UMBONI WA TONY ALAMO Mafupa Owuma

Yolembedwa ndi Tony Alamo

Ezekieli, yemwe ndi mneneri wa mu Chipangano Chakale, anaona masomphenya ochokera kwa Mulungu. Iye anaona chigwa cha mafupa owuma, chomwe chinaimira kufa mwa uzimu kwa Isiraeli ndiponso dziko lonse lapansi. Masomphenyawa analosera za kubwera koyamba kwa Khristu, kulalikira kwake uthenga wabwino ndiponso zotsatira zake, kuukitsidwa kwa akufa koyamba n’kulandira moyo wosatha kwa anthu onse amene amakhulupirira “Mawu a Ambuye.”1

Mulungu anamufunsa Ezekieli kuti, “Iwe mwana wa munthu, kodi mafupa amenewa angakhalenso ndi moyo?” (Kodi anthu amene anafa mwauzimu angakhalenso ndi moyo?) Ezekieli anayankha kuti, “Ambuye, mukudziwa ndinu chifukwa ndinuyo amene munawalenga.”2 Kenako Mulungu analankhulanso ndi mneneriyu n’kumuuza kuti, “Losera zokhudza mafupawa ndipo ulankhule nawo kuti, mafupa owuma inu, imvani Mawu a Ambuye. Ambuye akulankhula ndi mafupawa kuti: Taonani, ndidzachititsa mpweya kulowanso mwa inu, ndipo mudzakhalanso ndi moyo.”3

Mtundu wa Isiraeli unkadziwiratu kuti unali utalowerera kotheratu ngati mtundu.4 Pomafika nthawiyi, Aisiraeli anali atagawanika komanso anali opanda chiyembekezo chilichonse. Koma Mulungu anamuuza Ezekieli kuti Iye adzautsa mtundu wina waukulu kuposa mtundu woyambirira wa Isiraeli, womwe unkapitiriza kuchimwira Mulungu. Mtundu wachiwiri wa Isiraeli udzakhala wa anthu ochokera mumtundu uliwonse padziko lapansi,5 anthu okhulupirika ochokera mwa Ayuda ena osankhidwa komanso khamu la anthu Amitundu amene anaphatikizidwa ku Mpesa Weniweni (Khristu).6 Mtunduwu unali kudzakhala waukulu komanso wopatulika, wopangidwa ndi anthu amene anaukitsidwa kwa akufa mu uchimo n’kukhalanso ndi moyo wosatha.7 Mtundu umenewu sudzakhala wogawanika pamaso pa Mulungu. Uku kunali kuukitsidwa koyamba kudzera mwa mphamvu zoukitsa akufa za Khristu.8

Mu 1964, ndisanaukitsidwe koyamba ndi Khristu, ineyo, Bernie Hoffman, amene ndimadziwikanso ndi dzina loti Tony Alamo, ndinali wodziwika bwino kuti ndine munthu wokonda kuchita machimo komanso zinthu zosaopa Mulungu. Sindinkamudziwa Mulungu ngakhale pang’ono. Sindinkadziwa n’komwe zoti kunja kuno kuli Mulungu. Ndinkangoona kuti nkhani zonse zimene zili m’mawu a Mulungu ndi zongopeka komanso nthano, ndipo sindinkamvetsa chifukwa chake anthu ena amakhulupirira Mulungu komanso Mwana Wake. Zinkandivuta kumvetsa kuti n’chifukwa chiyani anthu ena amakhulupirira Mulungu chifukwa anthuwo anali odzikonda. Ndinkaona kuti anthuwo amachitanso machimo ngati ine ndemwe, mwinanso kundiposa. Ndinkadziwa zimenezi chifukwa ena mwa anthuwa ndinkacheza nawo. Tonse tinali akufa, tinali mulu wa mafupa owuma. Ndinkakwiya koopsa wina akayeserera kundiuzako za Chikhristu chifukwa ndinkaona kuwerenga Baibulo n’kungotaya nthawi. M'moyo mwanga ndinalibe nthawi yoseka ndi munthu kapena kumvera zopusa.

