SODOMU NDI GOMORA

Yolembedwa ndi Tony Alamo

Kufupi ndi Yeriko ku Israeli kuli malo wotchedwa Sodomu ndi Gomora.1  Mutawaona, mukhonza kudziwa opandanso kukaika kuti MULUNGU ndi MULUNGU wa chiweruzo!2 Mukhoza kutenga zidutswa za chikasu za sulfure, ndipo zimanyeka mukaziyatsa. Ndi zinthu zoopsa kwambiri kuziona m’moyo wanu. Mapiri amaoneka ngati kuti MULUNGU anamenya chibakela nsonga za mapiri kukhala zidutswa zikuluzikulu, kenako, ndi nkhonya YAKE yaikulu, nkuphwanya chili chonse nkukhala mulu wotitimira, ndikukwilira mu mchere, sulfure (brimustoni), ndi moto. Tengerani kunyumba chidutswa cha chikasu cha sulfure (Brimustoni) monga chikumbutso. Tengani chidutswa china chapadera kuti mukaike mu bokosi loponyera mavoti a chisankho pamene anthu akuti, “Tiyeni tivote tione ngati ukwati wa amuna kapena akazi okhaokha ndi wabwino.” Osayerekeza kunena ndi anthu kuti MAWU A MULUNGU si oona! Sitingathe kudziwa cholondola, cholakwika, chabwino, kapena choipa opanda MAWU A MULUNGU!3

Dera lonseli ndilotentha kuposa malo ena aliwonse mu Nthaka Yopatulika. Komanso ndi dera lopanda moyo kwambiri. Kafupi nalo, kuli mapiri akuluakulu a mchere.4 Ziribe kanthu kuti Mtsinje wa Yorodani umayenda ndi kutsanulira madzi ake abwino bwanji mu Dead Sea, madzi a Dead Sea ndi amchere kwambiri, ndipo sadzasunga moyo, kupanga nsomba. Kugwa kwa mapiri kunapangitsa derali kukhala bwinja kwambiri, ndipo m’nthaka pafupi ndi mahotela muli chinthu chachikulu cha mphako. Derali limatchedwa Engedi, kutanthauza “diso la nkhosa.” Derali lili ndi mahotela akuluakulu atatu, ndi khumi ang’onoang’ono, onse ali ndi maiwe osambira. Chinthu chachikulu cha mphako komanso chionongeko chenicheni zili pamsewu wakumbuyo wochokera ku Engedi kupita ku Beeresheba. Mukaima m’mphepete mwa tsonga la mphako, mukhoza kuona bwinobwino chionongeko, dera la mapiri okugwa la Sodomu ndi Gomora. Kumbuyo kwa mphako, kuli mapiri ophimbidwa ndi mitambo ndi chifunga. Chete wake ndi bwinja lake zimapatsa mantha. Pafupifupi ndizosatheka kuona pansi pa mphako, ndipo ndiyotambalala kwambiri.

Ndi maphako akuluakulu angati mu nthaka amene alipo—mabowo akuluakulu mpaka nthaka kung’aluka—amene ali zotsatira za kuwonongedwa ndi kukwiliridwa kwa Sodomu ndi Gomora? Yeriko aphatikizidwe, nayenso, chifukwa Sodomu ndi boma chabe mu Yeriko. Pamene mukutsika msewu wa m’phiri kuchokera ku Yerusalemu kupita ku Yeriko, makutu anu amachita popu, ngati kuti mukutera mu ndege. Yeriko ali kutali pansi ndi madzi a m’nyanja, malo otsika kwambiri padziko lonse lapansi. Chifukwa chake n’chakuti MULUNGU anaphwanya dera lonse. IYE analipanga dera lotsikitsitsa padziko lapansi chifukwa cha tchimo limene iwo anachita.5

Yeriko, kupatulapo mzinda, pafupifupi ulibe kanthu, ndipo kulibe moyo uliwonse kumeneko, pakuti dziko linatembereredwa. Zimakupangitsa kukhala ndi chisoni. Nthaka yake ndi yankhanza. Zilibe kanthu kuti ndikangati kamene anthu ayesa kukonza nthakayo, kubweretsa mtundu wa moyo komanso chisangalalo ku nthakayo; nthaka imabwenzera kuwamenya, ndipo sipindula kapena kutukuka. Mukhonza kuona mapanga ndi nyumba zosiyanasiyana  kumeneko zimene zinawonongeka. Anthu amene amakhala kumeneko ndi ochepa, ndipo ambiri ndi osamala ziweto. Moyo wawo ndi wovuta ndiponso wozunzika, monga nthaka yawo ilili ndi nkhanza, ndipo nkhope zawo zioneka molimba ngati thanthwe.

