ANGELO A KUMWAMBA KUYANDAMA MALO AMODZI M’MLENGALENGA PAMWAMBA PA DZIKO LATHU

yolembedwa ndi Tony Alamo

“Magareta a MULUNGU alipo 20,000, ngakhale masauzande a angelo: AMBUYE ali pakati pawo” (Masalimo 68:17). Ndichachidziwikire kuti magareta a MULUNGU ndi mbale zouluka za lero, zimene zimadziwika kuti maUFO. Sizochokera ku dziko lina lili lonse, koma ndi angelo a MULUNGU, zimene kwa zaka zambiri zakhala zikuteteza dziko ku milandu yolakwira lamulo la MULUNGU ndi kulakwira amene adzalandire chipulumutso monga cholowa chawo.1

Ahebri 1:10-14 akuti, “Ndipo, INU, AMBUYE, pachiyambi munaika maziko a dziko lapansi; ndipo kumwamba ndi ntchito ya manja ANU: Zimenezi zidzatha; koma INU mudzakhalapo mpaka muyaya; ndipo zonsezi zidzatha ngati mmene malaya akunja amathera; INU mudzapindapinda zinthu zimenezi ngati mkanjo, ndipo zidzasinthidwa: koma INU simudzasintha, ndipo zaka zamoyo WANU sizidzatha. Koma kodi ndi mngelo uti amene IYE anamuuzapo, kuti Khala ku dzanja LANGA lamanja [monga IYE ananenera kwa KHRISTU yekha], kufikira nditaika adani AKO monga chopondapo mapazi AKO? Kodi iwo onse si mizimu, yotumidwa kukatumikira amene adzalandire chipulumutso monga cholowa chawo?”

Kupanda magareta a MULUNGU (amene anthu ambiri amawatchula kuti maUFO), mizimu yotumikira ya MULUNGU ikanakwanitsa bwanji kuyang’anira ntchito zabwino zonse za oyera mtima ndi zachinyengo zochitidwa pa dziko lapansi ndi anthu oipa maola 24 tsiku lili lonse? MULUNGU angadziwe bwanji, ngakhale IYE ali MULUNGU odziwa chili chonse, ndi angelo ati amene IYE angatumize ndipo ndi liti lomwe angawatumize kukadalitsa oyera mitima kapena kuchenjeza, kutembelera, kapena kuononga oipa?

Mwa chitsanzo, mu Genesis 32:12 MULUNGU ananena kwa Yakobo, amene IYE patsogolo pake anamutcha Israel, “Ndidzakuchitira iwe ubwino ndithu, ndidzakuyesa mbewu yako monga mchenga wa panyanja yayikulu, umene sungathe kuwerengeka chifukwa cha unyinji wake.” Koma MULUNGU amadziwa chimene chinali m’maganizo a Mfumu Davide pamene mfumu inaganiza zowerenga ana onse a Israeli. Umu ndi mmene zinayambira. 1 Mbiri 21:1-2 akuti, “Pamenepo Satana anaukira Israeil, nasonkhezera Davide awerenge Israel [chimene MULUNGU ananena kuti sichingawerengeke chifukwa ndiochulukitsitsa mosawerengeka (Ahebri 11:12)]. Ndipo Davide anati kwa Yoabu ndi kwa akulu [atsogoleri] a anthu, Pitani, kawerengeni a Israeli kuchokera ku Beersheba kufikira ku Dani; ndipo mundibweletsere chiwerengero, kuti ndidziwe.” Pakumvera Satana, Mfumu Davide anatsogoleredwa mumtima mwake, ngati momwe Hava anatsogoleredwa mumtima mwake, kunena m’mitima yawo, “Ndidzakhala ngati MULUNGU WAM’MWAMBAMWAMBA, ndipo ndidzadziwa chiwerengero monga MULUNGU adziwira chiwerengero.” Akanakhala kuti MULUNGU anakwiya kwambiri ndi Hava komanso Adamu posamumvera IYE kapena kumvera malamulo AKE mpaka IYE kutembelera moyo uli wonse wokhala padziko lapansi ndi imfa, Gehena, ndiponso Nyanja ya Moto wamuyaya, ndi chifukwa chiyani MULUNGU analola Davide osalangika chifukwa cha kusamvera ndi kuchimwa pakumvera ndi kutsatira malamulo a Satana?2 MULUNGU amalemekeza munthu.3 Ngati anatemberera Adamu ndi Hava pakusamumvera IYE, ndipo ngati anatemberera Mfumu Davide, yemwe IYE amamukonda, pakusamumvera IYE, IYE adzatemberera inu ndi ine ndi wina aliyense chifukwa chosamumvera IYE.4

