko 9:42-48, Yoh. 5:26-29, Aro. 2:1-16, Chiv. 14:9-11 return

15. Det. 30:14-20, Yos. 24:14-15, Ezek. 18:19-32, 33:11, Yow. 3:14, Mat. 16:24-27 return

16. Marko chap. 16, Yoh. 11:25-26, Mac. 2:29-33, 4:10-12, 1 Ako. 15:3-22, 1 Pet. 1:3-5 return

17. Eks. 20:6, Det. 7:9, 11:1, 13-15, 30:16, Yos. 22:5, Yoh. 14:15, 21, 15:10, 2 Yoh. 6 return


prayer footnotes:

1. Masa. 51:5, Aro. 3:10-12, 23 return

2. Mat. 26:63-64, 27:54, Luka 1:30-33, Yoh. 9:35-37, Aro. 1:3-4      return

3. Mach. 4:12, 20:28, Aro. 3:25, 1 Yoh. 1:7, Chiv. 5:9      return

4. Masa. 16:9-10, Mat. 28:5-7, Marko 16:9, 12, 14, Yoh. 2:19, 21, 10:17-18, 11:25, Mach. 2:24, 3:15, Aro. 8:11, 1 Akor. 15:3-7      return

5. Luka 22:69, Mach. 2:25-36, Aheb. 10:12-13   return

6. 1 Akor. 3:16, Chiv. 3:20      return

7. Aef. 2:13-22, Aheb. 9:22, 13:12, 20-21, 1 Yoh. 1:7, Chiv. 1:5, 7:14      return

8. Mat. 26:28, Mach. 2:21, 4:12, Aef. 1:7, Akol. 1:14      return

9. Mat. 21:22, Yoh. 6:35, 37-40, Aro. 10:13      return

10. Aheb. 11:6     return

11. Aheb. 5:14, 8:11, Aro. 6:4, 1 Akor. 15:10, Chiv. 7:14, 22:14      return

12. Mat. 28:18-20, Yoh. 3:5, Mach. 2:38, 19:3-5   return

13. Deut. 4:29, 13:4, 26:16, Yoswa 1:8, 22:5, 2 Tim. 2:15, 3:14-17, Yakobo 1:22-25, Chiv. 3:18 return