YESU ANANENA
KUTI SATANA ADZAKHALA NDI
TCHALITCHI NDI BOMA

Zolembedwa mu 1993

Mu Ufumu wa Kumwamba, Satana analankhula kuti adzatenga malo a Mulungu, ndipo ndithudi analephera. Satana anatenga ulamuliro wa dziko lapansi limene Mulungu adamupatsa Adamu pomunyengelera mkazi wa Adamu. Hava kenako adamunyenga Adamu, kudzera mwa Satana, ndipo kulumikizana kwa pakati pa munthu ndi Mulungu kunatha. Mwa chifundo pa ife, Mulungu anakonza njira ya chipulumutso kwa onse okhulupilira Iye m’malo mwa Satana. Mwana wa Mulungu anafa ndi kukhetsa mwazi pokwanilitsa ntchito za chipulumutso kukhaladi zoona. Njira YOKHAYO yomwe Mulungu anakonza iyenela kukhala yobisika, yosaoneka bwinobwino kapena yosamveka bwino ndi Satana, kapena ulamuliro wake udzatha. Kuti izi zitheke, Satana ayenera kudziwitsa anthu kuti iye kulibe (ndipo wachita ntchito yabwino ya ichi). Kumwamba, Satana anasintha 1/3 ya angelo (anakhulupilira bodza lofookali m’malo mwa Mulungu oona, wamphamvu) ndipo onse anaponyedwa pansi kuchoka Kumwamba kupita pa dziko lapansi. Satana anaona kukongola, kusangalatsa, komanso chisangalalo cha Kumwamba chomwe Mulungu anachilenga m’munda wa Edeni, ndipo mwa nsanje ndi chizondi Satana anaona awiri osachimwao omwe Mulungu anawadalitsa ndipo amene Iye anawapatsa ulamuliro wa dziko lapansi. Satana anaona kuti madzulo kukakhala bata, Yesu amabwera kumunda kudzakhala ndi awiriwo. Asanachimwe panalibe malire pakati pa munthu—chilengedwe cha Mulungu—ndi Mulungu, ndipo amalankhulana nthawi zambiri monga abwenzi, olengedwa kumulankhula mlengi wao wodabwitsa, mosaopa. Mgwirizano wao ndi Khristu unali wa pamwamba tsiku lili lonse, ndipo ankaphunzira kuchokera kwa Iye za ulemelero wa Mulungu, tanthauzo la zinthu zonse, ndi chitsimikizo cha chiyanjano chimenechi choti ndithu Mulungu amawakonda. Anauzidwa zotsatira za kusamvera ku lamulo limodzi loti asagwire kapena kudya chipatso cha mtengo wa m’munda wa pakati (mtengo wozindikira zabwino ndi zoipa). Satana anadziwa kuti Kumwamba, ukambelembere wake unali woti unakwanitsa kunyenga 1/3 ya chiwelengero chake kupita kumathero kopanda mfundo komanso kuchionongeko. Anachimva kuti atakwanitsa zofuna zake Kumwamba, ngakhale kumapeto kwake analephera, akhonza kukwanilitsanso kulanda ulamuliro kuchoka kwa awiri osachimwawoM’munda wa Edeni omwe Mulungu anawapatsa wa dziko lapansi. Malemba amati pa alionse mungamve, ameneyo ndi mtsogoleri wanu. "Iye amene ali wa Mulungu amamva mawu a Mulungu: inu simumamva chifukwa simuli a Mulungu" (Yohane 8:47). Pa ukamberembere wa Satana podzibisa kukhala ngati mngelo wapamwamba  wa kuwala kwa Mulungu (2 Akorinto 11:14), anapangitsa Hava kusalabadira za chenjezo lochoka kwa Mulungu, Mwana, omwe Iye anawapatsa mu umodzi wa usiku omwe anawayendera. Chomwecho, Satana anakhala  bwana wa Hava. Nthawi yomweyo anakhala mtumiki woyamba wa Satana ndipo Adamu anakhala yemwe anamusintha. Choncho, ulamuliro wa dziko lapansi unapita kwa Satana, ndipo khoma lopatula Mulungu mdi munthu linakhanzikitsidwa.

Dziko lapansi linakhala mdima, ndipo kulumikizana pakati pa Mulungu ndi munthu kunatha, pokhapokha malangizo a chipulumutso a Mulungu atatsatidwa mwa ndondomeko. Dongosolo linakhanzikitsidwa, ndipo linatchedwa dongosolo la chipulumutso. Mwana wa Mulungu ayenera kubwera kudzafa powonetsa anthu onse kuopsa kwa uchimo ndi Gehena. Komanso, Mulungu ayenera kuoneka pa nsembe Yake chikondi Chake chosaneneka kwa anthu chomwe sungachimvetse (2 Akoronto 9:15). Zopereka za nsembe yopseleza ndi maguwa a nsembe zinakhanzikitsidwa ngati chizindikiro cha munthu kuonetsa mwa chikhulupiliro kuti Mulungu adzatumiza Mwana Wake wobadwa yekha, Khristu. Ngati munthu anakhulupilira kuti Mulungu zoonadi adzatumiza mwana Wake wobadwa Yekha kudzafa pa mtanda ndi kukhetsa mwazi Wake pofuna kukhululukira mzimu wa munthu, ndiye kuti anakaonetsa chikhulupiliro Chake potenga nkhosa yabwino kuposa zonse, yopanda banga kapena chilema, kuipha, kuwaza mwazi Wake pa guwa la nsembe (guwa la nsembe ndiye chizindikiro cha mtima wa munthu), ndipo kenako ndi kuotcha nsembe ndi moto pokhulana. Fungo la chopereka lidzakwera Kumwamba ngati fungo lonunkhira-lokomera Ambuye. Zimenezi zinamuonetsa Mulungu kuti munthu ameneyu amakonda ndi kukhulupilira Mulungu osati Satana. Satana amadana ndi ndondomeko ya chipulumutsoyi chifukwa inagwirizanitsanso munthu ndi Mulungu ndi kuthetsa ufumu wa Satana pa munthu. Khoma lopatula lomwe linasiyanitsa wina ndi mzake tsopano linakhala ndi khomo—chikhulupiliro choti kukhulupilira mwa Mulungu kudzera mwa Yesu Khristu, Khomo, Njira, Moyo, Choonadi, Alfa, Omega, Oyamba, Otsiriza, Alfa, Kuwala ndi Nyenyezi ya M’mawa, "INE NDINE" Mfumu ya Mtendere, Mfumu ya Moyo, Mpulumutsi, Ambuye, Mlengi wa dziko ndi zonse zili m’menemo, Woyamba ndi Wotsiriza wa chikhulupiliro chathu, Iye ndiye kudzadza kwa thupi lauMulungu, ndipo mwa Iye takwaniritsidwa, kukumananso ndi Mulungu.

Inde, Satana anadana ndi ndondomeko za chipulumutso zomwe zinakhanzikitsidwa pa munthu. Onse amene ali anthu a dziko lapansi anali pa ulendo opita ku Gehena pokhapokha ngati njira yothawira (chipulumutso) inaperekedwa bwinobwino mwadongosolo ndi okhudzidwa amene anapeza kale njira. Mulungu amawadziwa anthu a chifundo, poti ndi omwe amakhudzidwa ndi za anthu ena omwe asokonezeka ndi mmene angapezere chipulumutso, ndipo anali malingaliro a Satana kuti asokoneze omwe amuphwekera. Wakhala akukwanitsa kulanda dziko ndikale mwa chinyengo cha usatana (podzibisa ndi kumaoneka ngati mngelo). Popitiriza kukwaniritsa kwake ayenera kukhala ndi tchalitchi, ndipo tchalitchi ichi chidzaphunzitsa kuti Satana ndiye Mulungu. Kuti izi zichitike, ayenera kukhala osamala, wa chinyengo, wa chinsinsi. Ukamberembere pano uyenera kugwiritsidwa ntchito kuposa kale. Aliyense asazindikire kuti ndi tchalitchi cha Satana, ndipo aliyense asazindikire kuti tchalitchichi ndi njira yaku Gehena. Tchalitchichi chiyenera kupempha maboma, pa zandale ndi zachuma, ndi cholinga chokopa atsogoleri a m’dziko lapansi, ndipo pomvera chidzapereka mphatso zopanda umulungu, ngati angabwenzere kukondeledwako. Atsogoleri amene Satana adzawaike pa ichi ayenera kukhala osunga chinsinsi kwambiri, kulumbiritsidwa kuti adzamvera mopanda kusunga chofuna chili chonse cha Satana. Atsogoleri oikidwa asadzaipitse tchalitchi cha Satana kapena kuulula kuti zoipitsitsa za katangale zonse za m’dziko lapansi ndi nthambi zochokera kwa iye (umene uli mtsitsi wa zoipa zonse, Satana iye yemwe). Dziko lapansi lisaone zochitika kuseri kapena m’zipinda zovalilamo. Tchalitchi cha Satana chiyenera kukhala chachikulu, matchalitchi okongola kwambiri, nyimbo zake zokwera kuposa za matchalitchi ena onse. Miyambo yake idzaoneka yolungama, ngakhale miyambo yonse, monga kuyatsa kwa makandulo, kuimba kwa mabelu, kuyatsa kwa lubani, ndi mitundu yonse ya miyambo yomwe tchalitchi chake chimachita zosiyana ndi malemba. Zochitika za tchalitchi chake chikhale zosokonezeka zoti munthu sungathe kuzimvetsa. Tchalitchi cha Satana chikhale chodzichepetsa kwambiri (ngakhale kutakhala kudzichepetsa kwa bodza), azioneka othandiza kwambiri ndi amphamvu, ndipo mapeto ake, Yesu asanabwerenso pa dziko lapansi, kuti akhale ndi mphamvu zolamulira maboma onse, ndi cholinga choti mphamvu zikhanzikitsidwe pamene vumbulutso lake (kuti ndi odana ndi Khristu) ladziwika.

Kodi tili pafupi bwanji ndi kubweranso kwa Khristu padziko lapansi? Kodi tili pafupi bwanji ndi tchalitchi cha Satana cholamulira maboma?

Zaulutsidwa kwa ife kuti gulu la a Khristu aku Texas anamufunsa Attorney General waku Texas (Jim Mattox) pa 19 May, 1986, "Kodi ndi zoona kuti boma la Texas  latenga ana athu kukhala ake?"
Attorney General Mattox waku Texas anayankha, "Inde, ndi zoona (kuti boma  latenga ana anu kukhala ake) ndipo osati ana anu okha ayi komanso inuyo!"

ULAMULIRO WA TCHALITCHI CHA SATANA WA BOMA LA U.S.

A gestapo I.R.S. ali pachintchito chochotsa onse osapereka msonkho ku matchalitchi osavomerezeka kapena kuti achilendo ku matchalitchi ndi boma za Satana. Kwa zaka I.R.S. yakhalanso ili pachintchito kuwapatsa mabungwe a tchalitchi cha Satana chilolezo chosalipira msonkho, monga matchalitchi onse a afiti ndi magulu a afiti. Bungwe lili lonse la communist ku United States linapatsidwa chilolezo chosapeleka msonkho cha 501(c) (3) kuchokera kuchokera ku tchalitchi cha Satana I.R.S. gestapo agency.