Anthu ankaona kuti ndine katswiri pa nkhani za malonda. Ndinathandiza anthu ambiri padziko lapansi kuti alemere komanso atchuke. Ena mwa anthu amene ndinawathandizawa ndi oimba odziwika bwino, anthu ochita masewero ndi makanema, komanso ndinatukula ndi kutsatsa malonda a zipangizo zosiyanasiyana zogwiritsidwa ntchito pakhomo. Koma nditakumana ndi zokhoma kwambiri m'moyo wanga ndi pamene ndinatembenuka mtima ndikuyamba  kufalitsa timapepala tonena za Yesu m’misewu, ndinayamba kukhala pamishoni ndikumalalikira uthenga wabwino, komanso ndinayamba kuyendetsa ntchito yosonkhanitsa zakudya n’kumagawira anthu a njala.

Pofika m’zaka za ma 1960, zinali zoonekeratu kuti zinthu zikusokonekera padzikoli. Anthu ambiri anayamba kugwiritsa mankhwala osokoneza bongo, komanso kuchita makhalidwe ambiri oipa. Ndipo ndinkadana ndi zimene hippie movement inkachita ku Hollywood, Sunset komanso padziko lonse lapansi.  N’zoona kuti ngakhale ine amene ndinkachitanso zinthu zina zoipa. Sizinkandikhudza ngati anthu akuchita zinthu zoipa, bola ngati ankachita zinthuzo pamalo osaonekera kwa mabanja ndi ana. Kwa ine dziko linali litatha, litafa, litauma, litanyasa kwambiri, ndiponso litayipiratu. Ndinkaona kuti palibe chifukwa chilichonse chokhalira ndi moyo.9 Ndinkakhulupirira kuti anthu enanso padzikoli akuona chimodzimodzi ngati ine, ndipo ndidayamba kugwiritsanso ntchito mankhwala osokoneza bongo pofuna kuthawa mavuto. Ndinkaona kuti atsogoleri a matchalitchi ndi anthu achinyengo; ndipo aliyense ankatha kuona bwinobwino zimenezi. Dziko lonse linali lakufa ndi uchimo komanso ntchito zake zoipa.10 Dziko lonse linali ngati chigwa chachikulu cha mafupa owuma, chimene Ezekieli anaona.11

Ndili mu ofesi ku Beverly Hills, ndinakumana ndi Yesu m’njira yodabwitsa kwambiri. Palibe amene angamvetse m'mene ndinkaopera komanso pa nthawi yomweyo m'mene ndinasangalalira pamene Mulungu anadzisonyeza kuti Iye ndiponso Mwana wake alipodi. Ndinasangalala kwambiri nditadzadzidwa ndi Mzimu Wake Woyera komanso nditamva mawu Ake amphamvu amene anandikuta thupi langa lonse. Maonekedwe ake anali aulemerero komanso osangalatsa. Ndinadzazidwa kwambiri ndi Mzimu wake Woyera ngati kuti ndagwiridwa ndi dzanja la mphamvu la Mulungu. Kenako ndinamva mawu ake akundiuza kuti: “Imirira ndipo uwuze anthu amene ali m’chipinda chino zokhudza Ambuye Yesu Khristu. Uwawuzenso kuti Iye adzabweranso padzikoli ndipo sadzafanso.” Pamene Mzimu wake Woyera unabwera muofesiyo n’kundidzaza, ndinatha kuzindikira kuti Iye ndi wanzeru zodabwitsa.12 Iye anali paliponse ndi mumpweya momwe. Ankadziwanso chilichonse chimene chinachitikapo m’mbuyomu komanso chimene chidzachitika m’tsogolo.13 Ndinali wamanyazi chifukwa ndinkadziwa kuti Iye akudziwa chilichonse chimene chinachita pamoyo wanga. Kenako anandisonyeza kuti Kumwamba komanso Gehena zilipodi. Ndinkadziwiratu kumene ndikadapita ndikadapanda kuchita zimene Iye ananena...ndipo sikunali Kumwamba.