Anthu, mpaka lero, amatola miyala ya sulfure, mabrimustoni, amene MULUNGU amaonetsera deralo. Amatenga zikumbutso ndi kuyesa kuyatsa miyala ya sulfure ndi machesi. Mbala za ziliza  komanso akatswiri a zinthu za makedzana (archaeologists) kaŵirikaŵiri amayendera madera amenewa chifukwa cha mabokosi amaliro ndi ziliza.  Achifwamba amakumba usiku, kufunafuna matupi, mbiya, zikho, majuwale, ndi zokhoma monga mipando kuti akagulitse akatswiri a zinthu zakale asanawapeze. Amayesanso kukumba mapanga ndi nyumba zowonongedwa kuchokera ku miyala, mabrimustoni, ndi sulfure.

Aliyense amene ayang’ana pa ukulu wa chiwonongeko m’dera limeneli sadzakaika kuti ichi kwenikweni ndi chiwonongeko komanso chilango cha MULUNGU  pa deralo, monga dziko lonse la Israeli ndi lobiriwira ndi lotukuka, kupatula dera la Sodomu ndi midzi yozungulira. MULUNGU posachedwapa adzabweretsanso chiwonongeko CHAKE pa dziko lino ndi pa dziko lonse lapansi.6

Mu U.S., simunachitikepo chivomezi choposa 9.2 pasikelo yotchedwa Richter. Ndikosavuta kuona kuti ngati chiwonongeko cha MULUNGU cha Sodomu ndi Gomora chikanaweruzidwa pa sikelo ya  Richter ya masiku ano, chikanakhala 25.0 kapena kuposera. Izi sizikutengera ngakhale ndi moto ndi brimustoni kuvumba molimba pa anthu chifukwa cha zoipitsitsa zawo za mchitidwe wa kugonana, monga kugonana amuna kapena akazi okhaokha ndi dama.7

Dera lonseli likhale umboni wa MULUNGU kwa anthu onse, makamaka iwo opotozedwa ndi kuchita za umathanyula komanso kugonana akazi okhaokha. Mukaonetsetsa izi, mudzazindikira kuti MULUNGU si wantchedzera. IYE amatanthauza chenicheni chimene IYE anena.8 Ndi mapeto a nthawi, kotero inunso musakhale antchedzera pamene mukunena pemphero ili kwa MULUNGU:

Prayer

AMBUYE wanga komanso MULUNGU wanga, ndichitireni chifundo ndine munthu wochimwa.1 Ndikukhulupirira kuti YESU KHRISTU ndi MWANA wa MULUNGU wamoyo.2 Ndimakhulupiriranso kuti IYE anafera pamtanda ndipo anakhetsa mwazi WAKE wamtengo wapatali ndi cholinga choti machimo anga onse akhululukidwe.3 Ndikukhulupiriranso kuti MULUNGU anaukitsa YESU kwa akufa pogwiritsa ntchito mphamvu ya MZIMU WOYERA,4 ndiponso kuti IYE anakhala kudzanja lamanja la MULUNGU ndipo panopa akumva pemphero langa lolapali.5 Ndikutsegula zitseko za mtima wanga, ndipo ndikukuyitanani kuti mulowe mumtima mwanga, inu AMBUYE YESU.6 Tsukani machimo anga ambirimbiri achoke onse mu mwazi wamtengo wapatali umene INU munakhetsa m’malo mwanga pamtanda wa ku Kavari.7 Ndikudziwa kuti mundimvera pemphero langali AMBUYE YESU; INU mukhululukira machimo anga ndi kupulumutsa moyo wanga. Ndikudziwa izi chifukwa MAWU ANU, Baibulo, limanena zimenezi.8 MAWU ANU amati INUYO simudzakana kumvetsera pemphero la munthu aliyense, ndipo ine ndili m’gulu la anthu amenewo.9 Choncho, ndikudziwa kuti INUYO mukundimvetsera pamene ndikupemphera ndipo ndikudziwanso kuti INUYO mundiyankha komanso mundipulumutsa.10 Ndipo ndikukuthokozani AMBUYE YESU, chifukwa chopulumutsa moyo wanga, ndipo ndisonyeza kuyamikira mwa kuchita zinthu zimene INUYO munalamula komanso kupewa kuchita uchimo.111