Mfundo ikhonza kupezeka m’malo ambiri, amodzi mwa iwo kukhala Prentice Hall Federal Tax Book, Chapter 28, Social Security Taxes, Section 3804 Exemptions.1

A Katolika a Chiyanjano cha Yesu (Jesuit) ambiri analowelera m’maboma athu kuchokera kwa Ronald Reagan kutsika pansi, kuti iwo odana ndi America, odana ndi Khristu, anthu odana ndi malamulo a U.S. athananso ndi Unamerican Activities Commission ndi House of Representatives' International Security Subcommittee. Awa oukira onyoza chilungamo mwa chinsisi athetsa nthambi yomwe inkakana za a Katolika owukira Communist m’dziko mwathu. Chikatolika ndi gulu la chiphunzitso choipa chosavomereza kuti Mulungu aliko. Komwe komiti inkaimba milandu yokwana 55,000 yakuukira m’chaka chili chonse panopa yangozenga milandu 14 yokha kuchoka mu 1974 mpaka 1982. Okhawo amene akuzengedwa milandu pano ndi boma la zausatana ndi omwe amaulura za tchalitchi cha Satana ndi boma, anthu monga ine ndi Holy Alamo Christian Church ndi anthu ena okonda dziko lawo aku America omwe sia Katolika. A Neo-Nazi si anthu okonda dziko la America kapena a Khristu. Ndi gulu lina lachisilikali la Katolika lomwe linayambitsidwa ndi boma la Satana pofuna kuonetsa F.B.I. kukhala ngati ndiyabwino (kuika nkhope yabodza yatsopano pa F.B.I.) lomwe lisali lina koposa gulu la chisilikali lachi Katolika lomwelo. Mwachizolowezi a Neo-Nazi bwezi atamangidwa kale  chikhala kuti boma la malamulo la U.S. (mwa Mwa Mulungu Tikhulupilira) lidakalipo. J. Edgar Hoover munthawi yake yonse analamulidwa ndi Catholic Cardinal Spellman. F.B.I. ndi Katolika yeniyeni (Ku Nazi Germany ankatchedwa Gestapo, pano akutchedwa F.B.I.). Tili ndi umboni kuchokera kwa anthu ambiri (kuphatikizapo munthu wina yemwe anali wa F.B.I. yemwe anatembenuka kukhala wa Khristu m’tchalitchi chathu) izo zikuthilira ndemanga kuti F.B.I., I.R.S., Nthambi Yoona za Antchito, komanso onse achitaganya ndi mabungwe aboma a gestapo ndi a Katolika; ndipo analonjeza kulipira ogwiritsa ntchito mankhwala ozunguza bongo, mowa, mbava, ndi ena ndalama (ndalama za msonkho waku America) kuti aperekere umboni wabodza polimbana ndi tchalitchi chathu pamodzi ndi ine. Komanso anaopseza atolankhani achilungamo kuti asamalembe nkhani zoona zokhudza ife, ndi ntchito zabwino zomwe tchalitchi chathu chikuchita apo ayi tchalitchi cha Satana mabungwe a gestapo adzawachitira nkhanza nawonso.

Tchalitchi cha Satanachi chisaululidwe, kumbukirani, ndipo mphamvu yambiri nthawi yomweyo muigwiritse ntchito polimbana ndi anthu otsogolera anthu ena ku chipulumutso cha Mulungu kudzera mwa Mwana Wake Khristu Yesu, ndiponso polimbana ndi aliyense amene adzayelekeze kuulula za usatanazi zomwe zakhala za chinsisi kwa zaka zambiri. Dzina loti "munthu wa chiphunzitso chosavomerezeka" liyenera kuperekedwa kwa onse amene anasankhidwa ndi Mulungu kudzalalikira za ulemelero wa ndondomeko za chipulumutso ndi amene amaulula za asatana opembedza mafano. M’masiku otsiliza, matchalitchi ena onse omwe asankha uthenga wa Satana, kusiya Mawu a Mulungu, amalamuliridwa ndi atumiki a Satana omwe amadetsa maguwa awo podzala udani m’mitima ya anthu amumpingo. Atumiki a Satana amalamula matchalitchiwa kuti asamalabadire atumuki a kuwala. Atumiki a mdima amenewa amalamulanso mipingo yawo kutchula maina, kuopseza, kunyoza. Amapotoza Malembo monga Satana anachitira kwa Khristu pa Phiri la Mayesero. Mwa mwano, mphamvu kuopa kuululika, otsatira a Satana amakuwa mokwenza kuti onse ovomereza malangizo a Mulungu ndi "Odana ndi anzawo" ndipo kuti ayikidwe ku malo a anthu odwala misala. Malingana ndi Malembo, Satana ndi omutsatila ake ndiwo ali a misala podziyika mu ndende yawo ya misala mpaka muyaya  mu Gehena wa moto.

Zaka zambiri zonse zimene ntchito za ukamberembere za Satana zakhala mosamala, mwa chinsisi, mwa nthawi imodzi zaonongedwa pamene atumiki a Mulungu abwera mu mzinda.  Magetsi achuluka mphamvu chifukwa mdani wa Satana wafika, ndipo asakhulupilire kalikonse pa zauthengawu. Ndi chifukwa chake, nkhani za utambwalizi zikuyenera kunenedwa, ndiponso zinthu zonse za mmene Satana alili, Satana atsutse mwana wa Mulungu wa kukhala. Ayenera kuchita izi poteteza chinsisi cha zolinga zake zaupandu pa munthu. Bodza, maonekedwe a chinyengo a tchalitchi chake, zikuphwasulidwa tsopano, ndipo mwa njira ili yonse izi sizingachitike. Anthu adzatha kuona kuseri, ku zipinda zovalira, khalidwe loipa, ukatangale; chonyasa choipa chili chonse chomwe Mulungu amanena kuti chili mwa iye.

Ulamuliro m’dziko lonse wa kufalitsa nkhani ndi imodzi mwa njira zomwe tchalitchi cha Satana chimagwiritsa ntchito poyipitsa mbiri ndi kulemba zoipa za mtumiki wa Mulungu mokwanira. A Khristu onse otsatira malamulo a Mulungu ayenera kuonongedwa, Ayuda ayenera kuonongedwa, chifukwa ndi kudzera mwa Ayuda kuti dongosolo la chipulumutso, dongosolo la kuombola kwa Mulungu, likhanzikitsidwe kudzera mwa Yesu Khristu. M’yuda woyamba anali Abrahamu, kenako Izeki ndi Jakobo, wochokera kwa Jesse, Nyumba ya Davide, ndipo pamapeto Yesu, Amene ali Mkango wa mtundu wa Ayuda.

Ku Germany, Satana anaonetsa kuipa mtima kwake kwa thupi la Izraeli pakupha Ayuda 6 miliyoni. Kuseri, ulamuliro unaperekedwa kuchokera ku tchalitchi cha Satana ku Rome, kupita ku dziko limeneli lomwe linalandira ndalama zambiri kuchokera ku mabanki a tchalitchi cha Satana ndi maboma a mabungwe a Satana mu ndondomeko za malangizo kudzachotsa chikumbutso chomwecho cha thupi chomwe njira yokhayo yopitira Kumwamba, choonadi chokhacho chomwe chili pa dziko pano ngakhalenso Kumwamba, pakuti mwa Khristu mokha ndi momwe muli moyo. Kuyesera kwa Satana pakuzunza ndi kuononga Ayuda kumakumbutsa m’mbuyomu kwa zaka mahandiredi ambiri. Ndime zambiri m’baibulo zikhonza kupezeka zokhudzana ndi zinsisi, maudani opanda pake a Ayuda, komanso kuyesera kutheratu onse mtundu umenewu. Lero, Mulungu amagwiritsa ntchito mtundu wa Ayuda pa ndondomeko ya nthawi Yake pofuna kutionetsa chifupi chomwe tili nacho ndi kubwera kwa Khristu. Chizindikiro chimodzi chinali choti M’yuda adzabwenzeretsedwa ku dziko lake, Israeli. Ayuda ena adzabwelera kwa Mulungu kudzera mwa Yesu Khristu pakulandira ndondomeko ya chipulumutso Chake ndipo kenako adzalalikira za Mawu a Mulungu, ndondomeko za chipulumutso ku dziko lapansi. Ayuda enafe tikuchita zomwezo panopa. A Khristu a Hebri, akupitilizabe kunyozedwa ndi mfumu ya mdima chifukwa choti analandira ndondomeko za chipulumutso cha Mulungu kudzera mwa Yesu Khristu Ambuye ndi Mpulumutsi wathu. Ndipo chifukwa ndi mtundu wa Israeli komanso ndi nthawi yomweyo ndi mwana wa Mulungu wa Moyo. Mfundo zonsezi zikupezeka mu Chipangano Chakale ndi Chatsopano mu Baibulo lakale la King James Version, osati latsopano lomwe olemba analemba "mothandizidwa." Satana walowelera m’mabuku ena popitiriza kusokoneza ndi kuyesa kusintha kukula kwa Mawu a Mulungu kusiyana ndi mmene ziliri mubukhu loyambilira la King James Version.

Kupinda pang’ono kapena kusintha pang’ono Mawu, umboni wa choonadi cha Mulungu, ndi zachikhalidwe chabwino cholondola cha Mawu a Mulungu ndi zomwe zimafunika kuti asinthe mtundu onse wa dziko kuti ukhale mbuli zakupha ngati Satana, mtundu umene uli omvera Mawu a Mulungu (kudziwa bwino Malembo) sungalolere kupanga zophana, kunama, kapena kuzunza anthu chifukwa chosiyana chipembedzo kapena chifukwa chili chonse. Mulungu sanapeleke chilolezo chosintha kapena kupinda Mawu Ake. Ngati munthu, mzinda, kapena maboma akana Mawu a Mulungu, malamulo oona a Mulungu amapereka ulamuliro kwa anthu Ake kuti "sasani fumbi m’mapazi anu" (Mateyu 10:14), kutembenuza tsaya lina ndi kupereka moyo wanu kwa wina, kuti Mulungu alemekezeke. "Ndipo yemwe sadzakulandirani inu, kapena kusamva mawu anu, pamene muli kutuluka kumeneko, sasani fumbi mapazi anu kuti ukhale umboni wa kwa iwo. Indetu ndinena kwa inu, kuti patsiku la chiweruzo, mlandu wa Sodom ndi Gomora udzachepa kuposa wa mzinda umenewo." (Marko 6:11), poti lero tili ndi Chipangano Chatsopano komanso Chipangano Chakale.

Utunthu wa Mawu a Mulungu (kuchoka ku Genesis mpaka Chivumbulutso) umaonetsa chithunzi chonse cha Yesu, chaukadaulo, ndiponso chokongola molapitsa komanso zolinga Zake (utumiki). Fanizo lonse komanso la ukadaulo lomwe limapereka umboni wa uchimo kosatha ndi kuipitsa limapezekanso ndi otsatira Satana, tchalitchi chake ndi zolinga zake (utumiki), nyumba yake ya ukaidi ya mizimu ya anthu otayika.