Davide atalamulira Yoabu kuti awerenge anthu a Israel, Yowabu anayankha Davide kuti, “AMBUYE aonjezera anthu AKE monga ali kazana: koma, mbuyanga mfumu, sali onse anyamata akapolo a mbuyanga? nanga afuniranji chinthuchi mbuyanga, adzapalamulitsa Israeli bwanji? aonjezera pa anthu AKE monga ali kazana: koma, mbuyanga mfumu, sali onse anyamata akapolo a mbuyanga? Nanga afuniranji chinthuchi mbuyanga? N'chifukwa chiyani iye adzakhala chifukwa cha uchimo kwa Israeli? Koma mau a mfumu anamlaka Yoabu. Natuluka Yoabu, nakayendayenda mwa Aisraeli onse, nadza ku Yerusalemu. Ndipo Yoabu anapereka kwa Davide chiwerengo cha anthu owerengedwa. Ndipo Aisraeli onse anali zikwi mazana khumi ndi limodzi [1,100,000] osolola lupanga: ndi Yuda anali zikwi mazana anai mphambu makumi asanu ndi awiri [470,000] akusolola lupanga. Koma sanawerenge Alevi ndi Abenjamini pakati pao: pakuti mau a mfumu anam’nyansira Yoabu [monga izo zinali kwa MULUNGU].

“Ndipo Mulungu anaipidwa nacho chinthuchi; kotero IYE anakantha Israeli. Pamenepo Davide anati kwa MULUNGU, Ndachimwa kwakukuru, chifukwa ndachita chinthu ichi: koma tsopano, ndipempha INU, muchotse mphulupulu ya kapolo WANU; pakuti ndachita kopusa ndithu. Ndipo YEHOVA ananena ndi Gadi, mlauli wa Davide [mneneri], ndi kuti, Kanene kwa Davide, kuti, Atero YEHOVA, Ndikuikira zitatu [matemberero atatu—sankha limodzi]: dzisankhireko chimodzi, chimene ndikuchitire iwe. Nadza Gadi kwa Davide, nanena naye, Atero YEHOVA, Sankha pakati pa zaka zitatu za njala; kapena miyezi itatu ya kuthedwa pamaso pa adani ako, ndi kuti lupanga la adani ako likupeze; kapena masiku atatu lupanga la YEHOVA, ngakhale mliri, m'dzikomo, ndi mngelo wa YEHOVA kuononga malire onse a Israyeli. Ndipo Davide anati kwa Gadi, Ndapsinjika kwambiri: ndigwere tsopano m'dzanja la YEHOVA; pakuti zifundo ZAKE zichulukadi: koma ndisagwere m'dzanja la munthu.

“Momwemo YEHOVA anatumiza mliri pa Israeli: ndipo adagwapo amuna zikwi makumi asanu ndi awiri a Israeli. Ndipo MULUNGU anatuma MNGELO [mbale imodzi youluka yoyendetsedwa ndi MNGELO mmodzi yekha] ku Yerusalemu kukamuononga: ndipo [MNGELO] akuononga, YEHOVA anali kupenya, naleka IYE choipachi, nati kwa  [Oyang’anira] MNGELO wakuononga, Chakwanira, bweza dzanja lako tsopano. Ndipo [Oyang’anira] MNGELO wa YEHOVA anaima pa dwale la Orinani Myebusi. Ndipo Davide anakweza maso ake, naona MNGELO wa YEHOVA [Oyang’anira] alikuima pakati pa dziko ndi thambo, ali nalo lupanga losolola m'dzanja lake lotambasukira pa Yerusalemu.