Ngakhale kuti ndinkaopa kwambiri,14 ndinasangalalanso kudziwa kuti Mulungu ndi weniweni ndiponso ndi wamoyo. Iye ali monga m'mene aneneri komanso atumwi anamufotokozera. Iye sanasinthe ngakhale pang’ono kuyambira nthawi imene analenga kumwamba, dziko lapansi, ndiponso zinthu zonse zimene zilimo.15 Nthawi yomweyo ndinadziwiratu kuti nthawi zonse ndizimuopa, kumulemekeza, kumukonda, ndiponso kumutumikira. Ndinadziwa kuti ndidzafunitsitsa kukhala ndi moyo, kuzunzidwa, ndi kumufera Iye, ndikupanga zonsezi mosangalala, ndi chimwemwe chonse.16

Mulungu atandimasula mu ofesiyo, ndinamufunsa kuti, “Kodi Mukufuna kuti ndichite chiyani? Ndichita chilichonse chimene Munganene.” Koma sindinayankhidwe, choncho ndinaganiza kuti akufuna ndipite kutchalitchi. Ndinkaganiza kuti tchalitchi chachikulu kwambiri n’chimene chilinso chabwino kwambiri, choncho ndinapita kutchalitchi chachikulucho, koma sindinapeze Mulungu kumeneko. Kenako ndinapita kumatchalitchi ena, koma kumenekonso kunalibe Mulungu. Ndiyeno ndinayamba kuwerenga mabuku okhala ndi zithunzi m’zikuto zake. Zithunzizo zinali za anthu owoneka ngati anzeru komanso opemphera, okhala ndi ndevu zitalizitali komanso ovala zovala zachipembedzo. Koma ndinadziwa kuti zimene zinali m’mabukuwo zinali zolakwika chifukwa zinkasonyeza kuti Mulungu si woyenera kumuopa,17 zoti Mulungu saopseza anthu, ndiponso zoti munthu angachite tchimo lililonse koma sakawotchedwa ku Gehena.18 Sikuti ine ndinkafuna Mulungu wotere, koma ndinkafuna kupeza Mulungu amene anandiopseza,19 Mulungu amene anandionetsa Kumwamba komanso ku Gehena, Mulungu amene anandichititsa kuchita zinthu zomwe sindinachitepo, zomwe sindinkafuna kuchita.

M’mbuyomu, ndinkaganiza kuti chowonadi sichingapezeke mu Baibulo chifukwa pali mabaibulo ambirimbiri. Ndinkakhulupirira kuti chilichonse chimene anthu ambiri angachikhulupirire sichingakhale chanzeru chifukwa ndinkaona kuti anthu onse ndi opusa. Kenako ndinayamba kuwerenga Baibulo ndipo ndinazindikira njira yopezera chipulumutso komanso ndinapeza malangizo opezera moyo wosatha. Malangizowo amafotokozanso m'mene munthu angakulire mwa Khristu komanso mumzimu n’kukhala mtumiki wake wokhulupirika.20