Maulosi oposa 300 oona za kubwera kwa Khristu pa dziko lapansi kudzaombola mtundu wa anthu kuchoka ku Gehena wosatha wa Satana akhonza kupezeka ndi aliyense wofufuza Malemba. Khristu amadziwa za ndondomeko ya chipulumutso bwino—Iye pamodzi ndi Atate Ake anayikhanzikitsa ndi kugwirizana kuti panalibenso njira imene ikadalowa m’malo mwake. Mawu a Mulungu (Khristu) analenga zonse za Kumwamba ndi dziko lapansi, kuphatikizanso Kumwamba komweko, dziko lapansi lomwe tikukhalali ndi Nyanja zikuluzikulu. Analenga munthu ndi kupepelera mpweya m’mphuno mwake. Analenga munthu yekha (Amuna ndi akazi) mizimu ya moyo, ndipo Mawu a Mulungu anati: "Palibe chipulumutso mwa wina aliyense; pakuti palibe dzina lina pansi pa Thambo la Kumwamba, lapatsidwa mwa anthu lomwe lidzapulumutse ife" (Machitidwe 4:12). Dzina la Mpulumutsi ndi Yesu, ndipo anabadwa ndi kumwalira tsiku lenileni lomwe mneneri Danieli ananena kuti Mesiya, Mpulumutsi, adzabadwa ndipo adzafa. Anabadwira ku Bethlehemu yaku Yudea, komwe Mpulumutsi anabadwira, monga analosera. Anabadwa kwa mzimayi osadziwa mwamuna, kubadwa mwa Mzimu Woyera chimodzimodzi mmene m’Khristu wobadwadi mwatsopano amalandilira Khristu mwa Mzimu Woyera pamene Iye (Yesu) aitanidwa kulowa mumtima mwake. Zoipa za machimo zidzatsukidwa pomwepo pamene munthu wa chikhulupiliro, akhulupilira mopanda chikaiko kuti ndondomeko za Mulungu pa chipulumutso, mwazi wotsuka-moyo kuchoka m’misempha ya Muomboli, ndiwokwanira kuwafafaniza ngakhale tchimo lingaipe kapena kukula bwanji. Ndondomeko za chipulumutso cha ulemelero, Muomboli wa ulemelero, kudzamasula mizimu ya wanthu kuchoka munyumba za ndende za Satana. "Ndipo mudzazindikira choonadi, ndipo choonadi chidzakumasulani" (Yohane 8:32). Oh, chisangalalo cha kukhululukidwa kwa machimo!! Oh, chisangalalo cha kudziwa kuti ndi mwazi wokhawo unamasula!! Uthenga wa mphamvuwu ukupezekabe wa moyo kwambiri mu nthawi ya kale komanso ndikukhala munthawi ino Mawu amene ali a moyo dzulo, lero ndi nthawi zosatha (Ahebri 13:8) mu Baibulo la King James Version (osalisokoneza, osalipindapinda kapena kutembenuza).

Mawu a Mulungu ndi madzi a moyo ku miyoyo ya azibambo ndi azimayi. Yesu anati, "Tsopano ndinu oyera kudzera ku Mawu amene ndalankhula kwa inu [osapindika, osatembenuzidwa]" (Yohane 15:3). Osapindidwa mpang’ono pomwe, osatembenuzidwa mpang’ono pomwe, koma kukhala mwa dongosolo, Mawu a Mulungu oyeretsa olembedwa mwa Mzimu Woyera kuchoka Kumwamba ndi mu mwazi wa Yesu.
Mawu a Mulungu amatsuka ziphunzitso zabodza m’moyo wa munthu, Mawu a moyo ndi osapindidwa amatsuka maudani onse ndi zisokonezo zochitika chifukwa cha chiweruzo zomwe zimaikidwa m’maganizo ndi mumtima wa munthu ndi ziphunzitso zabodza za ntchito za Satana (tchalitchi chake ndi maboma ake). Ziphunzitso za bodza za ulesi ndi kusakhanzikika kudzatsukidwa kuchoka mwa munthu. Madzi a moyo osapindidwa, osatembenuzidwa a Ambuye amatiuza kuti Mulungu amadana ndi mdierekezi, tchalitchi cha mdierekezi, ndinso ana osalapa a mdierekezi. Ana a mdierekezi ndi onse amene amadana ndi dongosolo la Mulungu, Mawu osapindidwa, osatembenuzidwa, madzi a moyo oyeretsa ochoka ku mpando wa Mulungu Kumwamba. Madzi oyera a moyo osapindidwa, Mawu a Mulungu owona osatembenuzidwa amanena kuti onse amene sakhulupilira Mawu Ake (adongosolo, osapindidwa komanso osatembenuzidwa) adzalangidwa, koma onse okhulupilira ndi obatizidwa adzapulumutsidwa. Awa ndi mawu amene anayankhulidwa kuchokera ku dongosolo la Mawu a Yesu pamene amalankhula kwa ophunzira Ake (okhulupilira Ake ndi omutsatira Iye): "Iye wakumva ndi wakubatizidwa adzapulumutsidwa; koma iye osakhulupilira adzalangidwa." (Marko 16:16).
Yesu ananena kuti Iye amadana ndi zochita za a Nikolai, opembedza mafano, ndipo nali Lembo losapindika, losatembenuzidwa lokhudzana ndi dongosolo Lake: "Kotero uli nawo ogwira ntchito za a Nikolai momwemonso [a Khristu onama osatsata mawu ndi opembedza mafano] zomwe NDIMADANA nazo" (Chivumbulutso 2:15).

Yesu amadana ndi kupinda komanso kutembenuza dongosolo la Mawu Ake, ngakhalenso zikhulupiliro zabodza zomwe sizioneka mu Mawu Ake, kapena zipembedzo za bodza, zipembedzo za mafano zomwe Mulungu amazitchula kuti ziphunzitso zopanda pake. Mtumwi Paulo akutichenjeza kuti tisalandire ziphunzitso zochokera kwa angelo a Kumwamba kapena kuchokera kwa aliyense, koma tikulangizidwa ndi Paulo m’malo mwake kuti tiziwerenga ndi kulandira okhawo enieni, Mawu a Mulungu. Pali mawu enieni, a dongosolo, osapindidwa, osatembenuzidwa ochokera kwa M’yuda Mtumwi Paulo Oyera: "Koma ngakhale ife (Atumwi Oyera), kapena mngelo ochokera Kumwamba, akulalikirani uthenga wabwino ulionse osati umene tidakulalikirani, iye akhale otembeleredwa" (Agalatiya 1:8). Mtumwi Paulo ananenanso kuti: "Lalikirani Mawu [a dongosolo, osapindidwa ndi osatembenuzidwa]" (2 Timoteo 4:2). Mtumwi Paulo anapitiriza, "Pakuti nthawi idzafika [masiku otsiriza...panopa] imene iwo sadzapilira chiphunzitso chomveka [Mawu a Mulungu monga mmene analembedwera mwa dongosolo ndi Mzimu Woyera kuchoka ku mpando wa chifumu wa Mulungu, opanda kupinda kapena kutembenuza kali konse]; koma pakutha pa zikhumbokhumbo zawo adzazikundikira iwo okha aphunzitsi" [aphunzitsi ndi alaliki abodza, zipembedzo zolakwika zopanda mawu ndi abusa abodza achi Khristu] amene amadana ndi Mawu a Mulungu oona ndi ana a Mulungu (2 Timoteo 4:3). Atumiki a Mulungu amayalutsa Satana, tchalitchi cha Satana, boma la Satana, ndi nthambi zake zonse. Atumiki a Mulungu amakana kupinda kapena kutembenuza Mawu a Mulungu kapena kukambirana ndi mdierekezi, tchalitchi cha mdierekezi, boma lake, kapena ana ake, amene ali aphunzitsi abodza, ana otembeleredwa. "Mitambo yopanda madzi, yotengeka ndi mphepo [ziphunzitso za usatana zabodza kutsogozana]; mitengo imene zipatso zake zifota [mtengo wa mtundu umenewu ndi m’Khristu wabodza, chifukwa miyoyo imene amaphunzitsa amaphunzitsidwa ndi chiphunzitso chabodza] yopanda zipatso, yofa kawiri, yozuka mizu" (Yuda 12) imene mathero ake afanana ndi a tate wao mdierekezi—kupsa ku Gehena mpaka muyaya. Iwo "amanyoza ufumu [lamulo la Mulungu losapindika ndi losatembenuzika...Mawu Ake, ufumu wa boma la Mulungu], ndikulankhula zoipa za maulemelero [anthu oyera a Mulungu amene akufalitsa Mawu Ake lero]" (Yuda 8).

Inde, Satana amafuna tchalitchi chake, tchalitchi chimene chimaononga Mawu a Mulungu, chimene chimawapotoza ndi kuwatembenuza ndi kugwiritsa ntchito Mawu a Mulungu polimbana ndi azibambo ndi azimai oyera mitima a Mulungu amene atumidwa ndi Mulungu kudzalongosola Mawu a Mulungu (kuphatikiza Satana, tchalitchi cha Satana, ndi ulamuliro wa boma m’dziko lonse lapansi wa Satana). Ife a Khristu tisagwirizane ndi mphamvu za boma la tchalitchi cha usatanachi chifukwa mphamvu zake ndizochokera pa zikhulupiliro zabodza za kufooka kwa Satana. Mawu osapotozeka a Mulungu akuti: "Anthu onse amvere MAULAMULIRO A AKULU. Pakuti palibe ulamuliro wina koma ochokera kwa Mulungu: [mphamvu yeniyeni, mphamvu yosatha] mphamvu zomwe zilipo ziikidwa ndi Mulungu.

"Kotero kuti iye amene atsutsana nao ulamuliro, akaniza choikika ndi Mulungu: ndipo iwo akukaniza adzadzitengera chilango. [Mulungu anakhanzikitsa atumiki a Mulungu kuti akachite lamulo Lake padziko lapansi. Amawatcha atumiki Ake atsogoleri. Atumiki a Mulungu akuyenera kutsogolera mwa dongosolo, ndi Mawu Ake okha.] Pakuti mafumu sakhala oopsa ku ntchito zabwino, [dongosolo la Mawu a Mulungu] koma ku zoipa. Kodi tsono simudzaopa ulamuliro? [Iwo amene ali ndi dongosolo la Mawu a Mulungu] chitani chabwino [lalikirani ndi kuchita Mawu a Mulungu]; ndipo udzalandira matamando omwewo: Pakuti iye [mphamvu zoyikidwa ndi Mulungu ya padziko lapansi] ndiye mtumiki wa Mulungu kuchitira iwe zabwino" (Aroma 13:1-4). Satana wapotoza Malembo amenewa kuti azikhala ngati tchalitchi cha Satana ndi boma la Satana ndi nthambi zake, koma izi ndi zoipa. Vesi 4 ndi 5, chaputara 13 cha Aroma akuti: "Koma ngati uchita choipa, chita mantha: pakuti iye [mtumiki wa Mulungu, mphamvu za Mulungu zokhala padziko lapansi] sagwira lupanga [dongosolo la Mawu a Mulungu], pachabe: Pakuti ndi mtumiki wa Mulungu, wakukwiyira ndi kubwenzera chilango, kwa iye wochita zoipa. Chifukwa chake muyenera kukhala omvera osati chifukwa cha mkwiyo wokha [ngati ulakwila dongosolo la Mawu a Mulungu], komanso chifukwa cha chikumbumtima."