“Pamenepo Davide ndi akulu a Israeli, obvala ziguduli [izi zikutanthauza kuti anali kusala], anagwa nkhope zao pansi. Ndipo Davide anati kwa MULUNGU, Si ndine nanga ndalamulira kuti awerenge anthu? Inde, ndine amene ndachimwa ndi kuchita choipa ndithu; koma nkhosa izi, zinachitanji? dzanja LANU, ndikupemphera kwa INU, O YEHOVA MULUNGU wanga, munditsutse ine, ndi nyumba ya atate wanga; koma musatsutse anthu ANU, ndi kuwachitira mliri. Pamenepo MNGELO wa YEHOVA anauza Gadi [mneneri] kuti anene kwa Davide, kuti Davideyo akwere pamwamba, ndi kukonza guwa la nsembe kwa YEHOVA pa dwale la Orinani Myebusi. Ndipo Davide anakwera monga mwa mau a Gadi, amene adawanena m'dzina la YEHOVA. 

“Pocheuka Orinani, anaona MNGELO; ndi ana ake amuna anai anali naye atadzibisa [monga achitira anthu a lero nthawi zina akaona mbale zouluka, maUFO, ANGELO a MULUNGU, zikuyandama mlengalenga pamwamba pawo; izi sizochokera ku mapulaneti ena, koma zochokera Kumwamba!]. Koma Orinani anali kupuntha tirigu. Ndipo pofika Davide kwa Orinani, Orinaniyo anapenyetsa naona Davide, naturuka kudwale, nawerama kwa Davide [pamene Orinani anaona MNGELO kenako Davide, anamva mphamvu zochuluka zolumikizitsa MNGELOyo ndi Davide. Orinani anachita mantha, ndipo anagwada pamaso pa Davide] atagwetsa nkhope yake pansi. Ndipo Davide tsono anati kwa Orinani, Ndipatse padwale pano, kuti ndimangepo guwa la nsembe la YEHOVA: ndipo undipatse pa mtengo wake wonse: kuti mliri ulekeke pa anthu. Ndipo Orinani anati kwa Davide, Mulitenge, ndipo mbuye wanga mfumu ichite chomkomera m'maso mwake: taonani, ndikupatsani ng'ombe za nsembe zopsereza, ndi zipangizo zopunthira zikhale nkhuni, ndi tirigu wa nsembe yaufa; ndizipereka zonse. Koma mfumu Davide anati kwa Orinani, lai; koma ndidzaligula pa mtengo wake wonse: pakuti sindidzatengera YEHOVA chili chako, kapena kupereka nsembe yopsereza yopanda mtengo wake. Choncho Davide anapatsa Orinani chogulira malowa golidi wa masekeli mazana asanu ndi limodzi kulemera kwake. Ndipo Davide anamangira YEHOVA guwa la nsembe komweko, napereka nsembe zopsereza ndi nsembe zoyamika, naitana kwa YEHOVA; ndipo IYE [MULUNGU] anamuyankha iye kuchokera m'Mwamba ndi moto pa guwa la nsembe yopsereza. Ndipo Yehova anauza MNGELO; ndipo anabwenzeretsa lupanga lake m'chimake.

“Nthawi yomweyi pakuona Davide kuti YEHOVA anamuvomereza pa dwale la Orinani Myebusi, anaphera nsembe pomwepo. Pakuti kachisi wa YEHOVA, amene Mose anapanga m'chipululu, ndi guwa la nsembe yopsereza, zinali pa msanja wa ku Gibeoni nthawi yomweyi. Koma Davide sanathe kumuka kukhomo kwake kufunsira kwa MULUNGU: pakuti anaopa lupanga la MNGELO wa YEHOVA” (1 Mbiri 21:3-30). Pali malemba ena amene amasonyeza kuti Mulungu amagwiritsa ntchito angelo kutemberera ndi kuwononga.5

Mneneri wakale Nahumu anafotokoza misewu ikuluikulu ndi magalimoto za lero m'njira yokhayo yomwe iye ankadziwa. Nahumu 2:4 amati, “Magareta achita mkokomo m'miseu, akankhana m'makwalala: maonekedwe ao akunga miuni, athamanga ngati mphezi.” Awa ndi maulosi a nthawi yotsiriza a galimoto ndi misewu ikuluikulu.