Nditangoyamba kuwerenga Baibulo kwa nthawi yoyamba, ndinamva mphamvu ya Mulungu yomwe ija ndinamva ku ofesi ya ku Beverly Hills ija itadzadzanso mwa ine. Kenako Mulungu anandionetsanso masomphenya ena a Kumwamba ndi ku Gehena.21 Ndinafuula kwa Mulungu kuti: “Ambuye, musanditumize ku Gehena!” Kenako ndinaona Kumwamba ndipo ndinamva mtendere wa Kumwamba.22 Ngakhale kuti muuzimu ndinali wosaona, wamaliseche, komanso wamng’ono, ndinamuwuza Mulungu ndingasankhitsitse kukhalabe wosaona, wamaliseche, ndiopanda ntchito ngati atangondilola kumakhalabe ndi mtendere wa Kumwamba umenewu mpaka muyaya. Kenako ndinaonanso Gehena ndipo ndinakuwa kuti Mulungu andichitire chifundo komanso andikhululukire. Ndipo mphamvu ya Atate, Mwana, ndi Mzimu Woyera inalowa m’thupi langa.23 Kudzera m’chikhulupiriro changa mwa Yesu ndi magazi ake amene anakhetsedwa chifukwa cha ine, ndiponso chifukwa cha chikhulupiriro changa, mawu a Mulungu amene ndinawamva ndi kuwatsatira,24 ndinamva m’thupimu kuti tchimo lililonse limene ndinachitapo m’mbuyomu likuchoka.25 Zitatero, ndinayamba kumva kuti ndine woyera.26 Chinthu china chake chosangalatsa chinandichitikira, ndipo amene anandichitira chinthucho ndi Khristu Yesu, “Woyera wa Israeli.”27 Ndinasangalala kwambiri nditamasulidwa ku uchimo n’kulandira mphamvu imene imandithandiza kuti ndisamachimwe, ndipo ndikufunitsitsa kudziwitsa anthu onse padziko lapansi kuti nawonso amudziwe ndi kudzapeza moyo wosatha.

Ngakhale kuti ndakhala mu utumiki wa Khristu kuyambira mu 1964, ndikuonabe kuti umoyo wauzimu wochokera Kumwamba ukuyikidwa m’mafupa owuma aja nthawi iliyonse imene ndawerenga Baibulo. Mawu a Mulungu athandiza kuyikanso uwisi m’mafupa amene poyamba anali owuma, kuikamo minofu ndi khungu lomwe ndi chitetezo chauzimu. Mawu aliwonse a Mulungu athandiza Khristu alowe mumtima mwanga. Panopa ndikumvabe Mawu aliwonse a Mulungu amene analowa m’moyo mwanga kudzera mwa Mzimu Woyera. Mawu amenewa amandithandiza kukhala ndi mphamvu zozimitsira mivi yoyaka moto imene Satana wakhala akundiponyera pa zaka zonsezi. Ndikudziwa bwino kuti “ndife oposa ogonjetsa”28 mwa Khristu Yesu, ndipo “timamudalira ndi mtima wonse.”29 Ndikudziwanso bwino kwambiri kufunika kotsatira Mawu aliwonse a Yesu, amene iye anawalankhula atatsala pang’ono kukwera Kumwamba mumtambo. Yesu ananena mawu akuti, “Pitani m’dziko lapansi, mukalalikire uthenga wabwino ku chilengedwe chonse.”30 (Kalalikireni kwa fupa lililonse lowuma, kutanthauza anthu amene ndi akufa mumzimu n’cholinga choti “amve Mawu a Ambuye.”31)

“Iye amene akhulupirira n’kubatizidwa adzapulumuka, koma iye amene sakhulupirira, adzawonongedwa.”32

Ngati inuyo muli ngati ine ndipo simukufuna kudzawonongedwa, koma mukufuna kudzapulumuka, nenani pemphero ili kwa Mulungu:

Prayer

AMBUYE wanga komanso MULUNGU wanga, ndichitireni chifundo ndine munthu wochimwa.1 Ndikukhulupirira kuti YESU KHRISTU ndi MWANA wa MULUNGU wamoyo.2 Ndimakhulupiriranso kuti IYE anafera pamtanda ndipo anakhetsa mwazi WAKE wamtengo wapatali ndi cholinga choti machimo anga onse akhululukidwe.3 Ndikukhulupiriranso kuti MULUNGU anaukitsa YESU kwa akufa pogwiritsa ntchito mphamvu ya MZIMU WOYERA,4 ndiponso kuti IYE anakhala kudzanja lamanja la MULUNGU ndipo panopa akumva pemphero langa lolapali.5 Ndikutsegula zitseko za mtima wanga, ndipo ndikukuyitanani kuti mulowe mumtima mwanga, inu AMBUYE YESU.6 Tsukani machimo anga ambirimbiri achoke onse mu mwazi wamtengo wapatali umene INU munakhetsa m’malo mwanga pamtanda wa ku Kavari.7 Ndikudziwa kuti mundimvera pemphero langali AMBUYE YESU; INU mukhululukira machimo anga ndi kupulumutsa moyo wanga. Ndikudziwa izi chifukwa MAWU ANU, Baibulo, limanena zimenezi.8 MAWU ANU amati INUYO simudzakana kumvetsera pemphero la munthu aliyense, ndipo ine ndili m’gulu la anthu amenewo.9 Choncho, ndikudziwa kuti INUYO mukundimvetsera pamene ndikupemphera ndipo ndikudziwanso kuti INUYO mundiyankha komanso mundipulumutsa.10 Ndipo ndikukuthokozani AMBUYE YESU, chifukwa chopulumutsa moyo wanga, ndipo ndisonyeza kuyamikira mwa kuchita zinthu zimene INUYO munalamula komanso kupewa kuchita uchimo.11

Pambuyo pa chipulumutso, YESU ananena kuti munthu ayenera kubatizidwa pomizidwa thupi lonse m’madzi, m’dzina la ATATE, ndi la MWANA, ndi la MZIMU WOYERA.12 Muziphunzira mwakhama Baibulo la Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu, [King James Version] ndipo muzichitazimene Baibulolo limanena.13

AMBUYE akufuna kuti inuyo muziwuza ena za chipulumutso chanu. Mungathe kukhala wofalitsa uthenga wabwino wa M’busa Tony Alamo. Tizikutumizirani mabuku mwaulere. Imbani foni kapena tumizani imelo kwa ife kuti mudziwe zambiri. Tikukupemphani kuti muwuzeko ena uthengawu.

Ngati mukufuna kuti dziko lipulumutsidwe monga m’mene YESU akulamulira, mukufunika kupereka chakhumi kwa MULUNGU. MULUNGU anati, “Kodi munthu angabere MULUNGU? Inde, mwandibera kale. Koma akuti, Ife tikumubera bwanji MULUNGU? Mu chakhumi ndi mu zopereka. Anthuwo ndi otembereredwa chifukwa akundibera, ngakhale mtundu wonsewu [dziko lonse lapansi]. Bweretsani nonse chakhumi [‘chakhumi’ ndi gawo limodzi la magawo khumi (10%) ya malipiro anu] m’nkhokwe zanga n’cholinga choti pakhale nyama [chakudya cha Uzimu] mu nyumba
YANGA [anthu opulumutsidwa] kuti mundiyese, akutero AMBUYE wa MAKAMU, kuti muone ngati sindidzakutsegulirani mazenera a Kumwamba ndi kukukhuthulirani madalitso amene mudzasowa malo owalandirira.” Ndipo ndidzadzudzula anthu okudyerani masuku pamutu ndipo sadzawononga zipatso za nthaka yanu; ngakhalenso mphesa wanu sudzalephera kubala zipatso pa nyengo yake m’minda yanu, watero AMBUYE wa MAKAMU. Ndipo mitundu yonse idzakutchani odala: chifukwa
dziko lanu lidzakhala labwino, watero AMBUYE wa MAKAMU”(Malaki 3:8-12).


Chichewa/Nyanja Alamo Literature

Ngati mukufuna kudziwa zambiri kapena ngati mukufuna mabuku kapenanso nkhani zina zimene zimakusangalatsani, tiimbireni foni kapena tilembereni.