"Kotero, chifukwa cha ichi muperekanso msonkho [perekani zakhumi ndi zopereka zanu kwa iwo, osati ku tchalitchi cha Satana], chifukwa iwo ndiwo atumiki a Mulungu, akulabadira chinthu chimenechi [dongosolo la Mawu a Mulungu]. Perekani kwa anthu onse mangawa awo" (Aroma 13:6-7). "Osakhala ndi ngongole ndi munthu" (Aroma 13:8,) koma sungani malamulo, kutanthauza kondani wina ndi mzake. Chikondi ndi kusunga malamulo a Mulungu. Mukhonza kuona nokha kuti antchito oipa a dziko lino ochokera m’tchalitchi ndi boma za Satana atembenuza Malembowa ndipo anamiza dziko (chifukwa dziko silidziwa Baibulo) komabe, dongosolo la Malembowa likuonetsa kuti Satana ndi ofooka ndipo atumiki a Mulungu ndiwo mphamvu za Mulungu pa dziko lapansi, ndikuti aliyense azikhala pansi pa mphamvu. Satana alibe mphamvu. Sangapereke moyo; sangaukitse akufa; sangachiritse; iye ndi wakufa. Mulibe mphamvu mu imfa; iye ndi mfumu ya imfa (Ahebri 2:14). Mzimu womwewo uli mwa zochita za mdierekezi pa dziko lapansi lero. Iwo amene atembenuza mawu mokomera iwo amachitiranso chomwecho Khristu Mwini (Yemwe ali Mawu a Mulungu), ndipo Iye anakhomedwa pa mtanda chifukwa chakutembenuza mwabodza Mawu a Mulungu.

Pamene ola likuyandikira lakudza kwachiwiri kwa Yesu, Satana apangitsa zinthu kuvuta kwambiri padziko lapansi. Izi akuchita ndi cholinga choonjezera chisokonezo chomwe chilipo kale, chifukwa akudziwa Malembo amene akunena kuti atumiki oyera a Mulungu adzamuika iye poyera pamodzi ndi ntchito zake Yesu atatsala pang’ono kubweranso pa dziko lapansi. Moyesetsa Satana wachenjeza atumiki ake onse, chifukwa ola lake lafika. Zinsisi za papa sizinsisiso ayi. Ndipo iyi ndi ngozi kwa iye, ndi onse omutsatira ake. Kwa nthawi yaitali chiwembu chake, chiwembu cha tchalitchi lake mothandizidwa ndi ulamuliro wa boma, ndi iye mwini zinali zinsisi, koma pano zaululika. Ambiri amene anapusitsidwa m’tchalitchi chake panopa ayamba kuona bwinobwino kuwala ndi kukhala, ndipo akupanga ulendo wao panopa kutuluka m’chipembedzo chake chabodza ndikukalowa mu dongosolo la Mawu a Mulungu (Thupi la Khristu). Anasokonezedwa, koma pano salinso osokonezeka. Mitima yawo ili ya chimwemwe pamene Khristu walowamo, ndipo panopa akuyenda mwa Iye, asilikali a Khristu. Tsopano akudziwa Mawu a Mulungu ali ndi moyo, chifukwa anawachotsa iwo ku imfa kupita ku moyo wosatha.

Mawu a Mulungu ndi Yesu. Satana akusonkhanitsa pamodzi asilikali ake a anthu opanda mphamvu, amene akana choonadi ndi kuwala, koma kusankha mdima, imfa, ndi Gehena zimene zidakali m’tchalitchi cha Satana. Amasonkhana limodzi kuchita nkhondo kulimbana ndi Mulungu wa Mphamvu ndi oyera mtima Ake. Yesu anati Iyenso adzachita nkhondo (Chivumbulutso 19:11). Unyinji, unyinji waima m’chigwa cha chisankho chawo (Yoweli 3:14). Tsopano ndi nthawi yosankha mbali. Amantha ndi osakhulupilira adzakhala mu Gehena kwa muyaya (Chivumbulutso 21:8). Koma olungama alimba mtima ngati mikango (Miyambo 28:1) ndipo adzawala ngati nyenyezi (Danieli 12:3). Olungamafe tili ndi chikhulupiliro kuti Yesu apambana, ndipo Satana akudziwanso zimenezo, pakuti kunalembedwa iye akudziwa kuti nthawi yake ndi yochepa (Chivumbulutso 12:12) "...mdierekezi, monga mkango wobuma, ayendayenda ndi kufunafuna wina akamlikwire" (1 Petro 5:8).

Ambuye, kudzera mwa Mtumwi Paulo, anati: "Mulungu atumiza kwa iwo machitidwe akusocheretsa, kuti akhulupilire bodza: kuti aweruzidwe onse amene sanakhulupilire choonadi, koma anakondwera ndi chosalungama. [Chili chonse chotsutsana ndi dongosolo loona la Mawu a Mulungu]" (2 Atesalonika 2:11-12).

Machitidwe akusocheretsa amene Mulungu anawapatsa (chifukwa chokhala mwabodza) anapangitsa kukhala ochepa mphamvu (kupusa kuposa kale) kuti amenyane ndi Wamphamvu, kuti aweruzidwe. Adzaonongedwa ndi kuwala kwa kudza Kwake (2 Atesalonika 2:8).

Mtumwi Paulo anati, monga timachitira, kuti Ambuye akubweranso pa dziko lapansi, koma osati kasanafike koyamba kawo ndi kugwa kwa choonadi, Mawu Ake. Mtumwi Paulo ananenanso kuti Yesu sadzabweranso mpaka "kuti munthu wa kuipa avumbulutsike, mwana wa chionongeko" (2 Atesalonika 2:3). "Amene atsutsana nazo nadzikuza pa zonse zotchedwa Mulungu, kapena zopembedzeka; kuti iye monga Mulungu wakhala pansi m’kachisi wa Mulungu, nadzionetsera yekha kuti ali Mulungu" (2 Atesalonika 2:4). Yesu, kudzera mu utumiki wathu, akuulula Satana, tchalitchi chake, ndi boma lake lero, ndipo a Khristu onamizira akutida chifukwa cha ichi, chifukwa tikuwaululanso kuti ndi onamizira, ndi mulungu wao onamizira ku Rome amene amadzitamandira ndi kudziika iye mwini kuposa Mulungu, ndipo tchalitchi chake komanso boma lake zonamizira zimene Satana amafuna kuti anamize dziko lapansi (Chivumbulutso 12:9). Zimene anapanga, Mulungu anati adzapanga m’mabuku a Chivumbulutso, Danieli, 2 Tesalonika, Mateyu, komanso Baibulo lonse.
Ngati mumaonera nkhani mudzaona kuti tchalitchi cha Satana ndi boma lake zimadzionetsera zokha masiku ano, ndipo ngati mumadziwa Baibulo mukhonza kuona kudzionetsera uku bwinobwinonso. Baibulo limati kuti mitundu yonse idzaphatikizana ndi kupereka mphamvu kwa mdierekezi ndi tchalitchi chake (Chivumbulutso 17:2). Wa Katolika waku Ireland Ronald Reagan (mwachinyengo otchedwa Dutch) wathandiza kukwaniritsa Malembo amenewo pakuika mthumwi ya chitaganya mopanda chilolezo (mosatsata malamulo) m’zipinda za Vatican za mneneri wachinyengo. Ronald Reagan, motsatira lumbiro la Yesuit, (moyenelera) wakhala Oukira pakati pa Oukira mpaka zonse zitatheka monga mwa Malembo.

Apa pali imodzi mwa zofotokoza zambiri zimene Ronald Reagan anafotokoka pa kutamanda maubale ake ndi tchalitchi-boma za usatana komanso mulungu wake papa. "Ndikuthokoza chifukwa cha thandizo lanu pakupanga ndondomeko ya America kuonetsa zolinga za papa [mulungu wa Reagan], "ndipo ndiyembekezera kutsogoleredwabe ndi iye oyera, Papa Yohane Paulo Wachiwiri." Mauwa akuchokera pa zokamba zimene zinaperekedwa ku National Catholic Educational Institute pa 15 April, 1982. Oyang’anira onse a Reagan ndi atchalitchi cha Roma Katolika (tchalitchi cha Satana). Izi ndizodziwika ndipo zakhala zikuulutsidwa ndi masauzande pa kanema, pa wailesi, komanso m’manyuzipepala. Ziyerekezo za maumboni anayi pa zimenezi akhonza kupezeka m’magazini a Church and State mu nkhani yolembedwa ndi Albert Menendez mutu wake: "Of Presidents and Popes," June, 1982. The National Catholic Reporter ndi Congressional Quarterly ndi ena mwa ofalitsa nkhani za mfundo zokhumudwitsazi.

Reagan ananenanso zotsatirazi ku Catholic Knights of Columbus Convention, zimene analankhula pa 6 August, 1986:

"Ndili osangalala kukuuzani [abale a Katolika] kuti ndasankha kale majaji a chitaganya—azibambo ndi azimai amene zikhulupiliro zawo zili zofanana ndi zanu komanso zanga zimene timakonda [Katolika], ndipo kuti pomadzasiya ofesi, oyang’anira athu adzakhala atasankha 45% ya majaji onse… Kwenikweni ndinali osangalala chifukwa monga ena mwa inu mukudziwa, Jaji Scalia ndi Italian American woyamba kusankhidwa kupita ku Khoti la Supreme."

Majasitisi a Khoti la Supreme amene Reagan wasankha posachedwapa onse ndi a Roma Katolika (tchalitchi cha Satana). Senate ndi House of Representatives onse ndi a Roma Katolika (tchalitchi cha Satana) ndiponso/kapena ochitira chifundo Roma Katolika, ndipo amene akunola policy ya America, Reagan akuti, ndi Papa Yohane Paulo Wachiwiri (mtsogoleri wa gulu la afiti la tchalitchi cha Satana).
Ronald Reagan waphwanya Malamulo athu U.S. a umulungu mokomera lamulo la Roman Canon (lamulo la Satana), ndipo malingana ndi lamulo lokana za uzimu (Malamulo a U.S. aumulungu) achotsedwe ndi oyang’anira ake onse mosachedwetsa, ngati tikufuna kusangalatsa Mulungu ndi kubwelera m’chisomo Chake ndikupulumuka Gehena wa muyaya.