Palibe moyo pa pulaneti ina iliyonse, pa cholengedwa china chilichonse cha MULUNGU. Choncho, ndikupusa ndi bodza lamkunkhuniza mwamtheradi kuganiza kuti mbale zowuluka ndi maUFO ndizochokera ku planeti ina ililonse. Izo zikuchokera Kumwamba.

Koposa zonse, MULUNGU amafuna kukhulupiridwa, ndipo IYE akudziwa kuti inu simumukhulupirira IYE pamene inu muswa malamulo AKE. Izi n'zimene MULUNGU ananena zokhudza Kumwamba KWAKE ndi dziko LAKE lapansi. Mu Genesis 1:14-15, “Ndipo MULUNGU anati, Pakhale zounikira pa thambo la kumwamba zakulekanitsa usana ndi usiku; zikhale zizindikiro, ndi nyengo [za padziko lapansi pano, osati pa planeti ina ili yonse], ndi masiku, ndi zaka [izinso, za planeti ya dziko lapansi pano pokha]: Ndipo zikhale zounikira m'thambo la kumwamba kuti ziunikire pa DZIKO LAPANSI [osati pa Mars, Jupiter, Mercury, kapena planeti ina ili yonse]: ndipo kunatero.” Musaganize kuti inu mungazembe zinyengo ndi ziwawa zomwe tsopano zikuchitika ndipo zidzakula pa chomwe mumachitchula “mama dziko.” Musaganize mukupita ku maplaneti ena kukakhala, pakuti moyo sungathe kuchirikizidwa kwina kulikonse. Inu simudzapeza mtendere padziko lapansi chifukwa ndife anthu a chinyengo, ndipo popanda YEHOVA mu mitima yathu, nthawi zonse tidzakhala achinyengo. Komanso, chonde iwalani kuti maUFO awa, mbale zowuluka, OYANG'ANIRA, ANGELO, akuchokera ku maplaneti ena. Ngati inu mukukhulupirira zonama zimenezi, MULUNGU wakutumizirani kale machitidwe a kusocheretsa monga IYE akunenera mu 2 Atesalonika 2:8-12: Ndipo pamenepo adzabvumbulutsidwa Woipayo [mdierekezi, Satana, Otsutsa Khristu], amene AMBUYE adzamthera ndi MZIMU wa pakamwa PAKE, nadzamuononga ndi maonekedwe owala a kudza KWAKE: Ngakhale iye, amene kudza kwake kuli monga mwa machitidwe a Satana mu mphamvu yonse [mphamvu zofooka ndi zopemphetsa zonse za uSatana], ndi zizindikiro ndi zozizwa zonama [zonama monga zonena kuti ANGELO kapena maUFO ndiochokera ku maplaneti ena, ndipo kuti kuli moyo ku maplaneti ena, ndikuti posachedwa mudzatha kuzemba chinyengo choipa cha dziko lino lapansi ku maplaneti ena], ndi m'chinyengo chonse [kunena mabanja a amuna kapena akazi okhaokha sivuto, kutaya mimba, kupha mwa chiwembu, sivuto,6 kugonana akazi okhaokha ndi kugonana amuna okhaokha sivuto,7 chiwerewere,8 ndi kugonana usanalowe m’banja sivuto,9 kuledzera ndi mowa kapena mankhwala ozunguza bongo sivuto,10 zisudzo sivuto,11 kuba12 ndi mwano sivuto,13 osakonda YEHOVA MULUNGU wako ndi mtima, moyo, nzeru, ndi mphamvu zako zonse sivuto,14 osatumikira AMBUYE sivuto, ndipo kusilira sivuto15] cha chosalungama kwa iwo akuonongeka; popeza chikondi cha choonadi sanachilandire, kuti akapulumutsidwe iwo. Ndipo n’chifukwa chake MULUNGU adzatumiza kwa iwo machitidwe a kusocheretsa, kuti akhulupirire bodza [bodza ngati lonena kuti maUFO ndiochokera ku maplaneti ena, ngati kuti kuli moyo ku mapulaneti ena]: Kuti aweruzidwe onse amene sanakhulupirira choonadi, komatu anakondwera ndi chosalungama.”