Tony Alamo, World Pastor
Tony Alamo Christian Ministries Worldwide
P. O. Box 2948
Hollywood, CA 90078

Lamya ya pemphero ndi uthenga maola 24: (661) 252-5686

Tony Alamo Christian Ministries Worldwide imalandira anthu onse ndipo imapereka zinthu zofunika Kwa onse amene ali ku U.S. amene akufunitsitsadi kuti ayambe kutumikira AMBUYE ndi mtima wawo wonse moyo wawo wonse ndi mphamvu zawo zonse.

Mapemphero amachitika mu Mzinda wa New York Lachiwiri lili lonse nthawi ya 8 Koloko usiku ndi madera ena usiku okhaokha. Chonde imbani foni kuti mumve zambiri: +1 (908) 937-5723. ZAKUDYA ZIMAGAWIDWA PA MAPETO PA MAPEMPHERO ALI WONSE

Funsani buku la M’busa Alamo, lakuti Mesiya, losonyeza KHRISTU kuyambira ku Chipangano Chakale mu maulosi oposa 333.

Khalani wogwira ntchito yokolola miyoyo ya anthu pakukhala ogawira mabuku a M’busa Alamo. Mabuku ndi zinthu zonse zomvetsera n’zaulere, ndipo simulipira ndalama yotumizira

M’BUKU ILI MULI CHIKONZERO CHENICHENI CHA CHIPULUMUTSO (Machitidwe 4:12).
MUSALITAYE, PATSANI ENA KUTI AWERENGE.

Anthu amene muli m’mayiko ena, tikukulimbikitsani kuti mumasulire n’chinenero chanu mabukuwa. Ngati mukusindikizanso bukuli, musaiwale kuika mawu ali m’munsiwa omwe ndi okhudzana ndi zamalamulo:

© Copyright November 1995, March 2012   All rights reserved World Pastor Tony Alamo   ® Registered November 1995, March 2012


Mawu a m’musi:

1. Ezek. 36:1, 4 return

2. Ezek. 37:3, ochokera ku Chihe. return

3. Ezek. 37:4-5, ochokera ku Chiaramu return

4. Ezek. 37:11 return

5. Gen. 17:4-16, 22:18, 26:4, 46:3, 48:19, 49:10, Eks. 19:6, 32:10, Sal. 22:27, Yes. 2:2, Yoh. 11:51-52, Mac. 10:34-35, Aef. 1:10, Aheb. 8:8-12, 1 Pet. 2:9-10, Chiv. 5:9, 14:6 ndi ena ambiri return

6. Yoh. 15:1, Aro. 11:17, 19, 23, 24, Chiv. 7:4 return

7. 1 Pet. 2:9 return

8. Aro. 15:12, 1 Akor. 15:15, 16, Akol. 2:12, 3:1, 1 Ates. 4:16, Chiv. 20:5-6 return

9. Mat. 13:39, chap. 24, 1 Akor. 15:24, Aheb. 9:26, 1 Pet. 4:7 return

10. Aef. 2:1, 5, Akol. 2:13 return

11. Ezek. 37:1 return

12. Num. 24:16, 1 Sam. 2:3, Yobu 21:22, Sal. 32:8, Miy. 2:6, 3:20, 9:10, Luka 1:77, Aro. 11:33, 1 Akor. 1:25, 2:16, 3:19, 2 Akor. 4:6 return

13. Sal. 44:21, 94:11, Yes. 46:9-10, 1 Akor. 3:20, 1 Yoh. 3:20, Chiv. 21:6, 22:13 return

14. Gen. 35:5, Lev. 26:16, Yobu 31:23, Yer. 32:21, Ezek. 32:32, 2 Akor. 5:11 return

15. Gen 1:1, Mal. 3:6, Mac. 4:24, 2 Akor. 5:11, Aheb. 13:8 return

16. Sal. 5:11, 35:19, Yes. 51:11, 61:10, Yoh. 16:33, Mac. 2:28, 20:24, Aro. 12:8, 15:13, 2 Akor. 8:12 return

17. Gen. 22:12, Sal. 112:1, Miy. 13:13, 14:16, 28:14, 31:30, Mlal. 7:18 return

18. Miy. 8:36, Ezek. 18:2, 4, Chiv. 19:20, 20:10, 14, 15, 21:8 return

19. Gen. 2:17, 6:7, 9, 13, Ex. 20:5, 32:33, 34:7, Ezek. 3:18, 18:20, Mat. 8:12, 22:13, Marko 16:16, Chiv. 2:5, 16, 22-23, 3:3, 20:15 return