Pambuyo pa chipulumutso, YESU ananena kuti munthu ayenera kubatizidwa pomizidwa thupi lonse m’madzi, m’dzina la ATATE, ndi la MWANA, ndi la MZIMU WOYERA.12 Muziphunzira mwakhama Baibulo la Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu, [King James Version] ndipo muzichitazimene Baibulolo limanena.13

AMBUYE akufuna kuti inuyo muziwuza ena za chipulumutso chanu. Mungathe kukhala wofalitsa uthenga wabwino wa M’busa Tony Alamo. Tizikutumizirani mabuku mwaulere. Imbani foni kapena tumizani imelo kwa ife kuti mudziwe zambiri. Tikukupemphani kuti muwuzeko ena uthengawu.

Ngati mukufuna kuti dziko lipulumutsidwe monga m’mene YESU akulamulira, mukufunika kupereka chakhumi kwa MULUNGU. MULUNGU anati, “Kodi munthu angabere MULUNGU? Inde, mwandibera kale. Koma akuti, Ife tikumubera bwanji MULUNGU? Mu chakhumi ndi mu zopereka. Anthuwo ndi otembereredwa chifukwa akundibera, ngakhale mtundu wonsewu [dziko lonse lapansi]. Bweretsani nonse chakhumi [‘chakhumi’ ndi gawo limodzi la magawo khumi (10%) ya malipiro anu] m’nkhokwe zanga n’cholinga choti pakhale nyama [chakudya cha Uzimu] mu nyumba
YANGA [anthu opulumutsidwa] kuti mundiyese, akutero AMBUYE wa MAKAMU, kuti muone ngati sindidzakutsegulirani mazenera a Kumwamba ndi kukukhuthulirani madalitso amene mudzasowa malo owalandirira.” Ndipo ndidzadzudzula anthu okudyerani masuku pamutu ndipo sadzawononga zipatso za nthaka yanu; ngakhalenso mphesa wanu sudzalephera kubala zipatso pa nyengo yake m’minda yanu, watero AMBUYE wa MAKAMU. Ndipo mitundu yonse idzakutchani odala: chifukwa
dziko lanu lidzakhala labwino, watero AMBUYE wa MAKAMU”(Malaki 3:8-12).


Dera la Sodomu ndi Gomora

Genesis 19:27-28 amati, “Ndipo Abrahamu analawira m’mamawa kunka kumalo kumene anaima pamaso pa YEHOVA: Ndipo anayang’ana ku Sodomu ndi ku Gomora, ndi ku dziko lonse la chigwa, ndipo anapenya, ndipo, taonanitu, utsi wa dzikolo unakwera monga utsi wa ng’anjo.”

Zaka za kumayambiliro am’ma 1980, katswiri oyendera za malo a m’Baibulo (archaelogical), Ron Wyatt, anaona “mapangidwe” ooneka mwachilendo pamene ankayenda m’mphepete mwa nyanja ya Dead Sea. Kwa iye ankaoneka ngati makoma a mzinda ndi nyumba, a mtundu woyera okhaokha. Kwa zaka zambiri sanachitepo kanthu pa zokaikira zakezo, koma mu 1989, Ron anapeza chinachake chomwe chinamulimbikitsa kuti mapangidwe ooneka oyerawo sianali ochokera ku nthaka (geological).

Kuposa mphipi ya Miyala

Ron anapeza njira imene inabooledwa kudzera pakati pa zina mwa zinthu zoyera ndipo mkati mwake moonekera mwatsopano muli zinthu zoikidwa pamtetete mwadongosolo zomwe zimazungulira mowonetseratu kuti  zinali zoposa mphipi za miyala.

Pofufuza m’Baibulo kuti apeze malo awo, Ron ndi mkazi wake Mary Nell anapeza umboni wa malemba okamba za mizinda inayi yomwe inkapanga malire a Kenani:
“Ndipo malire a Kenani amachokera ku Sidon, ngati ukubwera ku Gerar, mpaka ku Gaza; ngati ukupita, ku Sodomu, ndi Gomora, ndi Admah, ndi Zeboim, ngakhalenso  ku Lasha” (Genesis 10:19).