Tiyeni tibwelere ku Genesis 1: “Ndipo MULUNGU anapanga zounikira zazikulu ziwiri; chounikira chachikuru chakulamulira usana [Dzuwa], chounikira chaching'ono chakulamulira usiku [Mwezi]: IYE anapanganso ndi nyenyezi zomwe. Ndipo MULUNGU adaika zimenezo m'thambo la kumwamba kuti ziunikire pa DZIKO LAPANSI [osati pa pulaneti ina iliyonse], Nizilamulire usana ndi usiku, nizilekanitse kuyera ndi mdima: ndipo MULUNGU anaona kuti kunali kwabwino” (Genesis 1:16-18). 

Mukukhulupirira chiani tsopano? Kodi inu mukukhulupirira zinthu zabwino kapena zoipa? Kodi inu mukukhulupirira MULUNGU anatipanga ife kuchokera mu dothi la pansi, kapena mukukhulupirira asayansi? Kodi mumakhulupirira MULUNGU kapena makina a carbon dating? M'mawu ena, kodi inu mukukhulupirira kuti dziko lapansi lili ndi zaka 6,000 monga YEHOVA ananenera, kapena mukukhulupirira bodza kuti dziko lapansi lili ndi zaka mamiliyoni kapena mabiliyoni monga achikunja amanenera? Ngati inu mukukhulupirira mabodza osati MAWU a MULUNGU, mwalandira machitidwe a kusocheretsa, ndipo muli otembereredwa.16 Tikukhulupirira, chifukwa cha inu, zimenezi sizoona. Ngati mukufuna kupulumutsidwa ndi kukhala muyaya Kumwamba ndi MULUNGU ATATE, MWANA, ndi MZIMU WOYERA, pamodzi ndi onse amene amakhulupirira MULUNGU kudzera mwa MWANA WAKE KHRISTU YESU, nenani pemphero ili:

Prayer

AMBUYE wanga komanso MULUNGU wanga, ndichitireni chifundo ndine munthu wochimwa.1 Ndikukhulupirira kuti YESU KHRISTU ndi MWANA wa MULUNGU wamoyo.2 Ndimakhulupiriranso kuti IYE anafera pamtanda ndipo anakhetsa mwazi WAKE wamtengo wapatali ndi cholinga choti machimo anga onse akhululukidwe.3 Ndikukhulupiriranso kuti MULUNGU anaukitsa YESU kwa akufa pogwiritsa ntchito mphamvu ya MZIMU WOYERA,4 ndiponso kuti IYE anakhala kudzanja lamanja la MULUNGU ndipo panopa akumva pemphero langa lolapali.5 Ndikutsegula zitseko za mtima wanga, ndipo ndikukuyitanani kuti mulowe mumtima mwanga, inu AMBUYE YESU.6 Tsukani machimo anga ambirimbiri achoke onse mu mwazi wamtengo wapatali umene INU munakhetsa m’malo mwanga pamtanda wa ku Kavari.7 Ndikudziwa kuti mundimvera pemphero langali AMBUYE YESU; INU mukhululukira machimo anga ndi kupulumutsa moyo wanga. Ndikudziwa izi chifukwa MAWU ANU, Baibulo, limanena zimenezi.8 MAWU ANU amati INUYO simudzakana kumvetsera pemphero la munthu aliyense, ndipo ine ndili m’gulu la anthu amenewo.9 Choncho, ndikudziwa kuti INUYO mukundimvetsera pamene ndikupemphera ndipo ndikudziwanso kuti INUYO mundiyankha komanso mundipulumutsa.10 Ndipo ndikukuthokozani AMBUYE YESU, chifukwa chopulumutsa moyo wanga, ndipo ndisonyeza kuyamikira mwa kuchita zinthu zimene INUYO munalamula komanso kupewa kuchita uchimo.111

Pambuyo pa chipulumutso, YESU ananena kuti munthu ayenera kubatizidwa pomizidwa thupi lonse m’madzi, m’dzina la ATATE, ndi la MWANA, ndi la MZIMU WOYERA.12 Muziphunzira mwakhama Baibulo la Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu, [King James Version] ndipo muzichitazimene Baibulolo limanena.13

AMBUYE akufuna kuti inuyo muziwuza ena za chipulumutso chanu. Mungathe kukhala wofalitsa uthenga wabwino wa M’busa Tony Alamo. Tizikutumizirani mabuku mwaulere. Imbani foni kapena tumizani imelo kwa ife kuti mudziwe zambiri. Tikukupemphani kuti muwuzeko ena uthengawu.