Magawo onse abwino ndi enieni a kayendetsedwe ka boma ndi bwalo la milandu (judicial system) a dziko lathu kuphatikizapo mizinda ing’onoing’ono, analekeleredwa, kugwira moyo, anatailiridwa, kuonongeka bongo, kuonongedwa, kukhumudwitsidwa, kusalabadilidwa, kupusitsidwa, kunamizidwa, kuoletsedwa, kusinthidwa, ndi kutsala pang’ono kuphedwa (pafupifupi kufa) chifukwa cha mpukutu wa makape ausatana opanda mphamvuwa amene amapereka mphamvu ku tchalitchi cha Satana, ndipo aliyense wangoima osapanga kali konse pamene ofalitsa uthenga a Vatican boma lonse ndi dziko lonse ali pa kalikiliki kuchita mabodza awo ndipo achiwembu ake ena onse amatenga mbali kuchita ntchito zawo zoipa. Tchalitchi cha Satana mwansangansanga chinalembetsa mabungwe ake owona za malamulo (kutchulidwa monama) mosavomerezeka; mosatsata malamulo anamanga amene Mulungu anatimiza kukalalika choonadi cha Mulungu chimene chimaulula zinsisi za tchalitchi cha Satana pamodzi ndi boma lake. Izi ndizotsutsana ngakhale ndi lamulo la zauzimu (ufulu olankhula, ufulu wa chipembedzo, ufulu wa nkhani). Satana samakondwera nazo zimenezi…sangakhale wamakonso pano. Makono ndikupanda nzeru!!

Anthu a Satana kulira "Siyani izi mwa njira ili yonse, akutiulula!!" Tipange malamulo ena atsopano otsutsana ndi ufulu wa mayankhulidwe ndi ufulu wolemba nkhani… Tiyitchula "GENOCIDE"!! Amangeni onse monga momwe tate wathu mdierekezi anamangira Yesu zaka 2000 zapitazo ndipo kwa zaka zambiri zisanachitike komanso zitachitika zimenezo anamanga aneneri ndi atumwi. Amangeni ndi kuthandizika!! Kagwereni uko ndi malamulo a U.S.!! Gwejemulirani m’mapaipi!! Kagwereni uko ndi lamulo la America!! Litayeni pa windo!! Kenako muliotche!! Ngati oona malamulo sangatero, tilemba asilikali athu omvera ife monga momwe tinapangira ku Germany, SS ndi Gestapo, pamene tinapanga mu Ayuda!! Satana akupitilirabe kusokosera. Kodi America ikhalebe ya Roma Katolika? Sitikuyenera kuchedwetsa pa bwalo la chiweruzo la Mulungu chifukwa cha unyolo wake pano kapena unyolo wosatha mu Gehena.

Zolembedwa zokhudzana ndi mbiri imene siyingachotsedwe, osanena kanthu za chitsanzo choopsa cha Latin America nthawi imeneyo, Spain, Ireland, Italy ndipo pano dziko lonse, chikutiwunikira kuti cholinga cha Rome chanenedwa bwinobwino, ndikuti njira zake zokwanitsira zolinga zake sizobisika (ulamuliro wa miyoyo ya amuna, ulamuliro wa dziko lapansi, komanso kupezeka bwinobwino mu Mawu a Mulungu). Apa pali zolemba kuchokera ku Malumbiro ama Yesuit a Katolika (Catholic Jesuit Oath):

"Mwana wanga wa mwamuna wa Katolika, isanafike nthawi ino wakhala ukuphunzitsidwa kukhala opusitsa: Pakati pa a Roma Katolika kukhala wa Roma Katolika, ndi kukhala kazitape ngakhale pakati pa abale ako enieni; osakhulupilira munthu, pakati pa wokonza, kukhala wokonza; pakati pa woukira, kukhala woukira; pakati pa wosintha zikhulupiliro (Calvinists), kukhala wosintha zikhulupiliro; pakati pa Wotsutsa, kukhala Wotsutsa; ndi kusunga chinsisi chawo ndi cholinga chofuna kufanana nawo kulalikira pa magome awo ndi kuipitsa mphamvu zanu zonse za chisawawa chipembedzo chathu choyera ndi papa; Ndiponso kudzichepetsa kukhala ngati m’Yuda pakati pa aYuda, kuti muzikwanitsa kusonkhanitsa mfundo zonse mokomela inu ngati msilikali wokhulupilika wa papa. Munaphunzitsidwa kudzala njere ya nsanje mkatikati ndi udani pakati pa maboma amene anali pa mtendere ndi kuwakhuwuzira kuti aziphana."

Nkhaniyi ikhonza kupezeka mu Laiburare ya Kongeresi m’bukhu lotchedwa, The Engineer Corps of Hell lolembedwa ndi Edwin A. Sherman, ndipo lilinso mu Congressional Record. Ndipo kumbukirani kuti maprezidenti, magavanala, majaji ndi maofesala onse a boma a Katolika amene amalumbilira izi amayenera kukhulupilika kaye ku tchalitchi cha Katolika. Umbuli oipitsitsiratu m’dziko ndikusalabadira Mawu a Moyo a Mulungu. Pamene simukudziwa za Baibulo, mumapunthwa mumdima ngati mzibambo kapena mzimai wakhungu (Yohane 12:35) chifukwa simungaone kumene mukupita. Mabiliyoni anali ndi moyo ndipo anafa osapindula ndipo ali ku Gehena, osati kuti akangodziwa mmene kuliri kenako ndikupita kwinanso, koma kukakhala mpaka muyaya m’nyanja ya moto m’dzenje limene silingathe. Kudzakhala kulira ndi kukuta mano mpaka muyaya (Mateyu 8:12). Ngati anthu ochuluka amene salabadira Baibulo amadziwa Mawu a Mulungu akuyenera kudziwa monga ndidziwira kuti Satana amafuna tchalitchi chake ndipo kuti tchalitchi chake chimafuna mphamvu zolamula kuti chithetse matchalitchi ena ndikudzitukula. Satana poyambilira akukonza mopusitsa maboma onse amene ali pansi pa ulamuliro wake (United Nations).  Izi zikuchitika mwakachetechete, modekha, mwa chinsisi ndi otsatira amene ali nganganga pa lumbiro kuti sangaiwale zofuna za mtsogoleri wao woipa.

America ikuyenera kugwiridwa mwa nzeru zapadera komanso mwa chinsinsi, chifukwa dziko ili linapezeka pa chinthu chimene chimamupangitsa Satana kuona kufiira. Chinthucho ndi "Mwa Mulungu Tikhulupilira," chimene chinapezeka pa mwala wolimba Khristu Yesu, Mawu a Mulungu, chimene ogwira ntchito ku tchalitchi ndi boma za Satana amadana nacho. Amatipangitsa kukhulupilira kuti dziko ili linapezedwa pa Chiboliboli cha Ufulu… (Statue of Liberty…) si choncho ayi. Chiboliboli cha Ufulu (Statue of Liberty) inatipatsa ndi France, chifukwa achifaransa anazindikira kuti tinali ndi ufulu umene maiko ena analibe. Ufulu umenewu sunakhanzikitsidwe ndi kupezeka pa Chiboliboli cha Ufulu (Statue of Liberty) koma pa Mawu a Mulungu. Inde, anayesetsa kutembenuza tanthauzo lenileni la Ufulu mu America… "Mwa Mulungu Tikhulupilira."

Chibadwireni dziko lathu kukhulupilira mwa Mulungu, maYesuit a Satana ndi atsogoleri awo akhala akutokota nthawi zonse, "Sitingalore kuti chiKhristu chikhaleko, tipange tchalitchi mu America cha mtsogoleri wathu (Satana)… Tilowelere muzintchito za Amerika, boma lake laulere, kufalitsa nkhani kwake kwaulere, kukhanzitsa migwirizano, komanso kuchita bwino kwathu monga mwachizolowezi. Umbanda, mtudzu, katangale, chisangalalo, msangulutso, ndi mankhwala ozunguza bongo azilamulidwa ndi ife (monga mwachizolowezi dziko lonse lapansi), ndipo pomaliza tilifoole dziko la umulunguli limene chiyambi chake chili pa "Mwa Mulungu Tikhulupilira" ndipo ichi chikuima pa (osapotozedwa) Mawu a Mulungu kwathunthu, pakuchilowetsa ndi atate wathu, uthenga wa Satana (umene analalikira koyamba yekha kwa Hava m’munda wa Edeni). Tilalikira zimenezo (Mulungu samadana ndi chili chonse, Mulungu ndi chikondi, Baibulo ndi nthano, ndipo papa ndi Mulungu.) Titati tilowe m’matchalitchi onse ndi uthenga wabodzawu, tikhonza kukopa America kukhala ya tate Satana, ndipo adzatilipira bwino m’dziko lopanda umulunguli…bolani akunena kuti adzatero.Ngati tingawaletse anthu kuwerenga Baibulo kapena kuwapangitsa kuti aziwerenga limodzi mwa maBaibulo athu atsopano amakono, ndiye kuti tikhonzanso kuzipangitsa zitsiru kukhulupilira kuti Mulungu wa Makamu amakondanso tate wathu mdierekezi, kuti Iye amakonda tchimo, zoipa, katangale ndi chili chonse chimene Mulungu wanena chingatipitse ku Gehena." Koma zoona zake zenizeni ndizakuti Mulungu amamunyozetsa Satana, chifukwa chinali chifukwa cha Satana kuti Khristu abwere kudzatifera ndikupita ku Gehena kwa masiku atatu. Koma anauka kwa akufa ndipo ali wamoyo kwamuyaya. Amadana ndi machimo chifukwa Iye anakhetsa mwazi Wake kuwachotsa iwo ku moyo. Ife amene tikhulupilira ndi kuthokoza ndi kusunga malamulo Ake (Mawu a Mulungu osapotoka, olongosoka) kudziwa kuti Mulungu amadana, amanyozetsa ndipo adzalanga iwo amene amenyana Naye ndi odzodzedwa Ake (Masalimo 105:15).

Ntchito imene Mulungu analamula kuti anthu agwire padziko lapansi siinachitike. Anthu a padziko lapansi anakhumudwitsa Mulungu. Dziko lapansi lagona mu chinyengo. Ife ku Holy Alamo Christian Church tikuguba m’misonkhano ya chitsitsimutso kufikira Iye adzabwere. Satana sanalapepo ndipo sadzalapapo. Gehena wakulitsidwa chifukwa cha alaliki ake, aphunzitsi ake, iyeyo, komanso chifukwa cha onse omutsatira (Yesaya 5:14) iwe wolefula amitundu (Yesaya 14:12).

Satana amalamula, "Pakuyendetsa migwirizano tikhonza kuonjezera malipiro wogwilira ntchito, kuyika mamiliyoni a anthu aku America pa ulova ndipo mabizinesi ambiri akhonza kutsekedwa ndi kupatsa maiko ena amene timalamulira kale malipiro a ntchito osakwera ndi cholinga choti apange ntchito yabwino kuposa United States. Tikhonza kukwaniritsa zonsezi mothandizidwa ndi anthu athu amene timawadalira mu Nyumba ya Chifumu, Nthambi Yoona za Ntchito, IRS, Migwirizano, Nthambi Zoona za Zomangamanga ndi Chitetezo komanso mahandiredi a nthambi zina monga OSHA ndi mabungwe ena onse a chitaganya ndi a boma amene timayendetsa panopa.