Zingakhale zachilendo kuti Sodomu, Gomora, Admah, ndi Zeboim aliyense akhale opanga malire ngati onsewo anali mudera limodzi, kumathero a kum’mwera kwa Dead Sea. Zikuonekeratu kuti mizindayi inali yotalikirana kuti kukhale koyenera kuphatikiza aliyense ngati opanga malire.

Malo omwe Ron anapeza anali, ndithudi, otalikilana mtunda oposa mamailosi makumi asanu kapena kuposela apo. Amodzi mwa iwo anali kumpoto kwa Yeriko zomwe zikugwirizana ndi malemba omwe akunena kuti Zeboin ali kumpoto kwa Dead Sea.

“Ndipo Sauli, ndi mwana wake Jonathan, ndi anthu omwe anali nawo, anali kukhala ku Gebeya wa ku Benjamini: koma Afilisiti anali atamanga misasa ku Mikimasi. Ndipo anthu olanda katundu anali kutuluka mumsasa wa Afilisiti m’magulu atatu: gulu loyamba linali kulowera njira yopita ku Ofira, kudera la Suwali: Ndipo gulu lachiwiri linali kulowera njira yopita ku Betihoroni: Ndipo gulu lachitatu linali kulowera njira yopita kumalire oyanq’anana ndi chigwa cha Zeboin molunjika kuchipululu” (1 Samueli 13:16-18).
Kenako m’chaka cha 1989, Ron ndi Mary Nell Wyatt anakayendera malo akunsi kwa Masada ndipo anatenga masampulo a zinthu zoyera zomwe zinanyenyekera m’manja mwao nkusanduka  ngati ufa wa talcum. Panthawi yimeneyo, Mary Nell anapeza imodzi mwa makapusolo a sulfure itakhanzikika m’chidutswa cha phulusa logwirana; komabe, sanapeze chotsatira chenicheni, pa nthawi imeneyo, kuti chinali chani.

Mu October ya 1990, Ron Watt ndi Richard Rives anabweleranso  kumalo aja. Pamene ankayeza malo akunsi kwa Masada, anapeza kuti mvula yangogwa kumene. Pamene ankayendabe kumaloko, Richard anaona kuti chomwe chimaoneka ngati chipinda chotsegula kapena mphanga chapatali ndipo pamene anafika pafupi ndi mphanga anaona mulu  waukulu wa phulusa omwe unali utangogwa kumene kuchoka ku chipupa chachitali—nkutheka kamba ka mvula yomwe inangogwa kumene. Pamene Ron anaima kuti aone izi, anaona mipila ya chikasu yambiri mkati mwa mulu wa phulusa logumukali, yonse yozunguliridwa ndi mzele wolimba mokukutika, wofiilira-wakuda . Ataonesetsa umodzi mwaiwo, anazindikila kuti anali sulfure. Ataonetsetsa pafupi, tsopano akudziwa choti afunefune, kunapezeka kuti mu zotsalira za phulusa zonse zija munali mipira yozungulira ya sulfure wa makapusolo (brimustoni).

Patatha kafukufuku wa brimustoni, Wyatt Archaeological Research inayamba kuphunzira kuti aone ngati brimustoni anapezekako wa maonekedwe awa kwina kuli. Ron Wyatt ndi Mary Nell pamodzi ndi Richard Rives anapita ku Smithsonian Institute, ku Washington D.C. ndi kuyeza chionetsero chawo cha sulfure m’maonekedwe ake osiyanasiyana, popanda sulfure waufa wozungulira ngati mipira. Kuwonjezera apo, panalibe ngakhale m’modzi okutiridwa ngati kapusolo. Pempho linaperekedwa ndi Smithsonian kuti masampulo ena osati omwe anali pa chionetsero ayezedwenso. Sulfure yense yemwe anasonkhetsedwa kuchokera padziko lonse lapansi, anali opangidwa ndi masampulo oposa makumi asanu. Panalibe yemwe anaonetsa zizindikilo zofanana ndi sulfure wa brimustoni yemwe anapezeka kufupi ndi “mizinda ya chigwa.”