Ngati mukufuna kuti dziko lipulumutsidwe monga m’mene YESU akulamulira, mukufunika kupereka chakhumi kwa MULUNGU. MULUNGU anati, “Kodi munthu angabere MULUNGU? Inde, mwandibera kale. Koma akuti, Ife tikumubera bwanji MULUNGU? Mu chakhumi ndi mu zopereka. Anthuwo ndi otembereredwa chifukwa akundibera, ngakhale mtundu wonsewu [dziko lonse lapansi]. Bweretsani nonse chakhumi [‘chakhumi’ ndi gawo limodzi la magawo khumi (10%) ya malipiro anu] m’nkhokwe zanga n’cholinga choti pakhale nyama [chakudya cha Uzimu] mu nyumba YANGA [anthu opulumutsidwa] kuti mundiyese, akutero AMBUYE wa MAKAMU, kuti muone ngati sindidzakutsegulirani mazenera a Kumwamba ndi kukukhuthulirani madalitso amene mudzasowa malo owalandirira.” Ndipo ndidzadzudzula anthu okudyerani masuku pamutu ndipo sadzawononga zipatso za nthaka yanu; ngakhalenso mphesa wanu sudzalephera kubala zipatso pa nyengo yake m’minda yanu, watero AMBUYE wa MAKAMU. Ndipo mitundu yonse idzakutchani odala: chifukwa dziko lanu lidzakhala labwino, watero AMBUYE wa MAKAMU”(Malaki 3:8-12).


Chichewa/Nyanja Alamo Literature

Ngati mukufuna kudziwa zambiri kapena ngati mukufuna mabuku kapenanso nkhani zina zimene zimakusangalatsani, tiimbireni foni kapena tilembereni.

Tony Alamo, World Pastor
Tony Alamo Christian Ministries Worldwide
P. O. Box 2948
Hollywood, CA 90078

Lamya ya pemphero ndi uthenga maola 24: (661) 252-5686

Tony Alamo Christian Ministries Worldwide imalandira anthu onse ndipo imapereka zinthu zofunika Kwa onse amene ali ku U.S. amene akufunitsitsadi kuti ayambe kutumikira AMBUYE ndi mtima wawo wonse moyo wawo wonse ndi mphamvu zawo zonse.

Mapemphero amachitika mu Mzinda wa New York Lachiwiri lili lonse nthawi ya 8 Koloko usiku ndi madera ena usiku okhaokha. Chonde imbani foni kuti mumve zambiri: +1 (908) 937-5723. ZAKUDYA ZIMAGAWIDWA PA MAPETO PA MAPEMPHERO ALI WONSE

Funsani buku la M’busa Alamo, lakuti Mesiya, losonyeza KHRISTU kuyambira ku Chipangano Chakale mu maulosi oposa 333.

Khalani wogwira ntchito yokolola miyoyo ya anthu pakukhala ogawira mabuku a M’busa Alamo. Mabuku ndi zinthu zonse zomvetsera n’zaulere, ndipo simulipira ndalama yotumizira

M’BUKU ILI MULI CHIKONZERO CHENICHENI CHA CHIPULUMUTSO (Machitidwe 4:12).
MUSALITAYE, PATSANI ENA KUTI AWERENGE.