20. Yoh. 4:35-36, 15:5, 8, 15-16, Chiv. 14:18 return

21. Yes. 5:14, 14:9, Luka 16:22-31, Mac. 7:55-56, Chiv. 4:1-11, 14:10-11, 15:1-4, 20:10, 21:2-5, 10-27, 22:1-5 return

22. Aro. 5:1, Aef. 2:14, Afil. 4:7, Akol. 3:15, 1 Ates. 5:23, 2 Ates. 3:16 return

23. Lev. 26:11-12, Yoh. 14:16, 2 Akor. 6:16, 1 Pet. 2:5, 1 Yoh. 3:24 return

24. Hab. 2:4, Mat. 17:20, Luka 7:50, Mac. 20:21, 26:18, Aro. 1:17, 3:28, 5:2, 10:17, 11:20, Gal. 2:16, 3:11, Aef. 2:8, 3:17, Aheb. 10:38 return

25. Marko 14:24, Yoh. 6:53, Mac. 20:28, Aro. 3:25, 5:9, Aef. 1:7, 2:13, Akol. 1:14, 20, Aheb. 9:12, 14, 22, 1 Pet. 1:18-19, Chiv. 1:5, 5:9 return

26. Aheb. 10:19-22, 1 Yoh. 1:7, Chiv. 1:5, 7:14 return

27. Sal. 89:18, Mac. 3:13-14 return

28. Aro. 8:37, 1 Yoh. 4:3-4 return

29. Akol. 2:10 return

30. Marko 16:15, Luka 14:23 return

31. 2 Maf. 20:16, Yes. 1:10, Yer. 2:4, Ezek. 37:4 return

32. Marko 16:16, 2 Ates. 2:12 return


Prayer Footnotes:

1. Masa. 51:5, Aro. 3:10-12, 23 return

2. Mat. 26:63-64, 27:54, Luka 1:30-33, Yoh. 9:35-37, Aro. 1:3-4      return

3. Mach. 4:12, 20:28, Aro. 3:25, 1 Yoh. 1:7, Chiv. 5:9      return

4. Masa. 16:9-10, Mat. 28:5-7, Marko 16:9, 12, 14, Yoh. 2:19, 21, 10:17-18, 11:25, Mach. 2:24, 3:15, Aro. 8:11, 1 Akor. 15:3-7      return

5. Luka 22:69, Mach. 2:25-36, Aheb. 10:12-13   return

6. 1 Akor. 3:16, Chiv. 3:20      return

7. Aef. 2:13-22, Aheb. 9:22, 13:12, 20-21, 1 Yoh. 1:7, Chiv. 1:5, 7:14      return

8. Mat. 26:28, Mach. 2:21, 4:12, Aef. 1:7, Akol. 1:14      return

9. Mat. 21:22, Yoh. 6:35, 37-40, Aro. 10:13      return

10. Aheb. 11:6     return

11. Aheb. 5:14, 8:11, Aro. 6:4, 1 Akor. 15:10, Chiv. 7:14, 22:14      return

12. Mat. 28:18-20, Yoh. 3:5, Mach. 2:38, 19:3-5   return

13. Deut. 4:29, 13:4, 26:16, Yoswa 1:8, 22:5, 2 Tim. 2:15, 3:14-17, Yakobo 1:22-25, Chiv. 3:18 return