Ron Wyatt sanali oyamba kupeza brimustoni pafupi ndi Dead Sea. Pamene William Albright ndi Melvin Kyle ananyamuka kupita kukapeza mizinda ya Sodomu ndi Gomora mu 1924, naonso, chimodzimodzi, anapeza zidutswa za brimustonizi ku kumapeto a kum’mwera kwa Dead Sea.

“…chigawo chomwe brimustoni anavumbidwa ndi mvula chidzaonetsa brimustoni. Ndithu, chitero; Tinatenga sulfure weniweni, mu dzidutswa zazikulu ngati mathero a chala change cha chikhatho. Ndiwosakanikirana ndi dothi la ku phiri ku mbali ya kumvuma kwa nyanja, ndipo tsopano apezeka atamwazikira ngakhale m’mbalimbali mwa nyanja ku mbali ya kuzambwe, mamailosi anayi kapena asanu kuchokera kuphompho lomwe linali ndi mphipi za miyala. Anamwazikira kutali ndi kumbali zonse pa chigwachi.” (Explorations at Sodom by Dr. Melvin Kyle, 1928, pp. 52-53)

Melvin Kyle sanali oyamba kuona zotsalira za phulusa. Nkhani zina zokhudza mizinda imeneyi ndi zochokera kwa Josephus mu bukhu lake la Wars of the Jews, Bukhu IV, Chaputara VIII:

“Tsopano dzikoli linaotcheka momvetsa chisoni, moti palibe yemwe amafuna kufikako;… Kale linali dziko losangalala kwambiri, kamba ka zipatso zomwe nthaka yake inkabereka komanso chuma cha mizinda yake, ngakhale pano inapsyelatu yonse. Zikugwirizana ndi m’mene, chifukwa cha kusowa ulemu pa chipembedzo kwa anthu ake, iyo inaotchedwa ndi mphenzi; kotero kudakali zotsalira za moto wa Mulungu; ndipo zizindikiro (kapena zithunzithunzi) za mizinda isanu zikudikiridwa kuoneka…”
Josephus’ description perfectly describes what can be seen at these ashen sites:
“...iwo tsopano zonse zawotcheka.”

Nkhani ya chiwonongeko cha Sodomu, Gomora, ndi “chigwa chonse” sinali nthano. Inali mbiri yochitika imene inachitika chimodzimodzi monga inanenera nkhani ya m’Baibulo.

http://www.wyattmuseum.com/cities-of-the-plain.htm


Chichewa/Nyanja Alamo Literature

Ngati mukufuna kudziwa zambiri kapena ngati mukufuna mabuku kapenanso nkhani zina zimene zimakusangalatsani, tiimbireni foni kapena tilembereni.

Tony Alamo, World Pastor
Tony Alamo Christian Ministries Worldwide
P. O. Box 2948
Hollywood, CA 90078

Lamya ya pemphero ndi uthenga maola 24: (661) 252-5686

Tony Alamo Christian Ministries Worldwide imalandira anthu onse ndipo imapereka zinthu zofunika Kwa onse amene ali ku U.S. amene akufunitsitsadi kuti ayambe kutumikira AMBUYE ndi mtima wawo wonse moyo wawo wonse ndi mphamvu zawo zonse.

Mapemphero amachitika mu Mzinda wa New York Lachiwiri lili lonse nthawi ya 8 Koloko usiku ndi madera ena usiku okhaokha. Chonde imbani foni kuti mumve zambiri: +1 (908) 937-5723. ZAKUDYA ZIMAGAWIDWA PA MAPETO PA MAPEMPHERO ALI WONSE

Funsani buku la M’busa Alamo, lakuti Mesiya, losonyeza KHRISTU kuyambira ku Chipangano Chakale mu maulosi oposa 333.

Khalani wogwira ntchito yokolola miyoyo ya anthu pakukhala ogawira mabuku a M’busa Alamo. Mabuku ndi zinthu zonse zomvetsera n’zaulere, ndipo simulipira ndalama yotumizira

M’BUKU ILI MULI CHIKONZERO CHENICHENI CHA CHIPULUMUTSO (Machitidwe 4:12).
MUSALITAYE, PATSANI ENA KUTI AWERENGE.