"Tikuyenera kulamulira mabanki onse komanso Federal Reserve (ndipo panopa tikutero), ndipo kotero panopa tikhonza kungongoza ndalama kwa anthu athu ndi kusiya ena onse amene amadana ndi tate wathu mdierekezi [monga Mulungu achitira]. Ndipo tikuyenera kulamulira Nthambi ya Ulimi, ndi cholinga cholamulira minda yonse, chifukwa cha tate wathu, Satana. Izi zikutanthauza kuti tichotse alimi onse aku America pa bizinesi, chifukwa tate wathu Satana akudziwa bwino lomwe kuti Esau anagulitsa ufulu wa kubadwa chifukwa cha chakudya, ndi anthu aku America ndi chimodzimodzi anthu ena onse amene panopa tikulamulira. Opanda mphamvu ya Mulungu m’miyoyo yawo, tikhonza kuwasintha ndi chakudya, monga momwe tachitira m’maiko ena onse, chiKatolika.  Ngati angasinthike ndi kumvera, tikhonza kuwapatsa chakudya pakusinthana ndi miyoyo yawo [chakudya chochokera m’munda wao omwe].

"Tikaba minda yonse powapangitsa alimi kukhulupilira monama kuti Malamulo a U.S. ndi  amakedzana, ndiye kuti tidzatenga malo awo ndipo tidzawapatsa zinthu zaulele zochokera kwa tate wathu mdierekezi. Chifukwa panopa akumulambira, akulandira zinthu zaulele."

"Pamene alimi amalambira Mulungu ndi kukakamila pa Malamulo anali ndi malo awoawo ndipo sanafune chopatsidwa chaulele. Inali nthawi imene anali amuna, osati opembedza a Satana angati jellyfish yogobozoka-maondo. Akaima pa Mawu a Mulungu palibe amawaposa. Atumiki athu a "Mulungu ndi Chikondi" achita ntchito yotamandika. Satana wakhutitsidwa. Tsopano tiyeni tiyike chizindikiro pa iwo monga tichitira ndi ng’ombe, kuti titsimikize za kukhulupilika kwao…  Mulungu amatchula chizindikirochi "Chilembo cha Chirombo" (Chivumbulutso 19:20). Tate wathu mdierekezi samakondwera nalo dzina limenelo, kotero tidzatchula dzina lina labwino kuposa ili monga lembo la mtendere kapena ubale kapenanso kungoti chili chonse chonama ndithu. Ndipo tikuyenera kuononga Tchalitchi  Choyera cha ChiKhristu cha Alamo (Holy Alamo Christian Church), chifukwa akuzungulira kuuza aliyense zimene tikuchita ndipo kuti Mulungu adzatipititsa ku Gehena chifukwa chochita zimenezi, ndiponso akuuza aliyense kuti adzapita ku Gehena ngati adzalandire lembo lathu la ubale. Alinso ndi Malembo a Baibulo kuchitira umboni. Ndichifukwa chake tikuyenera kuwaleketsa. Tate wathu ku Rome anauza Ronnie ku Washington kuti alamule Khoti la Supreme kuponya bukhu ku Holy Alamo Christian Church. Reagan mpaka anauza a nkhani kuti Holy Alamo Christian Church alipire malipiro a anthu odzipereka kutumikira Mulungu. Izi zinalinso pa mapeto pa Holy Alamo Christian Church itapereka dabulo kapena kuposa madola 19 miliyoni m’maphindu osakhalitsa, ndipo zapangitsa aliyense m’tchalitchimo kupita ku moyo wosatha kudzera mwa Yesu Khristu Mulungu ndi Mpulumutsi wathu. Ambiri otsatira Holy Alamo Christian Church anawomboledwa ku miyoyo ya umbanda, kuba, mankhwala opusitsa (narcotics) ndi mankhwala osokoneza bongo ndipo pano ndi zitsanzo zabwino za Mulungu wa moyo kukonza madera onse a m’dziko. Zitakhala kuti anthu onse m’dziko lathu la ufulu ayamba nthawi yomweyo kumvera Baibulo monga linalembedwera, mphamvu zonse za Satana komanso ulamuliro wake ukhonza kutheratu nthawi yomweyo. United States inali yopambana chabe chifukwa inayima pa Mawu a Mulungu molimba. Makolo amene anakhanzikitsa anaonetsetsa zimenezo. Inde, Satana akufuna mabungwe a boma ake onse kumenyana ndi ana a Mulungu onse amene atsala m’dzikoli ndikutinso achotse anthu a "Mwa Mulungu Tikhulupilira" ndi malamulo a malo athu amene ife a Khristu enieni taimapo. Satana, tchalitchi chake, boma lake, ndi anthu ake ali pa nkhondo ndi "Mwa Mulungu Tikhulupilira," Lamulo la U.S.

Atsogoleri a Satana a padziko, atafoola America kudzera m’migwirizano yake, m’malonda obisa a mankhwala ozunguza bongo, m’zipinda zodikilira m’malo ochotsera pakati, m’zinthu za maliseche komanso m’ziphunzitso za chihumanism m’masukulu ndi m’mayunivesite athu akunena panopa kudzera mwa ofalitsa nkhani awo kuti Malamulo a U.S. atha ntchito ndipo ndi amakedzana. Koma Mawu a Mulungu, amene Malamulo a U.S. akuyendera, si amakedzana koma ali chimodzimodzi dzulo, lero, ndi kunthawi yosatha… "Kumwamba ndi dziko lapansi zidzatha, koma Mawu Anga sadzatha" (Mateyu 24:35) ndipo pa tsiku la chiweruzo aliyense adzaweruzidwa ndi Mawu a Mulungu. Amdierekezi onamawa amene akunena kuti Malamulo a U.S., monga mwa Mawu a Mulungu, ndi achikalekale sadzanena kuti ndi achikalekale nthawi imeneyo, koma adzalira ndi kukukuta mano awo. Yesu amatchula Satana kuti tate wa onse abodza. Kutanthauza tchalicthi chake, boma lake, ndi onse omutsatira ndi abodza. Pakupangitsa anthu kukhulupilira mabodza ake, wapangitsa dziko lino kukhala dziko la opemphetsa ngati iyeyo…Satana mwa njira ili yonse akufuna ndipo akuyenera kumvera kwa ana ake, chifukwa amaona kumvera kumene Mulungu amalandira kuchokera kwa ana a Mulungu, ndipo Satana amamuchitira nsanje kwambiri Mulungu. Kumbukirani, Satana wopemphapempha ameneyi anati,

"Ndidzakwera Kumwamba, ndidzatamanda mpando wanga wa chifumu pamwamba pa nyenyezi za Mulungu: ndidzakhalanso pamwamba pa phiri la khamu, m’malekezero a kumpoto: Ndidzakwera pamwamba pa mitambo; Ndidzafanana ndi Wam’mwambamwamba" (Yesaya 14:12-14).

Koma Mulungu akuti, "Koma udzatsitsidwa pansi ku Gehena, kumalekezero a dzenje" (Yesaya 14:15).

Ngati mutsatira utsogoleri wa Satana, mudzamutsatira ku chionongeko komanso ku Gehena wosatha ndi matembelero masiku onse a moyo wanu pa dziko lapansi; koma ngati mutsatira utsogoleri wa Mulungu, mudzakhala moyenelera, moyo wosatha ndi moyo wochuluka (Yohane 10:10) pa dziko lapansi pano, ndipo dziko lanu lidzakhala lopambana ndi lapamwamba kuposa maiko onse.