Anthu amene muli m’mayiko ena, tikukulimbikitsani kuti mumasulire n’chinenero chanu mabukuwa. Ngati mukusindikizanso bukuli, musaiwale kuika mawu ali m’munsiwa omwe ndi okhudzana ndi zamalamulo:

© Copyright March 2013  All rights reserved World Pastor Tony Alamo  ® Registered March 2013


Makalata opita kwa M’busa Alamo

Malawi
Okondeka mwa Khristu,
Moni mwa Ambuye. Ndafuna ndikudziwitseni kuti katundu amene munanditumizira anafika m’nthawi yake yofunikira. Tinagawa pa malo ochitira malonda otchedwa Mthandizi pamene anthu ambiri analandira Yesu kukhala Mbuye wao. Amen.
Pempho lathu ndilakuti chonde musakaike kutitumizira ma Baibulo, mabuku a Mesiya ndi nkhani zam’makalata kuti tigawire anthu, komanso ma T-shirt a mamembala a timu yathu.
Nthawi zonse timamupemphelera M’busa Alamo ndi utumiki wake pa nyengo zomwe mukudutsamo.
Ine wanu mwa Ambuye,
Evance Nauliya         
Limbe, Malawi

India
Okondeka abale ndi alongo mwa Khristu,
Moni woyera kwa inu. Lero talandira zolemba zanu zodabwitsa. Ndife okondwa chifukwa zithunzi zanga za ubatizo zinalinso mu nkhani zanu za m’makalata!

Ndi thandizo lanu la mapemphero, kuno tinachita misonkhano ya Uzimu pa 4, 5 ndi 6


footnotes:

1. Gen. 18:20-22, 19:1-25, Num. 22:21-35, 2 Sam. 24:10-16, 2 Mafumu 6:8-17, 2 Mbiri 20:1-29, 32:1-22, Masa. 34:7, 35:4-5, 68:17, Dan. 6:21-22, Zeka. 1:7-21, 2:1-5, chap. 4, Mat. 28:1-7, Mac. 5:17-24, 12:1-12, 21-23, Chiv. 7:1-2, chap. 8, 9:1-5, 13-21, 14:6-11, 15-20, 15:1, 5-8, chap. 16, 18:1-6, 21, 19:17-18, 20:1-3 return

2. Gen. 2:16-17, 3:1-19, Aro. 5:12-18, 1 Akor. 15:22, 47 return

3. Lev. 19:15, Deut. 1:17, 16:19, 1 Sam. 26:23, 1 Mafumu 8:32, 2 Mbiri 6:23, 19:7, Masa. 9:8, Miy. 24:23, 28:21, Yes. 45:21, Mac. 10:34, Aro. 2:11, Aef. 6:9, Akol. 3:25, Yakobo 2:1-10, 1 Pet. 1:17, Chiv. 15:3 return

4. Gen. 3:1-19, Ex. 23:20-21, Deut. 11:26-28, 28:61-63, 1 Sam. 12:14-15, 15:22-23, 2 Sam. chap. 11, 12:1-23, Job 36:7-12, Jer. 12:16-17, 18:9-10, Rom. 2:5-13, 6:12-16, Eph. 5:3-6, 2 Thes. 1:7-9, Heb. 2:1-4 return

5. Gen. 19:1-25, Num. 22:1-35, 25:1-9, 2 Sam. 24:1-17, 2 Mafumu 19:35, 1 Mbiri 21:9-30, 2 Mbiri 32:19-22, Rev. 7:1-2, chap. 8, 9:1-5, 13-21, 14:8-11, 15-20, chap. 16, 18:1-2, 21, 19:17-21, 20:1-3, 21:9 return

6. Gen. 9:5-6, Ex. 20:13, 21:12-15, 22-23, Lev. 24:17, Num. 35:16-21, 30-33, Deut. 5:17, 27:24-25, Masa. 139:13-16, Miy. 1:10-16, 6:16-18, Yer. 1:5, Mat. 19:18, Marko 10:19, Luka 18:20, Aro. 13:9, Agal. 5:19-21, 1 Tim. 1:9-10, Yakobo 2:11, 1 Yoh. 3:15, Chiv. 9:20-21, 21:8, 22:14-15 return

7. Gen. 19:1-13, 24-25, Lev. 18:22, 20:13, Deut. 22:5, 23:17, Owe. 19:22-25, Aro. 1:20-32, 1 Akor. 6:9-10, 1 Tim. 1:9-10, 2 Tim. 3:1-5, Yuda 7 return