Anthu amene muli m’mayiko ena, tikukulimbikitsani kuti mumasulire n’chinenero chanu mabukuwa. Ngati mukusindikizanso bukuli, musaiwale kuika mawu ali m’munsiwa omwe ndi okhudzana ndi zamalamulo:

© Copyright April 2015 All rights reserved World Pastor Tony Alamo ® Registered April 2015
CHICHEWA/NYANJA—VOLUME 21200—SODOM AND GOMORRAH


footnotes:

1. Gen. 18:20-33, 19:1-29, Deut. 29:23 return

2. Gen. chap. 6-7, Num. 11:1, Deut. 4:24, 10:17, 32:4, 15-16, 19-26, 35:43, Masa. 2:1-5, 12, 7:11-12, 11:5-6, 21:8-9, Yes. 30:1-3, 30, 33, 66:15-16, 24, Yer. 7:20, 10:10, 21:11-14, Mali. 4:11, Nah. 1:2-8, Mat. 25:31-46, 2 Akor. 5:10-11, Aheb. 10:30-31, 2 Pet. 2:4-9, Yuda 7, Chiv. 14:9-11, 20:11-15 return

3. Ex. 20:1-7, Deut. 5:1-21, Yoswa 1:8, Masa. 119:9, 104-105, 130, Miy. 6:23, Mal. 4:4, Yoh. 5:24, 8:31-32,12:48, 15:3, 2 Tim. 3:15-17, Yako. 1:21-25, 2 Pet. 1:19 return

4. Gen. 19:24-26, Deut. 29:23, Yes. 13:19-22, Yer. 50:40, Mali. 4:6, Zef. 2:9 return

5. Gen. 13:13, 18:20-21, 19:1-13, 24-25, Ezek. 16:49-50, Yuda 7 return

6. Yes. 13:3-13, 24:1-21, 34:1-10, Ezek. 22:25-31, 24:6-14, chap. 38, Yowe. 1:13-15, Zefa. 3:8, Mal. 4:1, Mat. 24:3-7, 21-22, 29-34, Luka 17:24-30, 2 Ates. 1:7-10, 2 Pet. 3:3-12, Chiv. 6:15-17, 8:7-13, 9:1-19, 11:18, 16:1-11, 17-21, 19:11-21 return

7. Gen. 19:4-13, Lev. 18:20, 22, 20:13, Deut. 22:5, 23:17-18, Ower. 19:22-28, 1 Mafu. 14:22-24, Aro. 1:18, 24-32, 1 Akor. 6:9-10, 18, 10:8, 2 Akor. 12:21, Agal. 5:19-21, Aef. 5:3-6, Akol. 3:5-7, 1 Ates. 4:3, 1 Tim. 1:9-10, Aheb. 13:4, Yuda 7, Chiv. 2:21, 9:21, 22:15 return

8. Num. 23:19, 1 Sam. 15:29, Masa. 119:89, Miy. 19:21, Mlal. 3:14, Yes. 14:24, 40:8, Yer. 4:28, Ezek. 24:14, Dan. 4:35, Mat. 5:17-18 return


prayer footnotes:

1. Masa. 51:5, Aro. 3:10-12, 23 return

2. Mat. 26:63-64, 27:54, Luka 1:30-33, Yoh. 9:35-37, Aro. 1:3-4      return

3. Mach. 4:12, 20:28, Aro. 3:25, 1 Yoh. 1:7, Chiv. 5:9      return

4. Masa. 16:9-10, Mat. 28:5-7, Marko 16:9, 12, 14, Yoh. 2:19, 21, 10:17-18, 11:25, Mach. 2:24, 3:15, Aro. 8:11, 1 Akor. 15:3-7      return

5. Luka 22:69, Mach. 2:25-36, Aheb. 10:12-13   return

6. 1 Akor. 3:16, Chiv. 3:20      return

7. Aef. 2:13-22, Aheb. 9:22, 13:12, 20-21, 1 Yoh. 1:7, Chiv. 1:5, 7:14      return

8. Mat. 26:28, Mach. 2:21, 4:12, Aef. 1:7, Akol. 1:14      return

9. Mat. 21:22, Yoh. 6:35, 37-40, Aro. 10:13      return

10. Aheb. 11:6     return

11. Aheb. 5:14, 8:11, Aro. 6:4, 1 Akor. 15:10, Chiv. 7:14, 22:14      return

12. Mat. 28:18-20, Yoh. 3:5, Mach. 2:38, 19:3-5   return

13. Deut. 4:29, 13:4, 26:16, Yoswa 1:8, 22:5, 2 Tim. 2:15, 3:14-17, Yakobo 1:22-25, Chiv. 3:18 return