TCHALITCHI CHA SATANA SICHIMALALIKIRA IZI

1 Ndipo zidzachitikadi, mukadzamvera mawu a Ambuye Mulungu wanu mwachangu kusamalira ndi kuchita malamulo Ake onse amene ndikuuzani lero, kuti Ambuye Mulungu wanu adzakuikani inu pamwamba pa mitundu yonse ya padziko lapansi:
2 Ndipo madalitso onsewa adzabwera pa inu, ndi kukupezani, mukadzamvera mawu a Ambuye Mulungu wanu.
3 Mudzakhala odala mu mzinda, ndi odala kubwalo.
4 Zidzakhala zodala zipatso za thupi lanu, ndi zipatso za nthaka yanu, ndi zipatso za zoweta zanu, zoswana za ng’ombe zanu, ndi zoswana za nkhosa zanu.
5 Udzakhala odala mtanga wanu ndi chosungira chanu.
6 Mudzakhala odala polowa inu, ndipo mudzakhala odala potuluka inu.
7 Ambuye adzakantha adani anu akukuukirani: adzakudzerani njira imodzi, ndi kuthawa pamaso panu njira zisanu ndi ziwiri.
8 Ambuye adzalamula mdalitso pa inu m’nkhokwe zanu, ndi muzonse mutulutsirako dzanja lanu; ndipo Iye adzakudalitsa inu m’dziko limene Ambuye Mulungu wanu akupatsani.
9 Ambuye adzakukhazikirani Yekha mtundu wa anthu wopatulika, monga Iye anakulumbilirani, ngati mudzasunga malamulo a Ambuye Mulungu wanu, ndi kuyenda m’njira Zake.
10 Ndipo anthu onse padziko lapansi adzaona kuti akutchulani dzina la Ambuye; nadzakuopani.
11 Ndipo Ambuye adzakuchulukitsirani zokoma, m’zipatso za thupi lanu, ndi m’zipatso za nthaka yanu, m’dziko limene Ambuye analumbilira makolo anu kuti adzakupatsani ilo.
12 Ambuye adzakutsegulirani chuma Chake chokoma, ndicho Thambo la Kumwamba kupatsa dziko lanu mvula m’nyengo yake, ndi kudalitsa ntchito zonse za dzanja lanu: ndipo mudzakongoletsa amitundu ambiri, osakongola nokha.
13 Ndipo Ambuye adzakupangani mutu, osati mchira; ndipo mudzakhala wapamwamba pokha, ndipo simudzakhala wapansi ayi; ngati mudzamvera malamulo a Ambuye Mulungu wanu, amene ndikuuzani lero, kuwasunga ndi kuwachita:
14 Ndipo osapatukira mawu ali onse ndikuuzani lero, kudzanja la manja kapena ku lamanzere, kutsata milungu ina kuitumikira.
15 ¶ Koma kudzachitikadi, mukapanda kumvera Mawu a Ambuye Mulungu wanu, kusamalira kuchita malamulo Ake onse ndi malemba Ake amene  ndikuuzani lero; kuti matembelero onsewa adzakugwerani, ndi kukukutani:
16 Mudzakhala otembeleredwa inu mumzinda, ndi otembeleredwa pabwalo.
17 Mtanga ndi nkhokwe zanu zidzakhala zotembeleredwa.
18 Zidzakhala zotembeleredwa zipatso za thupi lanu, ndi zipatso za m’thaka yanu, zoswana za ng’ombe zanu, ndi zoswana za nkhosa zanu.
19 Mudzakhala otembereledwa polowa inu, ndipotuluka inu.
20 Ambuye adzakutumizirani temberero, chisokonezo, ndi kudzudzula, monsemo mukatulutsa dzanja lanu kuchita kanthu, kufikira mwaonongeka, kufikira mwatha msanga; chifukwa cha zochita zanu zoipa, zimene mwandisiya nazo.
21 Ambuye adzakumamatiritsani muliri, kufikira Iye akakuthani kukuchotsani kudziko, kumene mupitako kulilandira.
22 Ambuye adzakukanthani ndi nthenda yoondetsa yachifuwa, ndimalungo, ndi chibayo, ndi kutentha thupi, ndipo ndi lupanga, ndi chinsikwi, ndi chinoni; ndipo zidzakutsatani kufikira mwa tayika.
23 Ndipo thambo lanu lapamwamba pamutu panu lidzakhala ngati mkuwa, ndipo dziko lili pansi panu ngati chitsulo.
24 Ambuye adzasandulitsa mvula ya dziko lanu ikhale fumbi ndi phulusa: zidzakutsikirani kuchoka Kumwamba, kufikira mutaonongeka.
25 Ambuye adzalora adani anu akukantheni: mudzawatulukira njira imodzi, koma mudzawathawa pamaso pawo njira zisanu ndi ziwiri: ndikuchotsedwa pakati pa mafumu onse adziko lapansi.
26 Ndipo mitembo yanu idzakhala chakudya cha mbalame zonse zamlengalenga, ndi zirombo zonse za padziko lapansi, ndipo palibe wakuziingitsa.
27 Ambuye adzakukanthani ndi zirombo za ku Aigupto, ndi nthenda yotuluka m’mudzi, ndi chepere, ndi mphere, osachira nazo.
28 Ambuye adzakukanthani ndi misala, ndi khungu, ndi kuzizwa mumtima:
29 Ndipo mudzafufuza usana, monga wa khungu amafufuza mumdima, ndipo simudzapindula nazo njira zanu: ndipo mudzakhala wopsinjika ndi kukuberani masiku onse, wopanda wina wakukupulumutsani.
30 Mudzapalana ubwenzi ndi mkazi, ndipo mwamuna wina adzagona naye: mudzamanga nyumba, osakhala m’mwemo: mudzaoka m’munda wa mphesa, osalawa zipatso zake.
31 Adzapha ng’ombe yanu pamaso panu, osadyako inu: adzalanda bulu wanu molimbana pamaso panu, osakubwenzerani: adzapereka nkhosa zanu kwa adani anu, wopanda wina wakukupulumutsirani.
32 Adzapeleka ana anu amuna ndi akazi adzaperekedwa kwa anthu a mtundu wina, ndipo m’maso mwanu mudzada ndi kupenyelera, powalilira tsiku lonse: ndipo simudzakhala mphamvu m’dzanja lanu.
33 Mtundu wa anthu amene simudziwa, udzadya zipatso za nthaka yanu, ndi ntchito zanu zonse; ndipo mudzakhala wopsinjika ndi wophwanyika masiku onse;
34 Nimudzakhala oyeruka chifukwa cha chomwe muchiona ndi maso anu.
35 Ambuye adzakukanthani ndi chironda choipa chosachira nacho ku maondo, ndi ku miyendo, kuyambira pansi pa phazi lanu kufikira pamwamba pa mutu wanu.
36 Ambuye adzamukitsa inu, ndi mfumu yanu imene mudzadziikira, kwa mtundu wa anthu umene simudziwa, inu kapena makolo anu; ndipo mudzatumikirako milungu ina, mitengo ndi miyala.
37 Ndipo mudzakhala chodabwitsa, ndi nkhani, ndi nthanthi, mwa mitundu yonse ya anthu amene Ambuye akutsogoleraniko.
38 Mudzatuluka nazo mbewu zambiri kumunda, koma mudzakolora pang’ono; popeza dzombe lidzadya.
39 Mudzaoka minda ya mphesa, ndi kuilima, koma osamwa vinyo wake, kapena kukolora mphesa zake; popeza mbozi zidzaidya.
40 Mudzakhala nayo mitengo ya azitona m’malire anu onse, osadzola mafuta; popeza zipatso za mitengo ya azitona zidzapululuka.
41 Mudzabala ana amuna ndi akazi, koma osakhala nawo; popeza adzalowa ukapolo.
42 Mitengo yanu yonse ndi zipatso za nthaka yanu zidzadyedwa ndi dzombe.
43 Mlendo wokhala pakati panu adzakulirakulira inu, koma inu mudzacheperachepera.
44 Iye adzakukongozani, ndipo inu osamkongoza: iye adzakhala mutu, ndipo inu mudzakhala mchira.
45 ¶ Ndipo matembelero awa onse adzakugwerani, nadzakulondolani, ndikukhala nanu, kufikira mutaonongeka; popeza simunamvera mawu a Ambuye Mulungu wanu, kusunga malamulo Ake ndi malemba Ake amene Iye anakulamulirani:
46 Ndipo ndindakukhalalirani inu ndi mbewu zanu ngati chizindikiro ndi chozizwa nthawi zonse.
47 Popeza simunatumikira Ambuye Mulungu wanu ndi chimwemwe, ndi mokondwera mtima, chifukwa chakuchuluka zinthu zonse;
48 Chifukwa chake mudzatumikira adani anu amene Ambuye adzakutumizirani, ndi njala, ndi ludzu, ndi usiwa, ndi kusowa zinthu zonse: ndipo Iye adzaika goli lachitsulo pakhosi panu, kufukira Iye atakuonongani.
49 Ambuye adzakutengerani mtundu wa anthu wochokera kutali, kumalekezero a dziko lapansi, monga iwuluka mphungu; mtundu wa anthu umene simudzamva mayankhulidwe awo;
50 Mtundu wa anthu wa nkhope ya ukali, wosasamalira okalamba, wosam’chitira chifundo mwana:
51 Ndipo adzadya zipatso za ng’ombe zanu, ndi zipatso za nthaka yanu, kufikira mwaonongeka: osakuyikirani tirigu, vinyo, kapena mafuta, ngakhale zoswana ng’ombe zanu, kapena zoswana nkhosa zanu, kufikira atakuonongani.
52 Ndipo adzakuzingani m’midzi mwanu monse, kufikira adagwa malinga anu atali ndi olimba, amene munawakhulupilira, m’dziko lanu lonse: Inde, adzakuzingani m’midzi mwanu monse m’dziko lanu lonse, limene Ambuye Mulungu wanu akupatsani.
53 Ndipo mudzadya chipatso cha thupi lanu, nyama ya ana anu amuna ndi akazi, amene Ambuye Mulungu wanu anakupatsani, pakukumangirani tsasa, ndi kukupsinjani, adani anu:
54 Kuti mwamuna wololopoka nkhongono, ndi wanyonga pakati pa inu, diso lache lidzayipira mbale wake, ndi mkazi wa mtima wake, ndi ana ake amene adzawasiya:
55 Kuti asapatseko ndi mmodzi yemwe wa iwo nyama ya ana ache alinkudyayo: popeza sikamtsalira kanthu pakukumangirani tsasa, ndi kukupsinjani mdani wanu m’midzi mwanu monse.
56 Mkazi wololopoka nkhongono ndi wanyonga pakati pa inu, wosayesa kuponda pansi ndi phazi lake popeza ndiye wanyonga ndi wololopoka nkhongono, diso lache lidzamuipira mwamuna wa pamtima pache, ndi mwana wache wamwamuna, ndi mwana wake wamkazi,
57 Ndicho chifukwa cha matenda akutuluka pakati pa mapazi ache, ndi ana ache adzawabala: popeza adzawadya m’seri posowa zinthu zonse pakukumangirani tsasa ndi kukupsinjani mdani wanu m’midzi mwanu.
58 Mukapanda kusamalira kuchita mawu onse achilamulo ichi olembedwa m’bukhu ili, kuopa dzina ili laulemelero ndi loopsa, ndilo AMBUYE MULUNGU WANU;
59 Ndipo Ambuye adzachita miliri yanu, ndi ya ana anu ikhale yodabwitsa, miliri yaikuru, ndi yokhalitsa, ndi matenda, ndi zokhalitsa.
60 Ndipo Iye adzakubweretserani nthenda zonse za Aigupto, zimene munaziopa; ndipo zidzakumamatirani inu.
61 Ndiponso nthenda zonse, ndi miliri yonse, zosalembedwa m’buku la chilamulo ichi, Ambuye adzakutengerani izi, kufikira mwaonongeka.
62 Ndipo mudzatsala anthu pang’ono, mungakhale mudzachuluka ngati nyenyezi za m’mwamba; popeza simunamvera mau a Ambuye Mulungu wanu.
63 Ndipo kudzachitikadi, monga Ambuye anakondwera nanu kukuchitirani zabwino, ndi kukuchulutsani; momwemo Ambuye adzakondwera nanu kutayikitsa, ndi kuononga inu; ndipo adzakuzulani kudziko kumene mulowako kulilandira.
64 Ndipo Ambuye adzakubalalitsani mwa mitundu yonse ya anthu, kuyambira malekezero a dziko lapansi mpaka malekezero a dziko lapansi kwina; ndipo kumeneko mudzatumikira milungu yina, imene simudzayidziwa, inu ndi makolo anu, ngakhale mitengo ndi ya miyala.
65 Ndipo mwa a mitundu iyi simudzapumula, inde sipadzakhala popumula phazi lanu: koma Ambuye adzakupatsani kumeneko mtima wonjenjemera, m’maso mwanu mudzada, mudzafa ndi kulefuka mtima:
66 Ndipo moyo wanu udzakhala mokaikira pamaso panu; ndipo mudzachita mantha usiku ndi usana, ndiponso osakhazika mtima za moyo wanu.
67 M’mawa mudzati, Mulungu akadakhala madzulo! Ndipo madzulo mudzati, Mulungu ukanakhala m’mawa! Chifukwa cha mantha a mumtima mwanu amene mudzaopa nao, ndi chifukwa cha zopenya maso anu zimene mudzazipenya.
68 Ndipo Ambuye adzakubwezerani ku Aigupto ndi ngalawa, pa njira imene ndinati kwa inu kuti, Simudzaionanso: ndipo kumeneko mudzagulitsidwa kwa adani anu kuti mukhale akapolo ndi adzakazi, koma palibe wogula inu (Deuteronomo chaputara cha 28).

"Iye wakukonda atate wake kapena amake koposa Ine sayenera Ine: ndipo iye wakukonda mwana wake wamwamuna kapena wamkazi koposa Ine sayenera Ine" (Mateyu 10:37).

Ambuye ananena kuti ngati tisunga malamulo Ake, kapena kuti ngati tigwira ntchito Yake, Iye adzagwira yathu. Mulungu anati m’masiku otsiliza, iwo adzatenga icho chimene chili choipa ndikuchitembenuza kukhala chabwino, ndipo icho chimene chili chabwino kukhala choipa (Yesaya 5:20). Chifukwa cha kusokoneza kwa Satana pa malamulo a America, chilungamo sichikupezeka m’makhothi. Chilungamo chokhacho chimene chingapezeke lero chili m’nyumba ya Mulungu. Tsoka ilo, palibe ambiri. Komabe, tikufuna tisinthe zimenezo. Bwanji osatithandiza kusintha zimenezo? Bwanji osamulandira Ambuye Yesu Khristu? Bwanji osabwera ku tchalitchi ndi kuphunzira Mawu a Mulungu, kuvuta kwake, njira yake yoongoka ndi yopapatiza, chilungamo chake chosasinthika nthawi zonse? Aphunzireni ndi kugwiritsa ntchito mphamvu zake m’moyo wanu tsiku lili lonse kuti muthandize America kukhala yoyera ndi kuthandiza Khristu kuwina dziko lapansi.  Kwa a Katolika amene samadziwa zinthu izi, koma akufunitsitsa kutumikira Ambuye, Mulungu ali ndi uthenga wanu: "Tulukani m’menemo, anthu Anga" (Chivumbulutso. 18:4). Tulukani mwa iye ndipo "idzani kuno kwa Ine [Mau a Mulungu], inu nonse akulema ndi akuthodwa, ndipo Ine [Yesu] ndidzakupumulitsani inu [m’miyoyo yanu]" (Mateyu 11:28). Palibe munthu amene safuna mzake. Palibe munthu odziimila payekha. Mukuyenera kukhala ndi Khristu, osati chipembedzo kuti mukhululukidwe machimo anu ndikukalowa Kumwamba. Dzina lake ndi Wodabwitsa, Phungu, Kalonga wa Mtendere (Yesaya 9:6).