8. Ex. 20:14, Lev. 18:20, 20:10, Deut. 5:18, 22-24, 1 Mafumu 14:24, 15:11-12, Miy. 6:29, 32-33, Yer. 5:8-9, Ezek. 18:10-13, 22:11, Mal. 3:5 Mat. 5:27-28, 15:19-20, 19:18, Marko 7:21-23, Luka 18:20, Aro. 13:9, 1 Akor. 6:9-10, Yakobo 2:10-12 return

9. 1 Akor. 5:9-11, 6:9-10, 13-18, 7:2, 10:7-8, 2 Akor. 12:21, Aef. 5:3, Akol. 3:5-6, 1 Ates. 4:3-5, Yuda 7, Chiv. 2:14, 20-22, 9:20-21 return

10. Deut. 21:20-21, Miy. 23:21, 29-35, 31:4-5, Yesa. 5:11, 22-23, 28:1-4, Nahamu 1:9-10, Luka 21:33-36, Aro. 13:12-14, 1 Akor. 5:10-12, 6:9-10, Agal. 5:19-23, 1 Ates. 5:6-8, 1 Tim. 3:8-9, Tito 1:7-9, 2:1-5, 1 Pet. 4:1-5, 2 Pet. 1:5-8 return

11. Mlal. 2:1-3, 7:2-6, Mat. 12:36, Aef. 5:3-4, 1 Tim. 2:9-10, 15, Tito 2:1-8, 12, 1 Pet. 1:13-16, 4:7, 5:8 return

12. Ex. 20:15, 22:1-4, Lev. 19:11, 13, Deut. 5:19, Zeka. 5:3, Mat. 15:19-20, 19:18, Marko 7:21-23, Luka 18:20, 19:45-46, Aro. 13:9, 1 Akor. 6:10, Aef. 4:28, Chiv. 9:21 return

13. Lev. 24:11-16, 23, Mat. 12:22-32, 15:19-20, Luka 12:9-10, Chiv. 13:1-9, 14:8-11, 17:1-9 return

14. Deut. 4:29, 6:5, 10:12, 11:13, 13:3-4, 26:16, 30:6, Yos. 22:5, Mat. 22:37-40 return

15. Ex. 18:21, 20:17, Deut. 5:21, Masa. 10:3, Mika 2:1-3, Marko 7:21-23, Aro. 1:28-32, 13:8-9, 1 Akor. 5:9-11, 6:9-10, Aef. 5:1-5, Akol. 3:5-6, 2 Tim. 3:1-5, 2 Pet. 2:1-3, 12-14, 1 Yoh. 2:15-17 return

16. Yesa. 66:3-4, 2 Ates. 2:3-12 return


prayer footnotes:

1. Masa. 51:5, Aro. 3:10-12, 23 return

2. Mat. 26:63-64, 27:54, Luka 1:30-33, Yoh. 9:35-37, Aro. 1:3-4      return

3. Mach. 4:12, 20:28, Aro. 3:25, 1 Yoh. 1:7, Chiv. 5:9      return

4. Masa. 16:9-10, Mat. 28:5-7, Marko 16:9, 12, 14, Yoh. 2:19, 21, 10:17-18, 11:25, Mach. 2:24, 3:15, Aro. 8:11, 1 Akor. 15:3-7      return

5. Luka 22:69, Mach. 2:25-36, Aheb. 10:12-13   return

6. 1 Akor. 3:16, Chiv. 3:20      return

7. Aef. 2:13-22, Aheb. 9:22, 13:12, 20-21, 1 Yoh. 1:7, Chiv. 1:5, 7:14      return

8. Mat. 26:28, Mach. 2:21, 4:12, Aef. 1:7, Akol. 1:14      return

9. Mat. 21:22, Yoh. 6:35, 37-40, Aro. 10:13      return

10. Aheb. 11:6     return

11. Aheb. 5:14, 8:11, Aro. 6:4, 1 Akor. 15:10, Chiv. 7:14, 22:14      return

12. Mat. 28:18-20, Yoh. 3:5, Mach. 2:38, 19:3-5   return

13. Deut. 4:29, 13:4, 26:16, Yoswa 1:8, 22:5, 2 Tim. 2:15, 3:14-17, Yakobo 1:22-25, Chiv. 3:18 return