Pali nkhoswe imodzi ku mpando wa chifumu wa Mulungu. Ndiyo mamuna Khristu Yesu–Njira imodzi, Choona chimodzi, Moyo umodzi. Pali njira yoombola imodzi yokha. Palibe china koma mwazi wa Yesu ukhonza kuchotsa tchimo, chikhulupiliro chokha mu chiombolo cha Mulungu kudzera mwa Khristu Yesu.

"Ndipo musawaope iwo akupha thupi, koma moyo sangathe kuupha: koma makamaka muope Iye wakutha kuononga moyo ndi thupi lomwe m’Gehena" (Mateyu 10:28).

"Ine, Inedi, Ndine amene nditonthoza mtima wako: kodi iwe ndani, kuti uopa munthu amene adzafa, ndi mwana wa munthu amene adzakhala ngati udzu...?" (Yesaya 51:12).

"Siyani munthu, amene mpweya wake uli mphuno mwake: chifukwa mmene awerengedwamo ndi muti?" (Yesaya 2:22).

Simudzaonana ndi munthu pa bwalo la chiweruzo la Mulungu. Mudzaonana ndi Wamphamvu Zonse, Mlengi wanu. Simudzaonana ndi mulungu wachitini, wa bodza, amene avala nsalu yoyera, koma mudzaonana Naye Iye amene anati, "Ndi chinthu choopsa kugwa m’manja mwa Mulungu wamoyo" (Ahebri 10:31). Mulungu akunena kuti Iye ndi "Mulungu woopsa" (Nehemiya 1:5).

Ndimawakonda iwo akundiopa Ine (Masalimo 33:18). Udindo onse wa munthu ndiko kuopa Mulungu ndi kusunga malamulo Ake (Mlaliki 12:13).

Lapani, apo ayi mudzapita ku Gehena ndithu. Simukudziwa ngati mpweya ungathe m’thupi lanu mphindi zisanu kuchokera pano. Ndithu kuli Gehena yofunika kupewa komanso Kumwamba  kopindulitsa.  Kotero lekani kuchita ntchito zoipa ndi kutumikira Ambuye m’malo mwake, kuti mupulumutsidwe nthawi yomwe ino pompano. Nenani pemphero ili kwa Mulungu:

Prayer

AMBUYE wanga komanso MULUNGU wanga, ndichitireni chifundo ndine munthu wochimwa.1 Ndikukhulupirira kuti YESU KHRISTU ndi MWANA wa MULUNGU wamoyo.2 Ndimakhulupiriranso kuti IYE anafera pamtanda ndipo anakhetsa mwazi WAKE wamtengo wapatali ndi cholinga choti machimo anga onse akhululukidwe.3 Ndikukhulupiriranso kuti MULUNGU anaukitsa YESU kwa akufa pogwiritsa ntchito mphamvu ya MZIMU WOYERA,4 ndiponso kuti IYE anakhala kudzanja lamanja la MULUNGU ndipo panopa akumva pemphero langa lolapali.5 Ndikutsegula zitseko za mtima wanga, ndipo ndikukuyitanani kuti mulowe mumtima mwanga, inu AMBUYE YESU.6 Tsukani machimo anga ambirimbiri achoke onse mu mwazi wamtengo wapatali umene INU munakhetsa m’malo mwanga pamtanda wa ku Kavari.7 Ndikudziwa kuti mundimvera pemphero langali AMBUYE YESU; INU mukhululukira machimo anga ndi kupulumutsa moyo wanga. Ndikudziwa izi chifukwa MAWU ANU, Baibulo, limanena zimenezi.8 MAWU ANU amati INUYO simudzakana kumvetsera pemphero la munthu aliyense, ndipo ine ndili m’gulu la anthu amenewo.9 Choncho, ndikudziwa kuti INUYO mukundimvetsera pamene ndikupemphera ndipo ndikudziwanso kuti INUYO mundiyankha komanso mundipulumutsa.10 Ndipo ndikukuthokozani AMBUYE YESU, chifukwa chopulumutsa moyo wanga, ndipo ndisonyeza kuyamikira mwa kuchita zinthu zimene INUYO munalamula komanso kupewa kuchita uchimo.11

Pambuyo pa chipulumutso, YESU ananena kuti munthu ayenera kubatizidwa pomizidwa thupi lonse m’madzi, m’dzina la ATATE, ndi la MWANA, ndi la MZIMU WOYERA.12 Muziphunzira mwakhama Baibulo la Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu, [King James Version] ndipo muzichitazimene Baibulolo limanena.13

AMBUYE akufuna kuti inuyo muziwuza ena za chipulumutso chanu. Mungathe kukhala wofalitsa uthenga wabwino wa M’busa Tony Alamo. Tizikutumizirani mabuku mwaulere. Imbani foni kapena tumizani imelo kwa ife kuti mudziwe zambiri. Tikukupemphani kuti muwuzeko ena uthengawu.

Ngati mukufuna kuti dziko lipulumutsidwe monga m’mene YESU akulamulira, mukufunika kupereka chakhumi kwa MULUNGU. MULUNGU anati, “Kodi munthu angabere MULUNGU? Inde, mwandibera kale. Koma akuti, Ife tikumubera bwanji MULUNGU? Mu chakhumi ndi mu zopereka. Anthuwo ndi otembereredwa chifukwa akundibera, ngakhale mtundu wonsewu [dziko lonse lapansi]. Bweretsani nonse chakhumi [‘chakhumi’ ndi gawo limodzi la magawo khumi (10%) ya malipiro anu] m’nkhokwe zanga n’cholinga choti pakhale nyama [chakudya cha Uzimu] mu nyumba
YANGA [anthu opulumutsidwa] kuti mundiyese, akutero AMBUYE wa MAKAMU, kuti muone ngati sindidzakutsegulirani mazenera a Kumwamba ndi kukukhuthulirani madalitso amene mudzasowa malo owalandirira.” Ndipo ndidzadzudzula anthu okudyerani masuku pamutu ndipo sadzawononga zipatso za nthaka yanu; ngakhalenso mphesa wanu sudzalephera kubala zipatso pa nyengo yake m’minda yanu, watero AMBUYE wa MAKAMU. Ndipo mitundu yonse idzakutchani odala: chifukwa
dziko lanu lidzakhala labwino, watero AMBUYE wa MAKAMU”(Malaki 3:8-12).


Chichewa/Nyanja Alamo Literature

Ngati mukufuna kudziwa zambiri kapena ngati mukufuna mabuku kapenanso nkhani zina zimene zimakusangalatsani, tiimbireni foni kapena tilembereni.

Tony Alamo, World Pastor
Tony Alamo Christian Ministries Worldwide
P. O. Box 2948
Hollywood, CA 90078

Lamya ya pemphero ndi uthenga maola 24: (661) 252-5686

Tony Alamo Christian Ministries Worldwide imalandira anthu onse ndipo imapereka zinthu zofunika Kwa onse amene ali ku U.S. amene akufunitsitsadi kuti ayambe kutumikira AMBUYE ndi mtima wawo wonse moyo wawo wonse ndi mphamvu zawo zonse.

Mapemphero amachitika mu Mzinda wa New York Lachiwiri lili lonse nthawi ya 8 Koloko usiku ndi madera ena usiku okhaokha. Chonde imbani foni kuti mumve zambiri: +1 (908) 937-5723. ZAKUDYA ZIMAGAWIDWA PA MAPETO PA MAPEMPHERO ALI WONSE

Funsani buku la M’busa Alamo, lakuti Mesiya, losonyeza KHRISTU kuyambira ku Chipangano Chakale mu maulosi oposa 333.

Khalani wogwira ntchito yokolola miyoyo ya anthu pakukhala ogawira mabuku a M’busa Alamo. Mabuku ndi zinthu zonse zomvetsera n’zaulere, ndipo simulipira ndalama yotumizira

M’BUKU ILI MULI CHIKONZERO CHENICHENI CHA CHIPULUMUTSO (Machitidwe 4:12).
MUSALITAYE, PATSANI ENA KUTI AWERENGE.

Anthu amene muli m’mayiko ena, tikukulimbikitsani kuti mumasulire n’chinenero chanu mabukuwa. Ngati mukusindikizanso bukuli, musaiwale kuika mawu ali m’munsiwa omwe ndi okhudzana ndi zamalamulo:

© Copyright 1993 All rights reserved World Pastor Tony Alamo ® Registered 1993


footnotes:

1. Kufikira 1987 mabungwe onse achi communism samalipira msonkho. Tsopano Internal Revenue Service anachotsa kusapereka msonkhoku. Komabe ma communist a Vatican anakhanzikika kwambiri m’boma podziphimba nkumadzionetsa ngati ma Republlican ndi ma Democrat kuti sakufunanso kuchotsedwa polipira misonkho, ndalama (grants) za boma ndiye osanena zimene zimaperekedwa kumagulu awo a "Pseudo Charitable" ndi magiranti a madollar ma biliyoni ambirimbiri ku masukulu a mdera ndi mabungwe ena a communist a Katolika. return


prayer footnotes:

1. Masa. 51:5, Aro. 3:10-12, 23 return

2. Mat. 26:63-64, 27:54, Luka 1:30-33, Yoh. 9:35-37, Aro. 1:3-4      return

3. Mach. 4:12, 20:28, Aro. 3:25, 1 Yoh. 1:7, Chiv. 5:9      return

4. Masa. 16:9-10, Mat. 28:5-7, Marko 16:9, 12, 14, Yoh. 2:19, 21, 10:17-18, 11:25, Mach. 2:24, 3:15, Aro. 8:11, 1 Akor. 15:3-7      return

5. Luka 22:69, Mach. 2:25-36, Aheb. 10:12-13   return

6. 1 Akor. 3:16, Chiv. 3:20      return

7. Aef. 2:13-22, Aheb. 9:22, 13:12, 20-21, 1 Yoh. 1:7, Chiv. 1:5, 7:14      return

8. Mat. 26:28, Mach. 2:21, 4:12, Aef. 1:7, Akol. 1:14      return

9. Mat. 21:22, Yoh. 6:35, 37-40, Aro. 10:13      return

10. Aheb. 11:6     return

11. Aheb. 5:14, 8:11, Aro. 6:4, 1 Akor. 15:10, Chiv. 7:14, 22:14      return

12. Mat. 28:18-20, Yoh. 3:5, Mach. 2:38, 19:3-5   return

13. Deut. 4:29, 13:4, 26:16, Yoswa 1:8, 22:5, 2 Tim. 2:15, 3:14-17, Yakobo 1:22-25, Chiv. 3:18 return